Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawaphunzira mosamalitsa makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Ngati ndi choncho, mudzasangalala kukumbukira zotsatirazi:
◻ Ndi mafunso ena ati omwe Akristu aŵiri ayenera kudzifunsa asanayambe kuganiza zochita pangano laukwati?
‘Kodi ndikudziŵadi bwino za mkhalidwe wauzimu wa mnzangayu ndi kudzipereka kwake kwa Mulungu? Kodi n’zoonekera kuti ndidzatumikira Mulungu ndi mnzangayo kwa moyo wonse? Kodi tadziŵana bwino zofooka zathu? Kodi ndili ndi chikhulupiriro chakuti tidzakhala ogwirizana nthaŵi zonse? Kodi aliyense wa ife akudziŵa bwino khalidwe la mnzake la m’mbuyomu ndi mmene zinthu zilili panopa?’—8/15, tsamba 31.
◻ Kodi Yesu anatanthauzanji pamene anauza om’tsatira ake kuti: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi”? (Mateyu 5:13)
Yesu anasonyeza kuti kulalikira kwa om’tsatirawo kwa ena ponena za Ufumu wa Mulungu kukakhala ndi mphamvu ya kuteteza, kapena kupulumutsa miyoyo, ya amene akaŵamvera. Ndithudi, awo amene anatsatira mawu a Yesu anatetezeka ku kuvunda kwakhalidwe ndi kwauzimu m’dziko.—8/15, tsamba 32.
◻ Kodi anthu otomerana angapeŵe bwanji msampha wa chisembwere?
Ngati muli paubwenzi wotomerana ndi wina, mungachite mwanzeru kupeŵa kukhala aŵiriŵiri panokha m’malo osayenera. Ndibwino zedi kusangalala ndi bwenzi lanulo pakati pa anzanu ena kapena m’malo apoyera. Ikani malire pa zochita zanu zosonyezana chikondi, aliyense polemekeza malingaliro ndi chikumbumtima cha mnzake.—9/1, tsamba 17, 18.
◻ Kodi kumvetsa n’chiyani?
Ndiko kukhoza kuona chimene nkhani ikutanthauza ndi kuzindikira nkhani yonseyo mwa kumvetsa kugwirizana kwa mbali zake zonse ndi mutu wa nkhaniyo, potero mukumamvetsa tanthauzo lake. (Miyambo 4:1)—9/15, tsamba 13.
◻ Kodi Yehova amafunanji kwa ife lerolino?
Kwenikweni chimene Yehova amafuna kwa ife ndicho kumvera Mwana Wake ndi kutsanzira chitsanzo chake ndi ziphunzitso zake. (Mateyu 16:24; 1 Petro 2:21)—9/15, tsamba 22.
◻ Kodi ndani okha amene angakhale ndi mtendere?
Popeza kuti Yehova ndi “Mulungu wa mtendere,” anthu amene amakonda Mulungu ndipo amalemekezadi mfundo zake zolungama za chikhalidwe ndi okhawo amene amakhala ndi mtendere. (Aroma 15:33)—10/1, tsamba 11.
◻ Kodi Yosefe anapeza bwanji mphamvu ya khalidwe labwino yomwe inam’theketsa kukana zofuna za mkazi wa Potifara tsiku ndi tsiku?
Yosefe anaona unansi wake ndi Yehova kukhala wamtengo wapatali kuposa zokondweretsa za kanthaŵi. Komanso, Yosefe anadziŵa bwino za mfundo za chikhalidwe, ngakhale kuti panthaŵiyo kunalibe mpambo wa malamulo a Mulungu. (Genesis 39:9)—10/1, tsamba 29.
◻ Kodi kufunitsitsa kwathu kukhululukira abale athu n’kofunika motani?
Kuti Mulungu apitirizebe kutikhululukira kwakukulukulu zimadalira pa kufunitsitsa kwathu kukhululukira ena. (Mateyu 6:12, 14; Luka 11:4)—10/15, tsamba 17.
◻ Kodi Mateyu 18:15-17 anali kunena za machimo a mtundu wanji, ndipo n’chiyani chomwe chimasonyeza zimenezo?
Machimo omwe Yesu ankatanthauza analidi aakulu omwe akanachititsa wolakwayo kuonedwa “monga wakunja ndi wamsonkho.” Ayuda sanali kuyanjana ndi Akunja, ndipo ankapeŵa okhometsa misonkho. Choncho Mateyu 18:15-17 amanena za machimo aakulu, osati kusemphana chabe maganizo kapena zopweteketsa mtima zomwe mungakhululuke ndi kuziiŵala mosavuta. (Mateyu 18:21, 22)—10/15, tsamba 19.
◻ Kodi kukonda Mawu a Mulungu moona kumaphatikizapo chiyani?
Kukonda Mawu a Mulungu kumatsogolera munthu kukhala mogwirizana ndi zofunikira zake. (Salmo 119:97, 101, 105) Zimenezi zimafuna kusintha mmene timaganizira ndi kakhalidwe kathu.—11/1, tsamba 14.
◻ Popeza kuti timalandira zochuluka kuchokera m’dzanja la Yehova, kodi tingabwezere chiyani kwa Mfumu ndi Wopereka wamkuluyo?
Baibulo limasonyeza kuti mphatso yabwino kwambiri yomwe tingapereke kwa Yehova ndiyo “nsembe yakuyamika.” (Ahebri 13:15) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti nsembe imeneyi n’njogwirizana mwachindunji ndi kupulumutsa moyo, komwe Yehova akufunitsitsa kuchita m’nthaŵi ino yamapeto. (Ezekieli 18:23)—11/1, tsamba 21.
◻ Kodi Solomo anatanthauzanji pamene analemba kuti: “Mawu a anzeru akunga zisonga”? (Mlaliki 12:11)
Mawu a anthu okhala ndi nzeru yaumulungu amasonkhezera oŵerenga kapena omvetsera kupita patsogolo mogwirizana ndi mawu anzeru omwe aŵerenga kapena kumva.—11/15, tsamba 21.
◻ Kodi kuzindikira kwaumulungu n’chiyani?
Ndiko kukhoza kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndiyeno n’kusankha njira yolondola. Kuphunzira ndi kuchita zomwe Mawu a Mulungu akunena kumapangitsa munthu kuzindikira.—11/15, tsamba 25.
◻ Kodi chofunika n’chiyani pamene tikufunitsitsa kulandira maudindo? (1 Timoteo 3:1)
Chofunika ndicho kulingalira bwino. Aliyense sayenera kutenga mautumiki ambirimbiri omwe angamutayire chimwemwe chake muutumiki wa Yehova. Mzimu wofunitsitsa n’ngwoyamikirika, koma kufunitsitsako kuyenera kusonyezedwa modekha ndi ‘modziletsa.’ (Tito 2:12; Chivumbulutso 3:15, 16)—12/1, tsamba 28.
◻ Kodi mavuto a kulera ana angathetsedwe motani?
Mulungu akulangiza makolo kukhala zitsanzo, anzawo, olankhulana nawo, ndi aphunzitsi awo. (Deuteronomo 6:6, 7)—12/1, tsamba 32.