Kudzikongoletsa ndi Phelele Lagolidi
KUYAMBIRA m’nthaŵi zakale, anthu akhala akuona majuwelo agolidi monga amtengo wapatali chifukwa cha mtengo wake ndi kukongola kwake. Atangokhala nduna yaikulu ya dziko la Igupto, Yosefe analandira unyolo wagolidi wapakhosi kuchokera kwa Farao. (Genesis 41:42) Rebeka anapatsidwa mphete yagolidi yapamphuno ndi zingwinjiri ziŵiri zagolidi za m’manja ake, za ndalama pafupifupi $1,400 (U.S.) malinga nkuŵerengera kwa masiku ano. (Genesis 24:22) Mosakayika konse, mphatso zamtengo wapatalizi anazilandira ndi chiyamiko ndipo anazivala mosangalala.
Baibulo limanena za ngale zophiphiritsira zimene zili zamtengo wapatali kwambiri kuposa zimene Yosefe ndi Rebeka anavala. Miyambo 25:12 ikufotokoza kuti: “Monga phelele lagolidi ndi chipini chagolidi woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.” Pamene phungu apereka uphungu wochokera m’Mawu a Mulungu osati malingaliro akeake, zoonadi iyeyo akupereka mphatso yamtengo wapatali. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kwenikweni uphungu umenewo ngwochokera kwa Yehova iye mwini. Baibulo likutiuza kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.” (Miyambo 3:11, 12) Ngati womvetsera avomereza modzichepetsa ndi kutsatira uphungu umenewo, zili monga ngati akudzikongoletsa ndi phelele lagolidi. Zilidi monga momwe mwambi wouziridwa wa m’Baibulo ukunenera kuti: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka.”—Miyambo 3:13, 14.