Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2013 | November 15
    • 3 Yesaya anati: “Tamverani! Mtsikana adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli. Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino, nthaka ya mafumu awiri [a Siriya ndi Isiraeli] amene ukuchita nawo mantha ofika podwala nawowo, idzakhala itasiyidwiratu.” (Yes. 7:14, 16) N’zoona kuti mbali yoyamba ya ulosiwu inakwaniritsidwa pa kubadwa kwa Mesiya. (Mat. 1:23) Komatu pa nthawi imene Mesiya ankabadwa “mafumu awiri,” a Siriya ndi Isiraeli, sankafuna kumenyana ndi ufumu wa Yuda. Choncho ulosi wonena za Emanueli umenewu uyenera kuti unakwaniritsidwanso nthawi ya Yesaya.

      4 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yesaya ananena zimenezi, mkazi wake anatenga pakati n’kubereka mwana dzina lake Maheri-salala-hasi-bazi. N’kutheka kuti mwana ameneyu ndi amene Yesaya anamutchula kuti Emanueli.a Kalelo, nthawi zina mwana akabadwa ankapatsidwa dzina lina pofuna kuti anthu azikumbukira zinazake koma kenako makolo ake komanso achibale ankamutchula ndi dzina lina. (2 Sam. 12:24, 25) Koma palibe umboni wosonyeza kuti Yesu ankadziwika ndi dzina loti Emanueli.—Werengani Yesaya 7:14; 8:3, 4.

  • Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2013 | November 15
    • a Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mtsikana” pa Yesaya 7:14 angatanthauze mkazi wokwatiwa komanso namwali. Choncho mawuwa akhoza kugwiritsidwa ntchito ponena za mkazi wa Yesaya komanso Mariya, pa nthawi imene anali namwali.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena