Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/15 tsamba 32
  • Mungakhale ndi “Mtima wa Mkango”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungakhale ndi “Mtima wa Mkango”
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/15 tsamba 32

Mungakhale ndi “Mtima wa Mkango”

NTHAŴI zina Baibulo limagwiritsira ntchito mkango monga chizindikiro cha kulimba mtima ndi chidaliro. Amuna olimba mtima amafotokozedwa kukhala ali ndi “mtima wa mkango,” ndipo olungama akunenedwa kukhala ‘olimba mtima ngati mkango.’ (2 Samueli 17:10; Miyambo 28:1) Mkango umasonyeza kuti ngwoyenerera mbiri yakeyo ya kukhala ‘woposa zilombo kulimba’ makamaka pamene uputidwa.​—Miyambo 30:30.

Kupanda mantha kwa mkango kumafanizidwa ndi kwa Yehova Mulungu potsimikizira kutetezera anthu ake. Yesaya 31:4, 5 amati: “Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzawopa mawu a khamu la abusa oitanidwa kuupitikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lawo; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo ku phiri la Ziyoni . . . Adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.” Motero Yehova amatsimikizira atumiki ake za kusamalira kwake kokangalika, makamaka poyang’anizana ndi nsautso.

Baibulo limayerekezera mdani wamkulu koposa wa anthu, Satana Mdyerekezi, ndi mkango wobuma ndi wolusa. Kuti tipeŵe kukhala nyama yake, tikuuzidwa m’Malemba kuti: “Khalani odzisungira, dikirani.” (1 Petro 5:8) Njira imodzi yochitira zimenezi ndiyo mwa kupeŵa kuwodzera kwauzimu kwakupha. Ponena za zimenezi Yesu anati: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno.” (Luka 21:34-36) Inde, kukhala ogalamuka mwauzimu mu “masiku otsiriza” ano kungatipatse “mtima wa mkango,” umene uli “wokhazikika, wokhulupirira Yehova.”​—2 Timoteo 3:1; Salmo 112:7, 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena