-
Phindu la Uthenga WabwinoNsanja ya Olonda—2002 | January 1
-
-
Phindu la Uthenga Wabwino
“Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima; . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.”—YESAYA 61:1, 2.
1, 2. (a) Kodi Yesu anadziulula kuti anali yani, ndipo anachita motani zimenezo? (b) Kodi uthenga wabwino umene Yesu analengeza unali ndi phindu lotani?
YESU anali mu Sunagoge ku Nazarete tsiku lina la Sabata kuchiyambi kwa utumiki wake. Malinga ndi nkhaniyo, “anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo mmene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu . . . Uthenga Wabwino.” Yesu anapitiriza kuŵerenga ndime ya ulosiyo. Kenako anakhala pansi n’kunena kuti: “Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.”—Luka 4:16-21.
2 Yesu mwa kuchita zimenezi, anadziulula kuti anali mlaliki woloseredwayo, wolengeza uthenga wabwino ndiponso wotonthoza. (Mateyu 4:23) Ndipotu uthenga umene Yesu analengeza unalidi uthenga wabwino. Iye anawauza omvera ake kuti: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Iye ananenanso kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Inde, Yesu anali ndi “mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:68, 69) Mosakayika, kuwala, moyo, ndiponso ufulu ndi zinthu zabwino kwambiri zofunika kuziyamikira.
3. Kodi ophunzira a Yesu analalikira uthenga wabwino wotani?
3 Pentekoste wa 33 C.E. atatha, ophunzira anapitiriza ntchito ya Yesu yolalikira. Analalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ kwa Aisrayeli ndiponso kwa anthu a mitundu ina. (Mateyu 24:14; Machitidwe 15:7; Aroma 1:16) Amene anamvera uthengawo anam’dziŵa Yehova Mulungu. Anamasuka ku ukapolo wa chipembedzo ndipo anakhala mbali ya m’mtundu watsopano wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” anthu amene akuyembekeza kukalamulira kosatha kumwamba pamodzi ndi Mbuye wawo, Yesu Kristu. (Agalatiya 5:1; 6:16; Aefeso 3:5-7; Akolose 1:4, 5; Chivumbulutso 22:5) Linali phindu lalikulutu limenelo!
Kulalikira Lerolino
4. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino ikukwaniritsidwa motani lerolino?
4 Lerolino, Akristu odzozedwa mothandizidwa ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” akupitiriza kukwaniritsa ntchito yoloseredwayo imene inapatsidwa kwa Yesu poyambirira. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Zotsatira zake n’zakuti uthenga wabwino ukulalikidwa pa mlingo waukulu kuposa kale lonse. Mboni za Yehova m’mayiko ndi m’madera okwana 235 ‘zalalikira mawu abwino kwa ofatsa; kumanga osweka mtima; kulalikira kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; kulalikira chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; kutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’ (Yesaya 61:1, 2) Motero, ntchito yachikristu yolalikira ikupitiriza kupindulitsa anthu ambiri ndi kupereka chitonthozo chenicheni kwa “iwo okhala m’nsautso iliyonse.”—2 Akorinto 1:3, 4.
-
-
Phindu la Uthenga WabwinoNsanja ya Olonda—2002 | January 1
-
-
6. Kodi ndi uthenga wabwino wotani umene ukulalikidwa lerolino?
6 Mboni za Yehova zimalalikira uthenga wabwino kuposa wina uliwonse. Zimatsegula mabaibulo awo ndi kusonyeza anthu omvera kuti Yesu anapereka nsembe moyo wake kuti apatse anthu njira yom’fikira Mulungu, kuwakhululukira machimo awo ndi kuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha. (Yohane 3:16; 2 Akorinto 5:18, 19) Zimalengeza kuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’manja mwa Mfumu yodzozedwa, Yesu Kristu, ndipo kuti posachedwapa udzachotsa kuipa pa dziko lapansi ndi kuyang’anira kubwezeretsedwa kwa Paradaiso. (Chivumbulutso 11:15; 21:3, 4) Izo pokwaniritsa ulosi wa Yesaya, zimauza anansi awo kuti tsopano ndi “chaka chokomera Yehova” pamene mwayi udakalipo woti anthu alabadire uthenga wabwino. Izo zimachenjezanso kuti posachedwapa lifika “tsiku lakubwezera la Mulungu wathu” pamene Yehova adzawononga ochita zoipa onse amene sakulapa.—Salmo 37:9-11.
-