Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
    Samalani Ulosi wa Danieli!
    • 21. (a) Kodi nyengo ya nthaŵi yonenedweratu pa Danieli 12:11 ikayamba pochitika mikhalidwe yotani? (b) Kodi “nsembe yachikhalire” inali chiyani, ndipo inachotsedwa liti? (Onani bokosi la patsamba 298.)

      21 Danieli anauzidwa kuti: “Kuyambira nthaŵi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana aŵiri kudza makumi asanu ndi anayi.” Choncho nyengo ya nthaŵi imeneyi inayenera kuyamba pamene mikhalidwe inayake itayamba. “Nsembe yachikhalire,” kapena “nsembe yopitirira”a inayenera kuchotsedwa. (Danieli 12:11, NW, mawu am’munsi) Ndi nsembe yotani imene mngeloyo amanena? Si nsembe za nyama zoperekedwa pakachisi aliyense wa padziko lapansi. Eya, ngakhale kachisi wa ku Yerusalemu anali chabe ‘wakutsanza woonayo’—woonayo anali kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova, amene anayamba kugwira ntchito pamene Kristu anakhazikitsidwa monga Mkulu wa Ansembe mu 29 C.E.! M’kachisi wauzimu ameneyu, amene akuimira makonzedwe a Mulungu a kulambira koyera, simufunikira nsembe za uchimo zopitirira, chifukwa ‘Kristu anaperekedwa nsembe kamodzi kusenza machimo a ambiri.” (Ahebri 9:24-28) Komabe, Akristu oona onse amapereka nsembe m’kachisi ameneyu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mwa Iye [Kristu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15) Choncho mkhalidwe woyamba wa ulosi umenewu—kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire”—unakhalapo pakatikati pa 1918 pamene ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuferatu.

      22. (a) Kodi “chonyansa” chopululutsa n’chiyani, ndipo chinakhazikitsidwa liti? (b) Kodi nyengo ya nthaŵi yonenedweratu pa Danieli 12:11 inayamba liti, ndipo inatha liti?

      22 Bwanji nanga za mkhalidwe wachiŵiri—‘kuimikidwa,’ kapena kukhazikitsidwa, kwa “chonyansa chakupululutsa”? Monga tinaonera pofotokoza Danieli 11:31, chonyansa chimenechi poyamba chinali bungwe lotchedwa League of Nations limene linadzatulukiranso pambuyo pake monga United Nations. Mabungwe onse aŵiriwo n’ngonyansa m’ganizo lakuti akhala akulengezedwa monga chiyembekezo chokha chopezera mtendere padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezo, m’mitima ya ambiri, mabungwe ameneŵa kwenikweni alanda malo Ufumu wa Mulungu! Bungwe la League of Nations linalengezedwa mwalamulo mu January 1919. Panthaŵiyo, mikhalidwe yonse iŵiri ya pa Danieli 12:11 inachitika. Choncho, masiku 1,290 anayamba kumayambiriro kwa 1919 ndipo anapitirira mpaka m’chilimwe cha 1922.

      23. Kodi opatulika a Mulungu anapita bwanji patsogolo pokhala ndi khalidwe loyeretsedwa m’kati mwa masiku 1,290 onenedweratu pa Danieli chaputala 12?

      23 M’kati mwa nthaŵi imeneyo, kodi opatulikawo anapita patsogolo pankhani ya kuyeretsedwa ndi kutsukidwa pamaso pa Mulungu? Anatero kumene! M’March 1919, pulezidenti wa Watch Tower Society ndi anzake anatulutsidwa m’ndende. Pambuyo pake anamasulidwa ku milandu yonse yowanamizira. Pozindikira kuti ntchito yawo inali isanathebe, anakangalikanso mwachangu, nalinganiza msonkhano waukulu mu September 1919. M’chaka chimenechonso, inzake ya magazini ya Nsanja ya Olonda inayamba kufalitsidwa. Poyamba inali kutchedwa The Golden Age, (tsopano Galamukani!) Nthaŵi zonse yachirikiza Nsanja ya Olonda povumbula mopanda mantha mikhalidwe yovunda ya dzikoli ndi kuthandiza anthu a Mulungu kukhalabe oyera. Pofika kumapeto kwa masiku 1,290 onenedweratuwo, opatulika anali m’kati mwa kuyeretsedwa ndi kubwezeretsedwa ku mkhalidwe wawo wabwino. Mu September 1922, pafupi kwenikweni ndi pothera nyengo imeneyi, iwo anakhala ndi msonkhano wapadera kwambiri ku Cedar Point, Ohio, U.S.A. Msonkhanowo unapereka chisonkhezero chachikulu pa ntchito yolalikira. Komabe, panafunikira kupitabe patsogolo. Zimenezo zikachitika m’nyengo yotsatira yoikidwiratu.

    • [Bokosi pamasamba 298]

      KUCHOTSEDWA KWA NSEMBE YACHIKHALIRE

      M’buku la Danieli, mawu akuti “nsembe yachikhalire” amapezeka kasanu. Amanena za nsembe zachitamando—“chipatso cha milomo”—zimene atumiki a Yehova Mulungu amapereka kwa iye nthaŵi zonse. (Ahebri 13:15) Kuchotsedwa kwake konenedweratu kumatchulidwa pa Danieli 8:11, 11:31, ndi 12:11.

      M’kati mwa nkhondo ziŵirizo za padziko lonse, anthu a Yehova anazunzidwa koopsa mu ulamuliro wa “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera.” (Danieli 11:14, 15) Kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire” kunachitika chakumapeto kwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse pamene ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuferatu chapakatikati pa 1918. (Danieli 12:7) M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, “nsembe yachikhalire” ‘inachotsedwanso’ kwa masiku 2,300 ndi Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America. (Danieli 8:11-14; onani Mutu 10 wa buku lino.) Inachotsedwanso ndi “ankhondo” a Nazi kwa nyengo ya nthaŵi imene utali wake sunatchulidwe m’Malemba.—Danieli 11:31; onani Mutu 15 wa buku lino.

  • Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
    Samalani Ulosi wa Danieli!
    • Masiku 1,290: January 1919 mpaka

      Danieli 12:11 September 1922

      (Akristu odzozedwa auka

      napita patsogolo mwauzimu.)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena