Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mukukwaniritsa Udindo Wanu Wonse kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1999 | November 15
    • 12. M’mawu anu, mungalongosole motani zimene Solomo ananena zolembedwa pa Mlaliki 12:11, 12?

      12 Ngakhale kusanakhale njira zamakono zosindikizira mabuku, kunali mabuku ambiri m’tsiku la Solomo. Kodi mabuku amenewo anayenera kuonedwa motani? Iye anati: “Mawu a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mawu amene mbusa mmodzi awapatsa mawu awo akunga misomali yokhomedwa zolimba. Pamodzi ndi izi [“kupatulapo izi,” NW], mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.”​—Mlaliki 12:11, 12.

  • Kodi Mukukwaniritsa Udindo Wanu Wonse kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1999 | November 15
    • 14. (a) Kodi ndi “kuphunzira kwambiri” mabuku a mtundu wotani kumene kulibe phindu? (b) Kodi ndi mabuku ati amene tiyenera kuwakonda kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?

      14 Komano n’chifukwa chiyani Solomo ananena mawu amenewo ponena za mabuku? Eya, poyerekeza ndi Mawu a Yehova, mabuku osatha ambirimbiri a dziko lino ali ndi malingaliro wamba a anthu. Ambiri mwa malingaliro ameneŵa ndi malingaliro a Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4) Chotero, “kuphunzira kwambiri” mabuku akudziko oterowo kulibe phindu lenileni lokhalitsa. Kwenikweni, ambiri mwa iwo angakhale owononga mwauzimu. Mofanana ndi Solomo, tiyeni tisinkhesinkhe pa zimene Mawu a Mulungu amanena ponena za moyo. Zimenezi zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutiyandikizitsa kwa Yehova. Kukondetsa mabuku ena kapena malangizo ochokera kwina kungatitopetse. Mabuku amenewo amakhala oipa ndi owononga chikhulupiriro mwa Mulungu ndi zifuno zake makamaka ngati ali ndi malingaliro akudziko otsutsana ndi nzeru yaumulungu. Chotero, tiyeni tikumbukire kuti mabuku opindulitsa zedi m’tsiku la Solomo ndi lathu ndi aja amene amasonyeza nzeru ya “mbusa mmodzi,” Yehova Mulungu. Iye wapereka mabuku 66 a Malemba Opatulika, ndipo ndiwo mabuku amene tiyenera kuwakondetsetsa. Baibulo ndi zofalitsa zothandiza za “kapolo wokhulupirika” zimatithandiza kukhala ‘om’dziŵadi Mulungu.’​—Miyambo 2:1-6.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena