Mutu 16
Chosankha Chotsimikiziritsa Moyo mu Mtendere Weniweni ndi Chisungiko
1. Ngati tipanga chosankha choyenera, kodi ndi mtendere ndi chidaliro zotani zimene zingakhale zathu tsopano?
HA ndichisangalalo chotani nanga kukhala ndi chifuno chenicheni m’moyo, kudziŵa kumene muli kupita! Ndipo ha ndimtendere wamaganizo ndi mtima wotani nanga zochokera m’chitsimikiziro chakuti palibe njira inanso yabwino kwambiri imene mothekera mukanaitsatira! Mtendere ndi chidaliro zoterozo zingakhale zanu, kokha ngati mupanga chosankha choyenera tsopano lino.
2. Kodi ndimotani mmene kufika kwathu pakudziŵa Yehova ndi zifuno zake kumatithandizira ponena za lingaliro lathu pa moyo?
2 Umboni uli wowoneka bwino kuti sitingayang’ane kudziko lino monga magwero amtendere weniweni ndi chisungiko. Madongosolo azamalonda, azipembedzo, ndi andale zadziko, koma kuphatikizapo Mitundu Yogwirizana limodzi ndi zilengezo zake za ‘mtendere ndi chisungiko,’ sangaubweretse. Chifukwa chake, Baibulo limatilozera kwa Yehova Mulungu, monga magwero okha amtendere weniweni ndi chisungiko. Kufikira pa kumdziŵa ndi zifuno zake kumatithandiza kuzindikira chifukwa chake tiri pano padziko lapansi ndi chifukwa chake zinthu ziri monga momwe ziririmu lerolino. Timaphunzira za nkhani yaikulu yolowetsamo ulamuliro wachilengedwe chonse wa Yehova, ndi mmene umayambukilira aliyense wa ife. Timaphunzira kupima kuyenera ndi nzeru za zolinga zathu, ndipo timapeza miyezo yodalirika yamakhalidwe abwino yokhalira ndi moyo. Pamene tiyang’anizana ndi matenda, ukalamba, kapena imfa, tiri ndi chiyembekezo chotonthoza cha moyo m’dongosolo latsopano lolungama, la moyo wabwino, ngakhale mwachiukiriro kuchokera kwa akufa, ngati nkofunika.
3. Kodi nchifukwa ninji Yehova ali uyo amene tiyenera kuikapo ziyembekezo zathu zonse?
3 Pamenepa, mposadabwitsa, kuti Yesaya 26:4 amalangiza kuti: “Khulupilirani Yehova [anthu inu] nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.” Yehova wosasintha, wamphamvu yonse ndi wamuyaya, ndiyedi woyenera kuikapo ziyembekezo zathu zonse. Kodi mukufuna kukhala ndi chitsogozo chake ndi chitetezo osati kokha kaamba ka tsopano lino koma kunthawi yonse yamtsogolo m’Dongosolo lake Latsopano lolonjezedwa? Ngati ziri choncho, kodi muyenera kuchitanji?
4. Kuti tipeze chiyanjo cha Yehova, kodi tifunikira chiyani, ndipo nchiyani chimene chimachitheketsa?
4 Anthu onse ali otalikirana ndi Mulungu chifukwa cha uchimo wamakolo athu oyambilira. Koma Mulungu watsegula njira yakuyanjanitsidwa ndi kuchita ubwenzi naye kupyolera mwa nsembe ya Mwana wake. (2 Akorinto 5:19-21; Aefeso 2:12, 13) Komabe, sikokwanira kwa ife tsopano kungonena kuti tikufuna ubwenzi wa Mulungu.
5. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chisonkhezero chathu m’kufunafuna ubwenzi ndi Yehova?
5 Tiyenera kukhala ofunitsitsa, ngakhale aphamphu, kutsimikizira kwa iye kuti tikuufuna, ndipo ncholinga choyenera. Mwachitsanzo, kodi timafunafuna ubwenzi wa Yehova kokha kuti tipewe tsoka? Ngati titi tipeze kaimidwe kolungama ndi Mulungu, sikungakhale kokha kwanyengo iyi yofulumira chiweruzo chake chisanaperekedwe kapena kokha kupulumuka “chisautso chachikulu” chirinkudza. (Mateyu 24:21, 22) Kuyenera kukhala kwanthawi yonse yamtsogolo. Chikondi chenicheni chokha chidzatipatsa chisonkhezero chimenechi. Chotero tingathe kusonyeza kukhulupirika kwa chikhumbo chathu kaamba ka ubwenzi wake, Yehova wapereka m’Mawu ake zinthu zina zimene ife payekha aliyense tiyenera kuchita kuti tiyanjanitsidwe naye.
Chikhulupiliro Chamoyo
6. Kuti tikondweretse Mulungu, kodi nchidaliro chotani ponena za iye chimene tiyenera kukhala nacho?
6 Yehova ali Mulungu wachowonadi. Chotero ife tingakhale ndi chidaliro chotheratu m’malonjezo ake. Kunena zowona, “wopanda chikhulupiliro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndikuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Ngati inu muli ndi chikhulupiliro chotero, pamenepo mukudziŵa kuti chirichonse chimene Mulungu achita chiri ndi chifuno cholungama, ndi kuti iye nthawi zonse amakondwera nacho koposa. Kuchokera m’ntchito zake zakulenga ndi kuchokera m’Mawu ake olembedwa, mumawona kuti sikokha kuti iye ali Mulungu wanzeru zonse ndi wamphamvu yonse komanso kuti ali wakukoma mtima kwachikondi. Ndithudi, iye sadzapatuka konse pamiyezo yake yolungama. Komabe, ngakhale kuli kwakuti ndife opanda ungwiro ndipo timachita zolakwa, ngati tikonda chilungamo, iye ali ndi njira yakuchita nafe imene idzachititsa madalitso.
7. Kodi ndimotani mmene chidaliro m’kuyenera ndi nzeru za Yehova chidzatichinjirizira?
7 Motero, pamene tilandira chiwongolero kuchokera kwa Mulungu, tidzadziŵa kuti chiri kaamba ka ubwino wathu wamuyaya. Tidzafikira pakudalira Yehova monga momwe mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi amadalirira atate wake wachikondi, wanzeru, ndi wamphamvu. (Salmo 103:13, 14; Miyambo 3:11, 12) Pokhala ndi chikhulupiliro choterocho sitidzakaikira kapena kupenekera nzeru ya uphungu wake kapena kulungama kwanjira zake, ngakhale kuli kwakuti kwakanthawi sitingazindikire kotheratu nkhani zina. Mwakutero timadziika pakati pa awo amene wamasalmo analongosola kuti: “Akukonda chilamulo chanu ali nawo mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.”—Salmo 119:165; Miyambo 3:5-8.
8. (a) Kodi nchifukwa ninji chikhulupiliro chokha chiri chosakwanira? (b) Kodi chikhulupiriro chiyenera kutisonkhezera kukachitidwe kotani kotchulidwa pa Machitidwe 3:19?
8 Koma “chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa,” Yakobo 2:26 amasonyeza motero. Chikhulupiliro chenicheni chimasonkhezera munthu kuchitapo kanthu. Ndipo chimodzi cha zinthu zoyamba chimene chimasonkhezera munthuyo kuchita ndicho chimene mtumwi Petro analimbikitsa kuchita chakuti: “Lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.” (Machitidwe 3:19) Kodi zimenezi zikutanthauzanji?
Kulapa ndi Kubwerera
9. (a) Kodi kulapa kowona nchiyani? (b) Kodi tifunikira kulapa chiyani?
9 M’Baibulo kulapa kumatanthauza kusintha maganizo kotsagana ndi kumva chisoni kochokera mu mtima kaamba kanjira yakale yamoyo kapena machitidwe oipa. (2 Akorinto 7:9-11) Koma ngati titi tisangalale ndi “nyengo zakutsitsimutsa” zolonjezedwazo zochokera kwa Mulungu, sitingangolapa chabe zolakwa zakale. Mmalo mwake, tiyenera kusonyeza kulapa chifukwa chakuti tazindikira kuti, monga ana a Adamu mkhalidwe wathu weniweniwo uli wauchimo. Monga momwe mtumwi Yohane akulongosolera kuti: “Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, . . . timuyesa [Mulungu] wonama, ndipo mawu ake sakhala mwa ife.” (1 Yohane 1:8, 10) Tiyenera kusonyeza Mlengi wathu moyenera, tikumasonyeza ‘chifaniziro ndi chifanefane chake.’ Komabe, uchimo wacholoŵa umatilepheretsa kuchita chimenechi m’njira yangwiro. Chifukwa chake, ‘timaphonya chizindikiro,’ kumene kuli chimene liwu lakuti “uchimo” limatanthauza m’Baibulo.—Genesis 1:26; Aroma 3:23.
10, 11. (a) Kodi tiri ndimangawa kwayani kaamba ka moyo wathu, ndipo chifukwa ninji? (b) Chotero, kodi tiyenera kukhala tikugwiritsira ntchito motani moyo wathu?
10 Chotero tifunikira chikhululukiro cha Mulungu. (Mateyu 6:12) Timazindikira kuti moyo wathu umachokera kwa iye monga Mlengi wathu. Koma tsopano tikuphunzira kuti kupyolera mwa nsembe ya Mwana wa Mulungu, anthu ‘anagudwanso ndi mtengo’ waukulu. Chotero sitiyenera kukhala akapolo a anthu. Osati ngakhale azikhumbo za ife eni za dyera. (1 Akorinto 7:23) Komabe, tisanaphunzire ndi kulandira chowonadi, kodi zimenezo sindizo zimene tonsefe tinali?—Yohane 8:31-34.
11 Mu mtima mwanu, kodi mumayamikira mphatso ya Mulungu ya Mwana wake ndi zimene wachita kupyolera m’kugaŵira chimasuko ku ukapolo wauchimo ndi imfa? Pamenepo ndithudi inu mudzamva chisoni mowona mtima kulephera kulikonse kwakale kwa kugwiritsira ntchito moyo wanu momvera Mlengi wanu. Kumeneku kudzakusonkhezerani kukulapa kochokera mu mtima chifukwa chakukhala mutatsatira njira yamoyo yofanana ndi ija yadziko, yosagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndi zifuno.—Machitidwe 17:28, 30; Chivumbulutso 4:11.
12. Kodi ndimotani mmene munthu wolapa amasonyezera kuti wakanadi njira yake yakale?
12 Kulapa kwenikweni kumeneku kumatsogolera ku ‘kubwerera,’ kumene kuli chimene liwu lakutilo “kutembenuka” limatanthauza. Munthu wolapa mowona mtima samangomva chisoni kokha ndi kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwakale kwa moyo wake. Iye amakana njira yolakwa imeneyo ndipo kwenikweni amafika pakuda njira zake zolakwa. Iye amasonyeza chimenechi mwa ‘kubwerera’ ndi kuchita “ntchito zoyenera kutembenuka mtima,” akumabweretsa moyo wake m’chigwirizano ndi chifuniro cha Mulungu.—Machitidwe 26:20; Aroma 6:11.
13. (a) Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mawu a Yesu akuti otsatira ake ayenera ‘kudzikana’? (b) Chotero kodi timadzigonjetsera kwa Yehova kaamba ka chifukwa chotani, ndipo kodi kumayambukira motani miyoyo yathu?
13 Mbali yakulapa ndi kubwerera imeneyi imalowetsamo chimene Yesu anachitcha ‘kudzikana.’ (Mateyu 16:24) Ndiko kuti, ife sitimakhalanso ndi moyo mogwirizanadi ndi zikhumbo zathu zadyera popanda kudera nkhaŵa chifuniro cha Mulungu ndi zifuno. Mmalomwake, timazindikira kuti Yehova Mulungu kwenikweni ali ndi kuyenera kotheratu kwa miyoyo yathu monga Mlengi ndi Wotigula kupyolera mwa nsembe yadipo ya mwana wake. Monga momwe Baibulo limanenera, ife ‘sitikhala a ife tokha, pakuti tinagudwa ndi mtengo.’ (1 Akorinto 6:19, 20) Chotero, mmalo mwakugwiritsira ntchito molakwa ufulu waukulu wotitsegukira mwachowonadi, timadzigonjetsera mokwanira kukuchita chifuniro cha Mulungu. (Agalatiya 5:13; 1 Petro 2:16) Ndipo timachita ichi osati kokha chifukwa chakuti nkoyenera, koma chifukwa chakuti timakonda Yehova Mulungu ndi ‘mtima wathu wonse, moyo, maganizo ndi nyonga.’ (Marko 12:29, 30) Ndithudi zimenezi zimafunikiritsa aliyense wa ife kukhala ndi moyo wodzipatulira kwa Mulungu. Mmalo mwakukhala yothodwetsa, njira imeneyi imatikhozetsa kusangalala ndi moyo koposa ndi kale lonse.—Mateyu 11:28-30.
Kupanga Chilengezo Chapoyera Kaamba ka Chipulumutso
14. (a) Pamene munthu afikira pakuvomereza umbuye woyenerera wa Yehova pa iye, kodi angasonyeze motani zimenezi kwa Mulungu? (b) Kodi iye ayenera kufuna kuchitanso chiyani, monga momwe kwasonyezedwera pa Aroma 10:10?
14 Chiri chinthu chabwino kwambiri kusonyeza chikhulupiriro chathu m’makonzedwe a Mulungu, tikumavomereza umbuye wake pa ife. Koma tingathe ndipo tiyenera kufuna kunyamula mawu ake achikhulupiriro kuposadi apa, monga momwe Aroma 10:10 amatiuzira kuti: “Ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso.” Mawu “apoyera” amenewa achikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi makonzedwe ake ayenera kutuluka mokondwera kuchokera mu mtima wodzaza chiyamikiro. Kupanga chilengezo chimenechi kumalowetsamo kupatulira moyo wathu kwa Yehova kuchita chifuniro chake ndi kusonyeza kumeneku mwa ubatizo wa m’madzi.
15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira mwamphamvu ponena za ubatizo wa m’madzi?
15 Pamene Yesu Kristu anayamba uminisitala wake wapoyera, analola Yohane Mbatizi kum’miza m’madzi. Baibulo limasimba kuti Yesu pamenepo anati kwa Mulungu: “Ndafika kudzachita chifuniro chanu.” (Ahebri 10:9; Salmo 40:7, 8) Yesu analangiza kuti onse amene afikira kukhala ophunzira ake ayeneranso kubatizidwa. Kodi inu muli wophunzira wotero? Pamenepo ubatizo wanu wa m’madzi udzakhala “chilengezo chapoyera” cha kumeneku.—Mateyu 28:19, 20.
16. (a) Kodi mungadziŵe motani ngati muli wokonzekera kubatizidwa? (b) Kodi ndimotani mmene oyang’anira amathandizira anthu m’kukonzekera ubatizo?
16 Uli mwaŵi waukulu kukhala Mboni yodzipatulira, yobatizidwa ya Yehova, Mfumu yachilengedwe chonse. Pendani tsopano chimene uku kumalowetsamo: Yehova mwachikondi wakutsegulirani njira yakukhala bwenzi lake. Koma kuti muupeze, muyenera kukhala ndi chikhulupiliro, kukhulupiriradi kuti Baibulo ndilo Mawu ouziridwa a Mulungu. (2 Timoteo 3:16, 17) Muyeneranso kusonyeza chikhulupiliro m’nsembe yadipo ya Yesu monga njira yokha yopezera kaimidwe kovomerezeka ndi Mulungu. (Machitidwe 4:12) Mufunikira kuzindikira kudalira kwanu pa Yehova ndi kugonjetsera moyo wanu kwa iye kuchita chifuniro chake, osati kokha kwazaka zoŵerengeka, koma kosatha. Njira yotero imaloŵetsamo ‘kusakhala mbali yadziko.’ (Yohane 17:16, NW; 1 Yohane 2:15) Monga umboni wakuti mwalapa ndi ‘kubwerera,’ muyenera kukhala mutasiya machitachita aliwonse osemphana ndi miyezo yolungama ya Mulungu ndipo muyenera kukhala mukuchita zimene Mulungu amalamulira. Kodi mwasanduliza maganizo anu kotero kuti umu ndimo mmene mukuwonera moyo tsopano? (Aroma 12:1, 2) Ngati ziri choncho, Baibulo likukulimbikitsani kupanga “chilengezo chapoyera” chachikhulupiliro chotero. Njira yoyamba ikakhala kufikira mmodzi wa oyang’anira ampingo wa Mboni za Yehova m’dera lanu ndi kumuuza mmene mukulingalirira. Iye azachita makonzedwe akupenda nanu ziphunzitso zazikulu Zabaibulo mokonzekera ubatizo.
17. Mogwiritsira ntchito Baibulo, sonyezani mmene tiyenera kupitirizira kupanga ‘chilengezo chapoyera chachikhulupiliro chathu.’
17 Njira yaubatizo sidzakhala chizindikiro chamapeto akupanga kwanu ‘chilengezo chapoyera cha chikhulupiliro chanu.’ Monga Mkristu wodzipatulira wa Yehova Mulungu, mudzafuna kulengeza chikhulupiliro chanu mwakulankhula kwanu pamsonkhano wapoyera, ‘kumyamika pamsonkhano waukulu.’ (Salmo 35:18; 40:9, 10) Mudzafunanso kukhala ndi phande m’ntchito yapadera ya “chilengezo chapoyera” imene Yehova wagaŵira kwa onse amene akufuna kumtumikira—kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu padziko lonse ndi kupanga ophunzira mwa anthu amitundu yonse.—Mateyu 24:14; 28:19.
Kusungabe Unansi wanu ndi Mulungu
18. Kodi phunziro laumwini nlofunika motani m’kutsimikizira kuti unansi wa munthuyo ndi Yehova udzakhala wosatha?
18 Tsopano, pamenepa, kodi mungatsimikizire motani kuti pamene wapezedwa, unansi wanu udzakhala wosatha ku umuyaya wonse mu mtendere wosangalatsa ndi chisungiko? Choyamba mudzafuna kupitirizabe kukula m’kumdziŵa iye. Kupyolera mwa phunziro la inumwini mudzapeza chikondwerero chenicheni chanzeru choikidwa m’Mawu a Mulungu. Mungakhale ngati munthu amene Salmo 1:2, 3 limalongosola kuti: “M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingilira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pamitsinje yamadzi; wakupatsa chipatso chake panyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” Inde, kupeza chidziŵitso cha Mulungu, ndi kuchigwiritsira ntchito, kudzakukhozetsani kuyenda mu “njira zokondweretsa” ndi ‘m’mayendedwe amtendere,’ chifukwa chakuti chidzakupatsani nzeru yolimbanira ndi mavuto onse a moyo. (Miyambo 3:13, 17, 18) Ludzu la chidziŵitso chotero Chabaibulo tsopano lidzasonyeza kuyenelera kwanu kaamba ka moyo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu, chifukwa chakuti pamenepo “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzadza nyanja.”—Yesaya 11:9.
19. Kodi nchifukwa ninji kufika mokhazikika pamisonkhano kuli kofunika m’moyo wa anthu a Yehova?
19 Kanthu kenanso kamene mukufunikira kwambiri ndiko kufika pamisonkhano ndi atumiki ena a Yehova. Pamenepo mudzapezapo chisonkhezero chenicheni kuchikondi ndi ntchito zabwino, chilimbikitso chakupitirizabe kusunga unansi wanu wabwino ndi Mulungu. (Ahebri 10:23-25, NW) Gulu lokondweretsa, longa banja la atumiki a Yehova likupereka umboni wolimbikitsa wakuti mtendere ndi chisungiko zolonjezedwa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu ziri zenizeni.—Salmo 133:1; 1 Akorinto 14:26, 33.
20. Kodi ndimotani mmene akulu mu mpingo angatithandizire m’nthawi zachitsutso ndi vuto lathu?
20 Mu mpingo mungapindule ndi makonzedwe ena achikondi. Yesu, ‘Mbusa Wabwino,’ ali ndi ‘abusa ang’ono’ padziko lapansi. Amenewa ndiwo oyang’anira, kapena akulu auzimu, amene amasamalira “nkhosa” zake. Iwo ali chochititsa champhamvu m’kupititsa patsogolo mtendere ndi chisungiko pakati pa anthu osonkhanitsidwa padziko lonse lapansi. (1 Petro 5:2, 3) Amuna amenewa amatsimikizira kukhala monga ‘pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wathanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.’ (Yesaya 32:1, 2) Inde, m’nthawi zamkuntho mavuto chifukwa cha chitsutso chadziko kapena zovuta zanu, mwachikhulupiliro chawo chonga thanthwe ndi kumamatira kwawo zolimba ku Mawu a Mulungu, akulu auzimu amenewa amapereka chichirikizo chenicheni. Angathe kukupatsani uphungu wotsitsimula ndi chilimbikitso.
21. Kodi nchiyani chimene chidzatitetezeradi kusalola konse zolakwa za ena kuvulaza unansi wathu ndi Yehova?
21 Nzowona kuti kupanda ungwiro kwaumunthu kudzawonekera, ngakhale pa atumiki a Mulungu. Ife tonse timapanga zolakwa tsiku ndi tsiku. (Yakobo 3:2) Koma kodi tidzadzilola kukhumudwitsidwa ndi zolakwa za ena ndi kulola zimenezi kuvulaza unansi wathu ndi Yehova? Popeza kuti nafenso, timalakwa, kodi sitiyenera kusonyeza ena chikhululukiro chofananacho chimene timachifuna kwa ife eni? (Mateyu 6:14, 15) Ngati titi tidzitsimikizire kukhala nzika zoyenelera Dongosolo Latsopano lamtendere la Mulungu, tiyenera kusonyeza tsopano luso lathu la kukhalira limodzi ndi ena mu mtendere. Sitingathe kukonda Mulungu popanda kukondanso abale ndi alongo athu auzimu amene Kristu anawafera.—1 Yohane 4:20, 21.
22. Kodi pemphero liyenera kukhala ndi malo otani m’miyoyo yathu?
22 Unansi wanu woyenera ndi Mulungu umakupatsani mwaŵi wina waukulu: kufika kwa Mulungu mwapemphero ndi chitsimikiziro chakuti amakumvani. Sunganibe mwaŵi umenewo ndi kuugwiritsira ntchito tsiku ndi tsiku, mkati mwatsiku lonse. Mavuto azabuka. Kupanda kwanu ungwiro kungakuvutitseni. Komabe Baibulo limapereka uphungu wakuti: “Musadere nkhawa konse, komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
23. Pamene tiyang’anizana ndi mayeso ndi mavuto achikhulupiriro chathu, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupilira?
23 Mwakusankha kutumikira Yehova, Magwero amtendere ndi chisungiko, ndi kuika chidaliro chanu m’Dongosolo Latsopano, mudzakhala mutapanga chiyambi chabwino. Tsopano, monga momwe Baibulo limanenera, “chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.” (Ahebri 10:36) Pokhala mutalaŵa madalitso a unansi wabwino ndi Yehova, tsimikizani kusaŵasiya konse. Musalole konse zikondwerero zakanthawi zadziko kukupatutsani. Ngakhale kuli kwakuti ziyeso zochokera m’dziko lamdani zikukhala zazikulu kwambiri, kumbukirani kuti zimenezi nzakanthawi. Poyerekezeredwa ndi madalitso amene Yehova adzapereka kwa awo omkonda, kuvutika kotero sikuli kanthu konse.—2 Akorinto 4:16-18.
24. (a) Kodi ife lerolino tiri ndi chifukwa chosangalalira kwenikweni ndi chiyani? (b) Mofanana ndi wamasalmo, kodi tiyenera kulingalira motani nthawi zonse ponena za Yehova ndi unansi wathu ndi iye?
24 Pitirizanibe m’njira yakudzipereka kwaumulungu, muli ndi chidaliro chakuti ndiyo njira yabwino koposa yamoyo tsopano ndi imene idzatsogolera ku moyo wamuyaya m’Dongosolo Latsopano la Mulungu. (1 Timoteo 4:8) Sangalalani ndi umboni wakuyandikira kwa Dongosolo Latsopano limenelo ndi mtendere wosatha ndi chisungiko zimene lidzadzetsa. Pamene mukupitiriza kukulitsa unansi wanu ndi Yehova, nthawi zonse lingalirani monga momwe anachitira wamasalmo wouziridwayo amene analemba kuti: “Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha. Pakuti tawonani, iwo okhala patali ndi inu adzawonongeka; muwononge onse akupembedza kwina, kosiyana ndi inu. Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.”—Salmo 73:26-28.
[Zithunzi patsamba 181]
Kupanga Chilengezo Chapoyera