CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AMOSI 1-9
“Yesetsani Kufunafuna Yehova Kuti Mupitirize Kukhala ndi Moyo”
Kodi kufunafuna Yehova kumatanthauza chiyani?
Kumatanthauza kupitiriza kuphunzira za iye komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wathu
Kodi chinkachitika n’chiyani Aisiraeli akasiya kufunafuna Yehova?
Ankasiya ‘kudana ndi zoipa ndipo sankakonda zabwino’
Ankayamba kuchita zinthu zongodzisangalatsa okha
Ankasiya kutsatira malamulo a Yehova
Kodi Yehova watipatsa zinthu ziti pofuna kutithandiza kuti tizimufunafuna?