Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’
    Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
    • Ulendo Wopita ku Betelehemu

      Yosefe ndi Mariya sanali okha paulendowu. Kaisara Augusto anali atangopereka lamulo loti m’dzikomo muchitike kalembera, motero aliyense anayenera kubwerera kumzinda wa kwawo. Kodi Yosefe anatani? Nkhaniyi imati: “Yosefe nayenso anakwezeka mtunda kuchokera ku Galileya, mu mzinda wa Nazarete, ndi kupita ku Yudeya, ku mzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide.”​—Luka 2:1-4.

      N’zosadabwitsa kuti Kaisara anapereka lamuloli panthawi imeneyi, chifukwa ulosi wina umene unalembedwa zaka pafupifupi 700 m’mbuyomo, unalosera kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Panali mzinda wina wotchedwa Betelehemu womwe unali pamtunda wa makilomita 11 kuchokera ku Nazareti. Koma ulosiwu unanena mwachindunji kuti Mesiya adzabadwira ku “Betelehemu Efrata.” (Mika 5:2) Tikatengera misewu ya masiku ano, Betelehemu Efrata ali kum’mwera, pamtunda wa makilomita 150 kuchokera ku mzinda wa Nazareti. Kumeneku n’kumene Yosefe anauzidwa kuti apite, chifukwa n’kumene kunali kumudzi kwa mbumba ya Mfumu Davide. Yosefe ndi mkazi wake Mariya anali a mbumba imeneyi.

  • ‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’
    Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
    • Kodi n’chinthu chinanso chiti chimene mwina chinachititsa kuti Mariya amvere mwamuna wake? Kodi n’zotheka kuti ankadziwa za ulosi wonena kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu? Ngakhale kuti Baibulo silinena chilichonse pankhaniyi, n’zotheka kuti Mariya ankadziwa zimenezi. Tikutero chifukwa choti zikuoneka kuti atsogoleri achipembedzo ngakhalenso anthu wamba ambiri ankadziwa ulosi umenewu. (Mateyo 2:1-7; Yohane 7:40-42) Ndiponsotu Mariya sanali mbuli pankhani ya Malemba. (Luka 1:46-55) Mulimonsemo, kaya Mariya anachita zimenezi pomvera mwamuna wake, kaya pomvera lamulo la boma, kapena ulosi wa Yehova, kapena pa zifukwa zingapo mwa zifukwa zimenezi, mfundo ndi yakuti iye anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Yehova amasangalala kwambiri ndi amuna komanso akazi amene ali ndi mtima wodzichepetsa ndiponso womvera. Masiku ano anthu ambiri amanyoza kwambiri anthu okonda kugonjera. N’chifukwa chake, padziko lonse, anthu okhulupirika kwa Mulungu ayenera kutsatira chitsanzo chabwino kwambiri cha Mariya.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena