Khalani ndi Moyo Wopindulitsa
A TATE anali gone m’nyumba, akuvutika ndi kansa. Mwana wawo anali m’nyumba yomwe amapaliramo matabwa, akulongedza zida zopalira za atate akewo. Mmene anali kulongedza zidazo, ankaganiza za zinthu zochititsa kaso zimene atate ake anapanga ndi zidazo. Ngakhale kuti chipindacho chinali pafupi ndi nyumba yawo, iye anadziŵa kuti atate ake sadzaloŵamonso, sadzagwiritsanso ntchito zidazo zomwe anali kuzigwiritsira ntchito mwaluso. Nthaŵi yochitira zimenezo idapita.
Mwanayo anaganiza za lemba la Mlaliki 9:10: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” Lembali ankalidziŵadi bwino. Anakhala akuligwiritsira ntchito nthaŵi zambiri pophunzitsa ena choonadi cha Baibulo chakuti wakufa sangachite chilichonse. Tsopano mphamvu ya mawu a Solomo inamkhudza mtima—tisangalale ndi kuchita zinthu mmene tingathere pamene tili ndi moyo chifukwa idzafika nthaŵi imene sitidzathanso kusangalala.
Sangalalani ndi Moyo
M’buku lonse la Mlaliki, Mfumu yanzeru Solomo inalimbikitsa oŵerenga ake kusangalala ndi moyo. Mwachitsanzo, chaputala 3 chimati: “Ndidziŵa kuti [anthu] alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Mlaliki 3:12, 13.
Solomo anauziridwa ndi Mulungu kubwereza mawuŵa: “Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.”—Mlaliki 5:18.
Akulimbikitsanso achinyamata kuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe [kapena, mtsikana iwe]; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona.” (Mlaliki 11:9a) Nkwabwino chotani nanga kusangalala kotheratu ndi mphamvu ndi nyonga za unyamata!—Miyambo 20:29.
‘Ukumbukire Mlengi Wako’
Zoona, Solomo sakunena kuti nkwanzeru kuchita chilichonse chimene chingakope mtima kapena maso athu. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 2:16.) Zimenezi zikumveketsedwa bwino ndi mawu ake otsatira: “Koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi [zochita zimene zingakhutiritse zikhumbo zako].” (Mlaliki 11:9b) Tiyenera kukumbukira kuti, mosasamala kanthu za msinkhu wathu, Mulungu amapenya zochita zathu ndipo adzatiweruza moyenerera.
Nkupusatu kuganiza kuti tingamachite zomwe zimatisangalatsa, tikumati tidzadziperekabe kwa Mulungu mtsogolo! Moyo wathu ukhoza kutha nthaŵi iliyonse. Ngakhale ngati usathe, nkovuta kutumikira Mulungu munthu utakalamba. Pozindikira zimenezi, Solomo analemba kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”—Mlaliki 12:1.
Kukalamba kumakhala ndi mavuto ake. Mwamawu ophiphiritsira, Solomo analongosola zimene zimachitika muukalamba. Manja amanjenjemera, miyendo imafooka, ndipo mano amatha m’kamwa. Tsitsi limachita imvi ndi kumasosoka. Sutha kugona kwambiri kwakuti umadzutsidwa ndi kulira kwa mbalame. Mphamvu zathupi—kuona, kumva, kukhudza, kununkhiza, ndi kulaŵa—zonse zimafooka. Thupi lofookalo limabweretsa mantha akuti ukhoza kugwa, umaopanso “zoopsa” zina za m’njira. Potsirizira pake munthuyo amafa.—Mlaliki 12:2-7.
Zaka zaukalamba ndi zosautsa kwambiri makamaka kwa aja amene ‘sanakumbukire Mlengi wawo’ panthaŵi ya unyamata wawo. Chifukwa chowononga moyo wake, munthu wotereyo ‘sakondwera’ ndi zaka zamtsogolo. Kusakhala ndi moyo waumulungu kungawonjezerenso mavuto ndi zoŵaŵa m’zaka zaukalamba. (Miyambo 5:3-11) Pamene ayang’ana kutsogolo, anthu oterowo mwachisoni amangoona manda okha basi.
Kusangalala mu Ukalamba
Izi sizitanthauza kuti achikulire sangasangalale ndi moyo. M’Baibulo, “masiku ambiri, ndi zaka za moyo” zimagwirizanitsidwanso ndi dalitso la Mulungu. (Miyambo 3:1, 2) Yehova anauza bwenzi lake Abrahamu kuti: ‘Ndipo iwe . . . udzaikidwa ndi ukalamba wabwino.’ (Genesis 15:15) Mosasamala kanthu za zovuta za muukalamba, Abrahamu anapeza mtendere ndi bata muukalamba wake, nakhutira ndi moyo wake wonse wodzipatulira kwa Yehova. Ndi chikhulupiriro analinso kuyembekezera “mudzi wokhala nawo maziko,” Ufumu wa Mulungu. (Ahebri 11:10) Iye motero anamwalira ali “wokalamba ndi wokhutiritsidwa.”—Genesis 25:8, NW.
Motero Solomo analimbikitsa kuti: “Munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo.” (Mlaliki 11:8) Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, timakhala achimwemwe kwambiri ngati tikhala paunansi ndi Mulungu.
Pamene mnyamata uja analongedza chida cha atate ake chomalizira m’nyumba yopalira matabwa muja, analingalira za zimenezi. Analingalira za anthu onse amene anali kuwadziŵa amene anayesa kukhala ndi moyo wosangalala koma amene sanapeze chimwemwe chifukwa chakuti analibe unansi uliwonse ndi Mlengi wawo. Nkoyenera chotani nanga kuti atalimbikitsa anthu kusangalala ndi moyo wawo, Solomo mwachidule anati: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi!”—Mlaliki 12:13.