Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/15 tsamba 10-15
  • Kutumikira Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutumikira Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mulungu Wako Ndi Mfumu”
  • Mthenga wa Mtendere Wamkulu Koposa wa Yehova
  • Ophunzitsidwa Kuyenda m’Mapazi a Kristu
  • A Mtendere m’Dziko Lodzala ndi Chipolowe
  • Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mmene Mungakumanire ndi Mtendere wa Umulungu Mokwanira Kwambiri?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/15 tsamba 10-15

Kutumikira Monga Amithenga a Mtendere Waumulungu

“Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye . . . amene abukitsa mtendere.”​—YESAYA 52:7.

1, 2. (a) Monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 52:7, kodi ndi uthenga wabwino uti umene ukufunika kuulengeza? (b) Kodi mawu aulosi a Yesaya anatanthauzanji kwa Israyeli wakale?

PALI uthenga wabwino wofunika kuulengeza! Uli uthenga wa mtendere​—mtendere weniweni. Uli uthenga wa chipulumutso wonena za Ufumu wa Mulungu. Kalekale mneneri Yesaya analemba za uwo, ndipo mawu ake anasungidwa kaamba ka ife pa Yesaya 52:7, pamene timaŵerenga kuti: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.”

2 Yehova anauzira mneneri wake Yesaya kulemba uthengawo kuti upindulitse Israyeli wakale ndi kupindulitsanso ife lerolino. Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Panthaŵi imene Yesaya analemba mawu ameneŵa, ufumu wakumpoto wa Israyeli unali utatengeredwa kale kuukapolo ndi Asuri. Pambuyo pake, nzika za ufumu wakummwera wa Yuda zinali kudzatengeredwa kundende ku Babulo. Amenewo anali masiku a nsautso ndi chipolowe pakati pa mtunduwo chifukwa anthu ake sanamvere Yehova ndipo sanali pamtendere ndi Mulungu. Monga momwe Yehova anali atawauzira, mkhalidwe wawo wochimwa unali kuchititsa magaŵano pakati pa iwo ndi Mulungu wawo. (Yesaya 42:24; 59:2-4) Komabe, kupyolera mwa Yesaya, Yehova ananeneratu kuti panthaŵi yake zipata za Babulo zinali kudzatseguka. Anthu a Mulungu anali kudzamasuka kubwerera kwawo, kumeneko kukamanganso kachisi wa Yehova. Ziyoni adzabwezeretsedwa ndipo kulambira Mulungu woona kudzapitirizanso mu Yerusalemu.​—Yesaya 44:28; 52:1, 2.

3. Kodi lonjezo la kubwezeretsedwa kwa Israyeli linalinso motani ulosi wa mtendere?

3 Lonjezo limeneli la chilanditso linalinso lonjezo la mtendere. Kubwezedwa ku dziko limene Yehova anapatsa Aisrayeli kunali kudzakhala umboni wa chifundo cha Mulungu ndi kulapa kwawo. Kunali kudzasonyeza kuti anali pamtendere ndi Mulungu.​—Yesaya 14:1; 48:17, 18.

“Mulungu Wako Ndi Mfumu”

4. (a) Kodi kunanenedwa m’lingaliro lotani mu 537 B.C.E. kuti ‘Yehova wakhala mfumu’? (b) Kodi Yehova anayendetsa motani zinthu kuti apindulitse anthu ake m’zaka zotsatira?

4 Pamene Yehova anapereka chilanditso chimenechi mu 537 B.C.E., chilengezo chomvekera bwino chinaperekedwa ku Ziyoni chakuti: “Mulungu wako ndi mfumu.” Zoona, Yehova ndiye ‘Mfumu yanthaŵi zosatha.’ (Chivumbulutso 15:3) Koma chilanditso chimenechi cha anthu ake chinali chisonyezero china cha uchifumu wake. M’njira yapadera, chinasonyeza kupambana kwa mphamvu yake ndi ulamuliro wake pa ufumu wamphamvu waumunthu uliwonse umene unakhalapo kufikira panthaŵiyo (Yeremiya 51:56, 57) Chifukwa cha kugwira ntchito kwa mzimu wa Yehova, ziŵembu zina zolinganizidwira anthu ake zinalephera. (Estere 9:24, 25) Nthaŵi ndi nthaŵi, Yehova analoŵerera m’njira zosiyanasiyana kuti achititse mafumu a Amedi ndi Aperisi kugwirizana ndi kuchita chifuniro cha ufumu wake. (Zekariya 4:6) Zochitika zozizwitsa za m’masikuwo zalembedwa kaamba ka ife m’mabuku a Baibulo a Ezara, Nehemiya, Estere, Hagai, ndi Zekariya. Ndipo nzolimbikitsa chikhulupiriro chotani nanga pamene tizipenda!

5. Kodi pa Yesaya 52:13–53:12 patchulidwa zochitika zapadera zotani?

5 Komabe, zimene zinachitika mu 537 B.C.E. ndi pambuyo pake zinali chiyambi chabe. Mwamsanga pambuyo pa ulosi wa kubwezeretsedwa m’chaputala 52, Yesaya analemba za kufika kwa Mesiya. (Yesaya 52:13–53:12) Mwa Mesiya, amene anadzakhala Yesu Kristu, Yehova anapereka uthenga wa chilanditso ndi mtendere wofunika kwambiri kuposa ndi zimene zinachitika mu 537 B.C.E.

Mthenga wa Mtendere Wamkulu Koposa wa Yehova

6. Kodi mthenga wa mtendere wamkulu koposa wa Yehova ndani, ndipo ndi ntchito yotani imene anati adzaichita?

6 Yesu Kristu ali mthenga wa mtendere wamkulu koposa wa Yehova. Iye ali Mawu a Mulungu, Wolankhulira wake wa Yehova. (Yohane 1:14) Mogwirizana ndi zimenezi, panthaŵi ina pambuyo pa kubatizidwa kwake mu Mtsinje wa Yordano, Yesu anaimirira m’sunagoge ku Nazarete ndi kuŵerenga za ntchito yake mofuula pa Yesaya chaputala 61. Ntchitoyo inasonyeza bwino lomwe kuti zimene anamtuma kudzalalikira zinaphatikizapo “mamasulidwe” ndi “kuchiritsa,” (NW) limodzinso ndi mwaŵi wa kupeza chiyanjo cha Yehova. Komabe, Yesu sanangolengeza uthenga wa mtendere. Mulungu anamtumizanso kudzapereka maziko a mtendere wokhalitsa.​—Luka 4:16-21.

7. Kodi kukhala pamtendere ndi Mulungu kumene kuli kotheka kudzera mwa Yesu Kristu kuli ndi zotulukapo zotani?

7 Panthaŵi ya kubadwa kwa Yesu, angelo anaonekera kwa abusa pafupi ndi Betelehemu, akumatamanda Mulungu ndi kunena: ‘Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.’ (Luka 2:8, 13, 14) Inde, panali kudzakhala mtendere kwa awo amene Mulungu anakondwera nawo chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro pa zogaŵira zimene anali kupanga mwa Mwana wake. Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Zinatanthauza kuti ngakhale kuti anthu amabadwa mu uchimo, iwo akhoza kupeza kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu, unansi woyanjidwa ndi iye. (Aroma 5:1) Akhoza kupeza bata la mumtima, mtendere, zimene zili zosatheka mwa njira ina iliyonse. Panthaŵi yoikika ya Mulungu, padzakhala chimasuko ku ziyambukiro zonse za choloŵa cha uchimo wa Adamu​—kuphatikizapo matenda, ndi imfa. Anthu sadzakhalanso akhungu kapena ogontha kapena opunduka. Kufooka kothetsa nzeru ndi matenda opsinja mtima a m’maganizo adzachotsedwapo kwamuyaya. Kudzakhala kotheka kusangalala ndi moyo mu ungwiro wosatha.​—Yesaya 33:24; Mateyu 9:35; Yohane 3:16.

8. Kodi mtendere waumulungu ukupatsidwa kwa yani?

8 Kodi mtendere waumulungu ukupatsidwa kwa yani? Ukupatsidwa kwa awo onse amene akusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. Mtumwi Paulo analemba kuti ‘Kunamkomera Mulungu kuti mwa Kristu ayanjanitse zinthu zonse kwa iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi umene Yesu anakhetsa pa [mtengo wozunzirapo, NW].’ Mtumwiyo anawonjezera kuti kuyanjanitsa kumeneku kudzaphatikizapo “za kumwamba”​—ndiko kuti, awo amene adzakhala oloŵa nyumba pamodzi ndi Kristu kumwamba. Kudzaphatikizaponso “za padziko”​—ndiko kuti, awo amene adzapatsidwa mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha pano padziko lapansi pamene lidzakhala Paradaiso weniweni. (Akolose 1:19, 20) Chifukwa cha kugwiritsira ntchito kwawo mtengo wa nsembe ya Yesu ndi chifukwa cha kumvera kwawo Mulungu ndi mtima wonse, onseŵa adzasangalala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu.​—Yerekezerani ndi Yakobo 2:22, 23.

9. (a) Kodi mtendere ndi Mulungu umasonkhezeranso maunansi ena ati? (b) Pofuna kubweretsa mtendere wokhalitsa kulikonse, kodi Yehova anampatsa mphamvu yotani Mwana wake?

9 Nkofunika chotani nanga kukhala pamtendere wotero ndi Mulungu! Ngati palibe mtendere ndi Mulungu, sipangakhalenso mtendere wokhalitsa kapena weniweni mu unansi wina uliwonse. Mtendere ndi Yehova ndiwo maziko a mtendere weniweni padziko lapansi. (Yesaya 57:19-21) Moyenerera, Yesu Kristu ali Kalonga wa Mtendere. (Yesaya 9:6) Kwa ameneyu, mwa amene anthu onse adzayanjanitsidwa kwa Mulungu, Yehova waperekanso mphamvu yolamulira. (Danieli 7:13, 14) Ndipo ponena za zotulukapo za kulamulira anthu kwa Yesu monga kalonga, Yehova akulonjeza kuti: “Za mtendere sizidzatha.”​—Yesaya 9:7; Salmo 72:7.

10. Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo cha kufalitsa uthenga wa Mulungu wa mtendere?

10 Uthenga wa mtendere wa Mulungu uli wofunikira kwa anthu onse. Yesu iye mwini anapereka chitsanzo cha changu poulalikira. Anachita motero m’bwalo la kachisi mu Yerusalemu, m’munsi mwa phiri, m’mbali mwa mseŵu, kwa mkazi wachisamariya pachitsime, ndi m’nyumba za anthu. Kulikonse kumene kunali anthu, Yesu anapeza mipata ya kulalikira za mtendere ndi Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 4:18, 19; 5:1, 2; 9:9; 26:55; Marko 6:34; Luka 19:1-10; Yohane 4:5-26.

Ophunzitsidwa Kuyenda m’Mapazi a Kristu

11. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuchita ntchito yotani?

11 Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kulalikira uthenga wa Mulungu wa mtendere. Monga momwe Yesu analiri “mboni yokhulupirika ndi yoona” ya Yehova, anazindikira kuti iwonso anali ndi thayo la kuchitira umboni. (Chivumbulutso. 3:14; Yesaya 43:10-12) Anayang’ana kwa Kristu monga Mtsogoleri wawo.

12. Kodi Paulo anasonyeza motani kufunika kwa ntchito yolalikira?

12 Mtumwi Paulo anasonyeza kufunika kwa ntchito yolalikira, nati: “Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira iye, sadzachita manyazi.” Ndiko kuti, palibe amene amaika chikhulupiriro mwa Yesu Kristu monga Mkulu wa chipulumutso wa Yehova amene adzagwiritsidwa mwala. Ndipo palibe aliyense amene adzakanidwa chifukwa cha mtundu wake, chifukwa Paulo anawonjezera kuti: “Kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa iye; pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.” (Aroma 10:11-13) Koma kodi anthu adzadziŵa motani za mwaŵi umenewo?

13. Kodi panafunikira chiyani kuti anthu amve uthenga wabwino, ndipo Akristu a m’zaka za zana loyamba anachita motani pa chofunika chimenecho?

13 Paulo anapereka yankho pa chofunika chimenecho mwa kufunsa mafunso omwe mtumiki aliyense wa Yehova amachita bwino kuwalingalira. Mtumwiyo anafunsa kuti: “Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa?” (Aroma 10:14, 15) Mbiri ya Chikristu choyambirira ili ndi umboni woonekera bwino wakuti amuna ndi akazi, ana ndi okalamba, anatsatira chitsanzo choperekedwa ndi Kristu ndi atumwi ake. Iwo anakhala alengezi okangalika a uthenga wabwino. Motsanzira Yesu, iwo analalikira kwa anthu kulikonse kumene anawapeza. Ndi chikhumbo chosafuna kuphonya aliyense, anapitiriza ndi utumiki wawo m’makwalala ndi kunyumba ndi nyumba.​—Machitidwe 17:17: 20:20.

14. Kodi zinakhala zoona motani kuti “mapazi” a olengeza uthenga wabwino anali “okometsetsa”?

14 Ndithudi, si aliyense amene analandira alaliki achikristu mokoma mtima. Komabe, mawu omwe Paulo anagwira pa Yesaya 52:7 anakhaladi oona. Atafunsa funso lakuti, ‘Adzalalikira bwanji, ngati satumidwa?’ iye anawonjezera kuti: “Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Ambiri a ife sitimalingalira za mapazi athu kukhala okometsetsa, kapena okongola. Motero, kodi zimenezi zikutanthauzanji? Kaŵirikaŵiri, mapazi ndiwo amayendetsa munthu pokalalikira kwa ena. Mapazi oterowo amaimiradi munthuyo. Ndipo tingakhale otsimikiza kuti kwa ambiri omwe anamva uthenga wabwino kwa atumwi ndi kwa ophunzira ena a Yesu Kristu a m’zaka za zana loyamba, Akristu oyambirira ameneŵa analidi okongola pamaso pawo. (Machitidwe 16:13-15) Koma chofunika koposa, iwo anali amtengo wapatali pamaso pa Mulungu.

15, 16. (a) Kodi Akristu oyambirira anasonyeza motani kuti analidi amithenga a mtendere? (b) Kodi nchiyani chingatithandize kuchita utumiki wathu mofanana ndi mmene Akristu a m’zaka za zana loyamba anachitira?

15 Otsatira a Yesu anali ndi uthenga wa mtendere, ndipo anaupereka mwamtendere. Yesu anapatsa ophunzira ake malangizo awa: “Ndipo m’nyumba iliyonse mukaloŵamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. Ndipo mukakhala mwana wa mtendere mmenemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.” (Luka 10:5, 6) Liwu lakuti Sha·lohmʹ, kapena “mtendere,” ndi moni wamwambo wachiyuda. Komabe, malangizo a Yesu anaphatikizapo zoposa zimenezi. Monga “atumiki m’malo mwa Kristu,” ophunzira ake odzozedwa analimbikitsa anthu kuti: “Yanjanitsidwani ndi Mulungu.” (2 Akorinto 5:20) Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, iwo analankhula kwa anthu za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzawachitira aliyense payekha. Awo amene anamvetsera analandira dalitso; awo amene anakana uthengawo anataya mwaŵi.

16 Mboni za Yehova zikuchita utumiki wawo m’njira imodzimodziyo lerolino. Uthenga wabwino umene zimaperekera anthu suli wawo ayi; uli wa Uyo amene anawatuma. Ntchito yawo ndiyo ya kuupereka. Ngati anthu aulandira, amaloŵa pamzera wokalandira madalitso odabwitsa. Ngati akana, amakana kukhala pamtendere ndi Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu.​—Luka 10:16.

A Mtendere m’Dziko Lodzala ndi Chipolowe

17. Ngakhale pamene tayang’anizana ndi anthu onyoza, kodi tiyenera kukhala ndi khalidwe lotani, ndipo chifukwa ninji?

17 Mulimonse mmene anthu angayankhire, nkofunika kwa atumiki a Yehova kukumbukira kuti ali amithenga a mtendere waumulungu. Anthu a dziko amaloŵa m’mikangano yaukali ndi kulankhula mokwiya mwa kunena mawu opweteka kapena mwa kutukwana amene awaputa. Mwinamwake ena a ife tinachita zimenezo m’nthaŵi zakumbuyoku. Komabe, ngati tavala umunthu watsopano ndipo sitili mbali ya dzikoli tsopano, sitidzatsanzira njira zawo. (Aefeso 4:23, 24, 31; Yakobo 1:19, 20) Mosasamala kanthu za zimene ena akuchita, tidzagwiritsira ntchito uphunguwu wakuti: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”​—Aroma 12:18.

18. Kodi tiyenera kutani ngati mkulu wa boma atikwiyira, ndipo chifukwa ninji?

18 Utumiki wathu nthaŵi zina ungatichititse kukaonekera pamaso pa akuluakulu a boma. Pogwiritsira ntchito ulamuliro wawo, ‘angatifunse’ chifukwa chake timachita zinthu zina kapena chimene timakanira kuchita chinthu chinachake. Angafune kudziŵa chifukwa chimene timalalikirira uthenga umene tili nawo​—umene umavumbula chipembedzo chonyenga ndi umene umanena za mapeto a dongosolo la zinthu lilipoli. Kulemekeza kwathu chitsanzo chimene Kristu anapereka kudzatisonkhezera kusonyeza chifatso ndi ulemu waukulu. (1 Petro 2:23; 3:15) Kaŵirikaŵiri, akuluakulu oterowo amasonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo kapena akuluakulu ena opambana pa iwo. Yankho lofatsa lingawathandize kuzindikira kuti ntchito yathu sikupereka chiwopsezo chilichonse kwa iwo kapena kusokoneza mtendere wa anthu. Yankho lotero limalimbikitsa mzimu wa ulemu, kugwirizana, ndi mtendere kwa awo amene amaulandira.​—Tito 3:1, 2.

19. Kodi Mboni za Yehova sizimatenga mbali m’zochitika ziti?

19 Mboni za Yehova nzodziŵika padziko lonse kukhala anthu amene samatenga mbali m’mikangano ya dziko. Samadziloŵetsa m’mikangano ya dziko pa nkhani za fuko, chipembedzo, kapena zandale. (Yohane 17:14) Chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amatilangiza ‘kumvera maulamuliro aakulu,’ sitiyesa ngakhale kulingalira nkomwe za kuloŵa m’machitidwe osokoneza mtendere wa anthu pokana malamulo a boma. (Aroma 13:1) Mboni za Yehova sizinaloŵepo m’chipani chilichonse chofuna kugwetsa boma. Chifukwa cha miyezo yoikidwa ndi Yehova ya atumiki ake achikristu, izo sizimaganizira nkomwe za kutengamo mbali m’kukhetsa mwazi ndi chiwawa cha mtundu uliwonse! Akristu oona samangolankhula za mtendere; iwo amakhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene amalalikira.

20. Ponena za mtendere, kodi Babulo Wamkulu wakhala ndi mbiri yotani?

20 Mosiyana ndi Akristu oona, awo amene amaimira zipembedzo za Dziko Lachikristu sakusonyeza kukhala amithenga a mtendere. Zipembedzo za Babulo Wamkulu​—matchalitchi a Dziko Lachikristu ndi a zipembedzo zosakhala zachikristu​—zalola nkhondo za mitundu, kuzichirikiza, ndi kukhaladi patsogolo m’nkhondozo. Zasonkhezeranso zizunzo ndipo ngakhale kuphedwa kwa atumiki okhulupirika a Yehova. Chotero, kunena za Babulo Wamkulu, Chivumbulutso 18:24 chimalengeza kuti: “Momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.”

21. Kodi anthu ambiri oona mtima amatani pamene aona kusiyana pakati pa khalidwe la anthu a Yehova ndi la aja omwe akuchita chipembedzo chonyenga?

21 Mosiyana ndi zipembedzo za Dziko Lachikristu ndi Babulo Wamkulu yense chipembedzo choona chili mphamvu yabwino ndi yogwirizanitsa. Kwa otsatira ake oona, Yesu Kristu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chimenecho ndicho chikondi chimene sichimaona malire a mtundu, mikhalidwe ya anthu, chuma, ndi fuko zimene zagaŵanitsa mtundu wonse wa anthu. Ataona zimenezi, mamiliyoni ambiri a anthu padziko lonse lapansi akunena kwa atumiki odzozedwa a Yehova kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zekariya 8:23.

22. Kodi timaiona bwanji ntchito yolalikira imene ikufunikabe kuichita?

22 Monga anthu a Yehova, tikusangalala zedi ndi zimene zakwaniritsidwa, koma ntchitoyo siinathebe. Mlimi atabzala mbewu ndi kulimirira munda wake, iye samalekera ntchito yake pamenepo. Amagwirabe ntchito makamaka pamene nyengo ya kukolola ili pachimake. Nthaŵi yakukolola imafuna nyonga yokulirapo ndi yopitiriza. Ndipo tsopano lino ntchito yaikulu yoposa ndi kale lonse yokolola alambiri a Mulungu woona ili mkati. Ino ndi nthaŵi ya chisangalalo. (Yesaya 9:3) Zoona, timayang’anizana ndi chitsutso ndi mphwayi. Aliyense payekha, tingakhale tikulimbana ndi matenda aakulu, mavuto a m’banja, kapena mavuto a zachuma. Koma chikondi kwa Yehova chimatisonkhezera kulimbikira. Uthenga umene Mulungu watisungiza ndi chinthu chimene anthu afunikira kumva. Ndiwo uthenga wa mtendere. Ndithudi, ndiwo uthenga umene Yesu iye mwini analalikira​—inde, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

Yankho Lanu Nlotani?

◻ Kodi Yesaya 52:7 anakwaniritsidwa motani pa Israyeli wakale?

◻ Kodi Yesu anakhala motani mthenga wa mtendere wamkulu koposa?

◻ Kodi mtumwi Paulo anagwirizanitsa motani Yesaya 52:7 ndi ntchito imene Akristu akuchita?

◻ Kodi kukhala amithenga a mtendere m’tsiku lathu kumaloŵetsamo chiyani?

[Zithunzi patsamba 13]

Monga Yesu, Mboni za Yehova zili amithenga a mtendere waumulungu

[Zithunzi patsamba 15]

Mboni za Yehova zimakhalabe zodekha kaya anthu achite motani ndi uthenga wa Ufumu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena