Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama’
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | September
    • 6. Kodi n’chiyani chidzachitike a khamu lalikulu akadzapulumuka chisautso chachikulu? Fotokozani. (Onaninso nkhani yakuti, “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” m’magaziniyi, kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kuukitsidwa kwa omwe adzakhale padzikoli.)

      6 Werengani Danieli 12:2. Kodi chidzachitike n’chiyani khamu lalikulu likadzapulumuka pa nthawi ya masautsoyi? Ulosiwu sukunena za kuukitsidwa kophiphiritsa kapena kwauzimu komwe kukuchitika masiku otsiriza ano, monga mmene tinkakhulupirira m’mbuyomu.c M’malomwake, mawuwa akunena za kuukitsidwa kwa anthu komwe kudzachitike m’dziko latsopano. N’chifukwa chiyani tikutero? Mawu akuti “munthaka,” kapena kuti m’fumbi, omwe agwiritsidwanso ntchito pa Yobu 17:16, ndi ofanana ndi mawu akuti “manda.” Choncho lemba la Danieli 12:2, likunena za kuukitsidwa kumanda komwe kudzachitike masiku otsiriza akadzatha komanso pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo.

      7. (a) Kodi kuukitsidwa kwa anthu ena kuti adzalandire “moyo wosatha” kumatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kumeneku ndi “kuuka kwabwino kwambiri”?

      7 Kodi lemba la Danieli 12:2, limatanthauza chiyani likamati ena adzaukitsidwa kuti alandire “moyo wosatha”? Limatanthauza kuti pa nthawi ya zaka 1,000 anthu oukitsidwa omwe adzadziwe kapena kupitiriza kudziwa ndi kumvera Yehova ndi Yesu, adzapatsidwa moyo wosatha. (Yoh. 17:3) Kumenekutu kudzakhala “kuuka kwabwino kwambiri” kuposa kwa anthu amene anaukitsidwapo m’mbuyomu. (Aheb. 11:35) N’chifukwa chiyani? Chifukwa anthuwa sanali angwiro ndipo anamwaliranso.

      8. Kodi zikutanthauza chiyani kuti ena adzauka kuti alandire ‘chitonzo ndiponso kudedwa mpaka kalekale’?

      8 Koma si oukitsidwa onse omwe adzavomereze kuphunzitsidwa ndi Yehova. Ulosi wa Danieli unanena kuti ena adzauka kuti ‘alandire chitonzo ndipo adzadedwa mpaka kalekale.’ Chifukwa chakuti adzasonyeza kusamvera, mayina awo sadzalembedwa m’buku la moyo ndipo sadzapatsidwa moyo wosatha. M’malomwake, iwo “adzadedwa mpaka kalekale” kapena kuti adzawonongedwa. Choncho lemba la Danieli 12:2, likufotokoza zimene zidzachitikire oukitsidwa onse potengera zimene azidzachita pambuyo pa kuukitsidwa kwawoko.d (Chiv. 20:12) Ena adzalandira moyo wosatha pomwe ena adzawonongedwa.

  • ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama’
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | September
    • a Nkhaniyi ifotokoza kamvedwe kathu katsopano kokhudza ntchito yaikulu yophunzitsa yofotokozedwa pa Danieli 12:2, 3. Tiona nthawi yomwe ntchitoyi idzagwiridwe komanso amene adzaigwire. Tionanso mmene ntchito yophunzitsayi idzathandizire anthu okhala padzikoli kukonzekera mayesero omaliza kumapeto kwa Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000.

  • ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kuti Akhale Olungama’
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | September
    • c Zimenezi zikusintha zomwe tinafotokoza m’buku la Samalani Ulosi wa Danieli! mutu 17, komanso mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1987, tsamba 21-25.

      d Mosiyana ndi zimenezi, mawu akuti “olungama” ndi “osalungama” opezeka pa Machitidwe 24:15, komanso akuti “amene anali kuchita zabwino” ndi “amene anali kuchita zoipa” opezeka pa Yohane 5:29, akunena za zochita za oukitsidwawo asanamwalire.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena