Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Machenjezo Aumulungu Amene Amakuyambukirani
    Nsanja ya Olonda—1989 | April 15
    • Mulungu abweretsa tsoka pa awo a liwongo la chiwawa molimbana ndi anthu ake. Kodi nchiyani chimene chiri chifukwa kaamba ka tsoka la Aedomu? Machitidwe obwerezedwabwerezedwa achiwawa molimbana ndi ana amuna a Yakobo, abale awo. Monga mbadwa za Esau, Aedomu anali pa ubale kwa Aisrayeli. Komabe, iwo akupatsidwa mlandu wa kulanda fuko lawo, kusangalala mwankhalwe pa kugwa kwa Yerusalemu, ndi kufikitsa chimenechi pachimake mwa kupereka opulumuka kwa mdani. Chotero, Edomu wasindikiza kugwa kwake.​—10-16.

  • Machenjezo Aumulungu Amene Amakuyambukirani
    Nsanja ya Olonda—1989 | April 15
    • ○ 10​—Edomu anaweruzidwa “nawonongeka ku nthaŵi yonse” chifukwa cha udani wake wowononga ndi kusoweka kwa chikondi cha chibadwa kolimba kaamba ka mtundu wake wachibale, “ana a Yuda.” (Vesi 12) Kuzimitsidwa kwa mtundu koteroko kunatanthauza kuti ufumu wa Edomu ndi boma limodzinso ndi anthu pamalo a dziko odziŵika ukazimiririka pa nkhope ya dziko lapansi. Lerolino, palibe anthu ozindikirika a mtundu wa Edomu; iwo “akhala monga ngati sanalipo.”​—Vesi 16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena