Chifukwa Chake Baibulo Liri Mphatso Youziridwa ya Mulungu
BAIBULO limanena kuti ‘Mulungu ndiye chikondi’ ndipo limasonyeza kuti nzeru ndi mphamvu zichokera kwa iye. (1 Yohane 4:8; Yobu 12:13; Yesaya 40:26) Limatiuza kuti ‘njira zake zonse ndi chiweruzo.’ (Deuteronomo 32:4) Malinga nkunena kwa Baibulo, Mulungu amasonyezanso mikhalidwe yonga chifundo ndi chisoni.—Eksodo 34:6; Aroma 9:15.
Chifukwa chakuti Baibulo limafotokoza Yehova Mulungu kukhala ndi mikhalidwe yotero, limatsogoza kwa iye anthu odzandira mwakhungu. Bukhu limeneli limanena za chilengedwe, chiyambi cha uchimo ndi imfa, ndi njira yoyanjanitsidwira kwa Mulungu. Limapereka chiyembekezo chochititsa chidwi cha Paradaiso wobwezeretsedwa padziko lapansi. Koma zonsezi zikhoza kukhala zaphindu kokha ngati Baibulo lingatsimikiziridwe kukhala mphatso youziridwa yochokera kwa Mulungu.
Baibulo ndi Sayansi
Baibulo lakhala lolakika nthaŵi zonse kwa olisuliza. Mwachitsanzo, pamene liŵerengedwa ndi maganizo omasuka, limapezedwa kukhala logwirizana ndi sayansi yowona. Ndithudi, Baibulo linalinganizidwa kukhala chitsogozo chauzimu, osati monga bukhu lophunzitsa sayansi. Koma tiyeni tiwone ngati Baibulo limavomerezana ndi zenizeni za sayansi.
Kapangidwe ka thupi: Baibulo limanena molondola kuti ‘ziŵalo zonse’ za mluza “zinalembedwa.” (Salmo 139:13-16) Ubongo, mtima, mapapo, maso—ndi ziŵalo zina zonse zathupi ‘nzolembedwa’ m’dongosolo la majini m’dzira lokhala ndi mphamvu ya moyo m’mimba mwa amayi. M’dongosolo lamajini limeneli mumakhala nthaŵi zolinganizidwa za kupangika kwa chimodzi ndi chimodzi cha ziŵalo zimenezi mwadongosolo loyenera. Ndipo tangolingalirani! Mfundo zimenezi za kupangika kwa thupi la munthu zinalembedwa m’Baibulo pafupifupi zaka 3,000 sayansi isanadziŵe za dongosolo lamajini.
Moyo wa nyama: Malinga nkunena kwa Baibulo, ‘kalulu, . . . amabzikula.’ (Levitiko 11:6) François Bourlière (The Natural History of Mammals, 1964, tsamba 41) amanena kuti: “Kachitidwe ka ‘kudyanso ndowe zake,’ kapena kupititsa chakudya m’matumbo kaŵiri mmalo mwa kamodzi, kakuwoneka kukhala kofala mwa akafumbwe ndi akalulu. Akafumbwe oŵeta kaŵirikaŵiri amadya ndi kumeza ndowe zawo za usiku popanda kutafuna, zimene m’maŵa zimachuluka mokwanira theka la chakudya chonse chomwe chimakhala m’mimba mwake. Koma kafumbwe wakutchire amadya ndoŵe zake kaŵiri patsiku, ndipo kalulu wa ku Yuropu amasimbidwa kuchita zofananazo.” Ponena za zimenezi, bukhu lakuti Mammals of the World (lolembedwa ndi E. P. Walker, 1964, Volyumu II, tsamba 647) limati: “Izi zingafanane ndi ‘kubzikula’ mwa nyama zogaŵanika chiboda.”
Kupenda za m’mabwinja: Mafumu a m’Baibulo, mizinda, ndi mitundu yadziŵidwa chifukwa chakutumbidwa kwa magome adongo, zoumba, zozokota, ndi zina zotero. Mwachitsanzo, anthu onga Ahiti otchulidwa m’Malemba anakhalakodi. (Eksodo 3:8) M’bukhu lake lakuti The Bible Comes Alive, Sir Charles Marston ananena kuti: “Awo amene adodometsa chikhulupiriro cha ambiri cha Baibulo, ndi kufooketsa ukumu wake, nawonso akufooketsedwa ndi umboni umene wapezedwa, ndipo ukumu wawo wagwetsedwa. Zofukulidwa m’mabwinja zikuchotsa kusuliza kowononga pa zenizeni zokaikiridwa ndi kusonyeza nthanthi kukhaladi nthanthi yeniyeni.”
Kupenda za m’mabwinja kwachirikiza Baibulo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, zotumbidwa zatsimikizira malo ndi maina opezeka m’Genesis mutu 10. Ofukula m’mabwinja atumba mzinda wa Uri wa Akaldayo, malo apakati a malonda ndi kupembedza kumene Abrahamu anabadwira. (Genesis 11:27-31) Kumtunda kwa kasupe wa Gihoni m’chigawo cha kum’mwera koma chakum’maŵa kwa Yerusalemu, ofukula m’mabwinja anapeza mzinda wa Ajebusi wolandidwa ndi Mfumu Davide. (2 Samueli 5:4-10) Cholembedwa cha Siloamu chozokotedwa kumapeto kwa mchera womangidwa ndi Mfumu Hezekiya chinatumbidwa mu 1880. (2 Mafumu 20:20) Kugwa kwa Babulo ku dzanja la Koresi Wamkulu mu 539 B.C.E. kumasimbidwa m’Mbiri ya Nabonidus, yofukulidwa m’zaka za zana la 19 C.E. Zofotokozedwa m’bukhu la Estere zatsimikiziridwa ndi zolembedwa zozokotedwa za ku Persepolis ndi kutumbidwa kwa nyumba yachifumu ya Mfumu Xerxes (Ahaswero) ku Susani, kapena Susa, pakati pa 1880 ndi 1890 C.E. Chozokota chopezedwa mu 1961 m’mabwinja a bwalo lamaseŵera la Roma ku Kaisareya chinatsimikizira kukhalako kwa kazembe Wachiroma Pontiyo Pilato, amene anapereka Yesu kuti apachikidwe.—Mateyu 27:11-26.
Kupenda zakuthambo: Pafupifupi zaka 2,700 zapitazo—anthu adakali kutali kwambiri ndi kudziŵa kuti dziko nlozungulira—mneneri Yesaya analemba kuti: “Alipo Iye amene akhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira.” (Yesaya 40:22, NW) Liwu Lachihebri lakuti chugh lotembenuzidwa “lozungulira” panopa lingamasulidwenso monga “mbulunga.” (A Concordance of the Hebrew and Chaldee Scriptures, lolembedwa ndi B. Davidson) Ndiyenonso, ‘kuzungulira’ kwa dziko lapansi kumawoneka bwino lomwe mutakhala kunja kwa thambo ladziko lapansi ndipo nthaŵi zina ngati muli m’ndege youlukira pamwamba kwambiri. Mwamwaŵi wanji, Yobu 26:7 amanena kuti Mulungu ‘alenjeka dziko pachabe.’ Izitu nzowona, popeza kuti openda zakuthambo amadziŵa kuti dziko lapansi liribe cholichirikiza chowoneka.
Zomera: Ena amalingalira molakwa kuti Baibulo nlosalondola chifukwa chakuti Yesu Kristu ananena kuti ‘mbewu ya mpiru . . . ichepa ndi mbewu zonse za padziko.’ (Marko 4:30-32) Mwachiwonekere, Yesu anatanthauza mbewu ya mpiru wotchedwa black mustard (Brassica nigra kapena Sinapis nigra), imene iri ndi ukulu wa mamilimita kuchokera pa 1 kufika 1.6. Ngakhale kuti ziripo mbewu zocheperapo, monga ngati mbewu za orchid zochepa ngati ufa wa tirigu, Yesu sankalankhula kwa anthu olima mbewu za orchid. Ayuda a ku Galileya amenewo anadziŵa kuti pambewu zonse zosiyanasiyana zowokedwa ndi alimi akumaloko, mbewu ya mpiru ndiyo inali yaing’ono kwambiri. Yesu anali kulankhula za Ufumu, osati kuphunzitsa zomera.
Kupenda miyala: Ponena za cholembedwa cha Baibulo cha chilengedwe, katswiri wotchuka wopenda miyala Wallace Pratt anati: “Ngati ine monga wopenda miyala ndinapemphedwa kufotokoza mwachidule malingaliro athu amakono ponena za chiyambi cha dziko lapansi ndi kuyambika kwa moyo wopezekapo, kwa anthu akumidzi osaphunzira, onga ngati mafuko aja kwa amene Bukhu la Genesis linalembedwako, sindingatero bwino lomwe popanda kulondola mosamalitsa chinenero cha m’mutu woyamba wa Genesis.” Pratt anawona kuti dongosolo la zochitika mu Genesis—chiyambi cha nyanja, kutundumuka kwa nthaka, ndiyeno kukhalapo kwa miyoyo ya m’madzi, mbalame, ndi nyama zakumtunda—kulidi kutsatizana kwa nyengo zanthaŵi kopezedwa mwakupenda miyala.
Mankhwala: M’bukhu lake lakuti The Physician Examines the Bible, C. Raimer Smith analemba kuti: “Zimandidabwitsa kwambiri kuti Baibulo nlolondola kwambiri ponena za mankhwala. . . . Pamene linena za kuchiritsa, monga zithupsa, zilonda, ndi zina zotero, limakhala lolondola ngakhale m’miyezo yamakono. . . . Anthu ambiri amakhulupirirabe malaulo monga akuti, kuika kamtsitsi kenakake m’thumba kumaletsa kuchita dzanzi; kuti kugwira achule kumapatsa njereŵere; kuti kuvala kachingwe kofiira m’khosi kumapoletsa zilonda zapakhosi; kuti kuvala chithumwa kumachinjiriza matenda; kuti nthaŵi zonse mwana akadwala ali ndi njoka zam’mimba; ndi zina zotero, koma mawu oterowo samapezeka m’Baibulo. Imeneyi ndimfundo yaikulu kwa ine ndipo iri umboni wina wosonyeza kuti linachokeradi kwa Mulungu.”
Lodalirika m’Kupereka Tsatanetsatane wa Mbiri Yakale
M’bukhu lake lakuti A Lawyer Examines the Bible, loya wamkulu wa boma Irwin H. Linton ananena kuti: “Pamene kuli kwakuti nkhani zolembedwa, nthano zoperekedwa ndiponso umboni wonama zimakhala zaluso kugwirizanitsa zochitika zosimbidwazo ndi malo akutali ndi nthaŵi zosadziŵika, mwakutero kuswa malamulo oyambirira amene ife maloya timaphunzira akutsatira bwino mlandu, akuti ‘mlandu uyenera kutchula nthaŵi ndi malo,’ nkhani za Baibulo zimatchula molondola bwino lomwe deti ndi malo a zinthu zonenedwazo.”
Kutsimikizira mfundo imeneyi, Linton anasonyeza Luke 3:1, 2. Pamenepo wolemba Uthenga Wabwinoyo anatchula nduna zisanu ndi ziŵiri kuti asonyeze nthaŵi pamene Yesu Kristu anayamba uminisitala Wake. Wonani tsatanetsatane amene Luka anapereka m’mawu aŵa: ‘Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo chiwanga cha Abilene; pa ukulu wansembe wawo wa Anasi ndi Kayafa, panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu.’
Baibulo nlodzala ndi tsatanetsatane wotero. Ndiponso, mbali zoterozo zonga Uthenga Wabwino zinalembedwa m’nyengo ya kutsungula kwa Ayuda, Agiriki ndi Aroma. Inali nthaŵi ya maloya, olemba nkhani, oyendetsa ntchito, ndi ena otero. Ndithudi, ngati tsatanetsatane wopezeka mu Mauthenga Abwino ndi mbali zina za Baibulo sizenizeni, zikanavumbulidwa kale kukhala zolakwa. Koma olemba mbiri akudziko anatsimikizira mfundo zonga kukhalako kwa Yesu Kristu. Mwachitsanzo, ponena za Yesu ndi otsatira Ake, wolemba mbiri Wachiroma Tacitus analemba kuti: “Kristu, komwe dzinalo [Akristu] linachokera, anapatsidwa chilango choipitsitsa m’kulamulira kwa Tiberiyo ndi mmodzi wa olamulira wathu, Pontiyo Pilato.” (Annals, Bukhu XV, 44) Kulondola kwa mbiri ya Baibulo kumathandiza kutsimikizira kuti ndilo mphatso ya Mulungu kwa anthu.
Umboni Waukulu Koposa
Ngakhale kuti kupenda za m’mabwinja, zakuthambo, mbiri yakale, ndi mbali zina za chidziŵitso zimachirikiza Baibulo, kulikhulupirira sikumadalira pa kutsimikizira koteroko. Pakati pa maumboni ambiri osonyeza kuti Baibulo ndimphatso youziridwa ya Mulungu kwa ife, palibe umboni umene ungaperekedwe woposa kukwaniritsidwa kwa maulosi ake.
Yehova Mulungu ndiye Magwero a ulosi wowona. Kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: ‘Zinthu zakale zawoneka, ndipo zatsopano ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.’ (Yesaya 42:9) Ndiponso, Baibulo limanena kuti olemba ake anauziridwa ndi Mulungu mwa mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. Mwachitsanzo, mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Mtumwi Petro analemba kuti: ‘Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera, analankhula.’ (2 Petro 1:20, 21) Chotero tiyeni tiupende ulosi wa Baibulo.
Pakati pa mazana a maulosi a m’Baibulo pali onena za likulu la Asuri, Nineve, “mudzi wa mwazi” umene unachititsa mantha Middle East wakale kwa zaka zoposa mazana 15. (Nahumu 3:1) Komabe, pachimake pa ulamuliro wa Nineve, Baibulo linanenera kuti: ‘[Mulungu] adzasanduliza Nineve akhale bwinja, wouma ngati chipululu. Ndipo zoŵeta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse zamitundumitundu; ndi vuo ndi nungu zidzakhala m’mitu ya nsanamira zake; adzaimba mawu awo m’mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.’ (Zefaniya 2:13, 14) Lerolino, alendo amangowona chitunda chokha monga chizindikiro cha bwinja la Nineve wakale. Ndiponso, magulu a nkhosa amabudula kumeneko, monga kunanenedweratu.
M’masomphenya, Danieli mneneri wa Mulungu anawona nkhosa yamphongo yanyanga ziŵiri ndi tonde wokhala ndi nyanga yaikulu pakati pa maso ake. Tondeyo anakantha nkhosa yamphongoyo, nathyola nyanga zake ziŵirizo. Pambuyo pake, nyanga yaikulu ya tondeyo inathyoka, ndipo panaphuka nyanga zinayi m’malo ake. (Danieli 8:1-8) Mngelo Gabrieli anafotokoza kuti: ‘Nkhosa yamphongo waiwona ya nyanga ziŵiri ndizo mafumu a Mediya ndi Peresiya. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene, ndi nyanga yaikulu iri pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. Ndikuti zinaphuka zinayi m’malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka mafumu anayi ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.’ (Danieli 8:20-22) Monga momwe mbiri yasonyezera, nkhosa yamphongo yanyanga ziŵiri—Ufumu wa Amedi ndi Aperesi—unagwetsedwa ndi “mfumu ya Helene [Girisi].” Tonde wophiphiritsira ameneyo anali ndi “nyanga yaikulu” yoimira Alexander Wamkulu. Pambuyo pa imfa yake, akazembe ake anayi anatenga malo a “nyanga yaikulu” imeneyo mwakudzikhazikitsa okha kukhala ‘mafumu anayi.’
Maulosi ambirimbiri m’Malemba Achihebri (“Chipangano Chakale”) akwaniritsidwa mwa Yesu Kristu. Ena a ameneŵa analembedwa ponena za iye ndi olemba ouziridwa ndi Mulungu amene analemba Malemba Achikristu Achigiriki (“Chipangano Chatsopano”). Mwachitsanzo, wolemba Uthenga Wabwino Mateyu anatchula kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Malemba onena za kubadwa kwa Yesu mwa namwali, kuti adzakhala ndi kalambula bwalo Wake, ndi kuloŵa Kwake mu Yerusalemu pa mwana wa bulu. (Yerekezerani Mateyu 1:18-23; 3:1-3; 21:1-9 ndi Yesaya 7:14; 40:3; Zekariya 9:9.) Kukwaniritsidwa kwa maulosi koteroko kumathandiza kutsimikizira kuti Baibulo liridi mphatso ya Mulungu youziridwa.
Kukwaniritsidwa kwatsopano kwa maulosi a Baibulo kumatsimikizira kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Nkhondo, kupereŵera kwa chakudya, miliri, ndi zivomezi pamlingo umene sizinachitikepo ziri mbali ya ‘chizindikiro’ cha ‘kukhalapo’ kwa Yesu m’mphamvu yake ya Ufumu. Chizindikirocho chimaphatikizaponso ntchito yadziko lonse ya Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni anayi, zimene zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwawo. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:10, 11) Maulosi a Baibulo amene akukwaniritsidwa tsopano akutitsimikiziranso kuti boma la Mulungu lakumwamba pansi pa Yesu Kristu posachedwapa lidzabweretsa dziko latsopano la chimwemwe chamuyaya kwa anthu omvera.—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1-5.
Tchati chosonyezedwacho chokhala ndi mutu wakuti “Kukwaniritsidwa kwa Maulosi a Baibulo” chimasonyeza ochepa okha a mazana a maulosi a Baibulo. Kukwaniritsidwa kwa ena a maulosi ameneŵa kunasonyezedwa m’Malemba, koma makamaka tiyenera kuzindikira maulosi amene akukwaniritsidwa tsopano.
Mwachiwonekere, mukhoza kuwona zochitika zina zapadziko lonse zonenedweratu m’Baibulo. Koma bwanji osasanthula zowonjezereka? Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukupatsani zowonjezereka mutazipempha. Ndipotu kufunafuna kwanu chidziŵitso cha Wam’mwambamwamba ndi zifuno zake kukukhutiritseni kuti Baibulo liridi mphatso youziridwa ya Mulungu.
[Tchati patsamba 7]
KUKWANIRITSIDWA KWA
MAULOSI A BAIBULO ULOSI KUKWANIRITSIDWA KWAKE
Genesis 49:10 Yuda anakhala mtundu wachifumu wa
Israyeli (1 Mbiri 5:2; Ahebri 7:14)
Zefaniya 2:13, 14 Kuwonongedwa kwa Nineve pafupifupi mu 632 B.C.E.
Yeremiya 25:1-11; Yesaya 39:6Kugonjetsedwa kwa Yerusalemu kuyambitsa
bwinja la zaka 70 (2 Mbiri 36:17-21; Yeremiya 39:1-9)
Yesaya 13:1, 17-22; Koresi agonjetsa Babulo; Ayuda abwerera kwawo
Danieli 8:3-8, 20-22 Amedi ndi Aperesi agonjetsedwa ndi Alexander
Wamkulu ndi kugaŵika kwa Ufumu wa Girisi
Yesaya 7:14; Yesu abadwa kwa namwali mu Betelehemu
Danieli 9:24-26 Kudzozedwa kwa Yesu monga Mesiya (29 C.E.)
Yesaya 9:1, 2 Kuyamba kwa uminisitala wa Yesu wotsegula maso
mu Galileya (Mateyu 4:12-23)
Yesaya 53:4, 5, 12 Imfa ya Kristu monga nsembe ya dipo
Salmo 22:18 Kuchitira maere malaya a Yesu
Salmo 16:10; Kuuka kwa Kristu patsiku lachitatu
Luka 19:41-44; 21:20-24 Kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi Aroma
(70 C.E.)
Luka 21:10, 11; Nkhondo, njala, zivomezi, miliri, kusayeruzika,
Mateyu 24:3-13; zosayerekezereka, ndi zina zotero,
2 Timoteo 3:1-5 zosonyeza “masiku otsizira”
Mateyu 24:14; Kulalikira kwa padziko lonse kwa Mboni
Yesaya 43:10; za Yehova kwakuti Ufumu wa Mulungu wakhazikitsidwa
Salmo 2:1-9 ndipo posachedwapa udzagonjetsa otsutsa onse
Mateyu 24:21-34; Banja la mitundu yonse la Mboni za Yehova
Chivumbulutso 7:9-17 likulambira Mulungu ndi kukonzekera kupulumuka
‘chisautso chachikulu’
[Chithunzi patsamba 8]
Nkhondo, njala, miliri, ndi zivomezi zikusakaza kwambiri lerolino, koma dziko latsopano la mtendere ndi chimwemwe layandikira