Chaputala 10
Chimene Mulungu Analumbirira Kuchitira Anthu—Tsopano Chayandikira!
1, 2. (a) Kodi Mulungu amalumbira m’lingaliro lotani, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi Mulungu amanenanji pa Yesaya 45:23? (c) Kodi ndimawu otani a mneneri Yesaya amene tiyenera kuvomerezana nawo?
KODI Mulungu amalumbira? Inde, Mulungu amalumbira, koma samatukwana, kukwiya ndi kutayikiridwa ndi kudziletsa. Nthaŵi zonse kulumbira kwake kumachitidwira kuchirikiza chimene amanena kukhala chifuno chake. Kumapereka chitsimikiziro chowonjezereka kwa amene adzayambukiridwa. Chifukwa chake, anthu onse amachita bwino kumvetsera mawu ake pa Yesaya 45:23: “Ndadzilumbira ndekha, mawu achokera mkamwa mwanga m’chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira ine, malirime onse nadzalumbira ine.”
2 Lerolino, zoposa zaka 2 700 pambuyo pa ulosi umenewo, kodi tiri okhutira kuti mawu a mneneriyo pa Yesaya 45:24 ngwowona: “Koma mwa Yehova Yekha, wina adzati kwa ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi”? Ngati ziri choncho, pamenepo tingathe kuvomerezananso ndi mawu otsatira a Yesaya m’vesi 25: “Mwa Yehova mbewu yonse ya Israyeli idzapulumutsidwa ndi kudzikuza.”
3, 4. (a) Kodi ndichifukwa ninji Yesaya 45:25 sayenera kutichititsa kulingalira za Lipabuliki la Israyeli? (b) Kodi pakhalapo kulephera kulikonse m’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 45:23-25, ndipo kodi ndichifukwa ninji muyankha motero?
3 Pamene tiŵerenga Yesaya 45:25, kodi tiyenera kulingalira za Lipabuliki la Israyeli? Ayi! Aisrayeli amenewo samapereka thamo kwa Mulungu wa Malemba awo Opatulika Achihebri kaamba ka chilakiko chawo. Chifukwa cha kulilemekeza kolakwika iwo amakanadi kutchula dzina lakelo.
4 Mwa mawu ameneŵa, kodi tikunena kuti Yesaya 45:23-25 walephera kukwaniritsidwa kufikira chaka chino? Ayi! Sipanakhale kulephereka m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa nthaŵi yoikidwiratu ya Yehova. Kwa iye, kulephereka kwa ulosi wake kuli kosatheka! Sikokha kuti mawu ake mwa iwo okha ngodalirika ndi okhulupirika koma kwakukulukulu ziri choncho pamene Yehova alilumbirira nawonjezera lumbiro lake, kutsimikizira nkhaniyo.
Mulungu Aloŵa ndi Lumbiro
5. Kodi ndimotani mmene Ahebri 6:13-18 amalongosolera kuloŵerera kwa Mulungu ndi lumbiriro m’lonjezo kwa Abrahamu?
5 Ponena za zimenezi, timaŵerenga pa Ahebri 6:13-18: “Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m’chitsutsano chawo chirichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuwonetsera mochulukira kwa oloŵa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analoŵa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziŵiri zosasinthika, mmene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathaŵira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu.”
6. (a) Kodi ndichisonkhezero chotani chimene chinalipo chakuti Mulungu adzilumbire ponena za lonjezo lake kwa Abrahamu? (b) Kodi Yehova akagwiritsira ntchito motani “bwenzi” lake?
6 Kaŵirikaŵiri, pamakhala chisonkhezero champhamvu cha kulumbirira, kuperekera lumbiro. Zimenezo ziri makamaka zowona pamene kulumbirako kuli chikhumbo cha Mulungu mwini, kodzifunira. Chisonkhezero chotero chikuperekedwa m’nkhani iyi imene Yehova akusimbidwa kukhala akulumbira, inde, kudzilumbira yekha. Lonjezo lophatikizapo lumbiro limene Yehova anapanga kwa Abrahamu, “bwenzi” lake, limayambukira ife tonse lerolino. Yehova anayamikira pamene Abrahamu anachitapo kanthu molabadira chiitano cha Mulungu nachoka kudziko la kwawo kumka kudziko limene Yehova akapatsa mbadwa za Abrahamu kukhala lawolawo. Yehova akanapanga mosavuta dzina la “bwenzi” limeneli kukhala lalikulu ndipo akanamgwiritsira ntchito kudalitsira ena. Yehova akananena bwino lomwe kwa iye kuti: “Ndipo ndidzadalitsa awo amene akukudalitsa, ndipo iye wa kutemberera ndidzamtemberera, ndipo mabanja onse a padziko lapansi azadzidalitsadi mwanjira ya iwe.”—Genesis 12:3, NW; Yesaya 41:8.
7. (a) Kodi Mulungu anadalitsa Abrahamu ndi chozizwitsa chotani pamene mkazi wake anali ndi msinkhu wa zaka 90? (b) Kodi Abrahamu anasonyeza motani chikhulupiriro chake ndi kumvera mwa njira yapadera?
7 Pamene mkazi wa Abrahamu Sara anali ndi zaka 90 za kubadwa, atapitirira kwambiri msinkhu wobala ana, Mulungu mozizwitsa anamdalitsa kuti abalire Abrahamu mwana wawo wokondedwa, Isake, kupititsa patsogolo lonjezo Lake lodabwitsa kwa Abrahamu. Abrahamu anadzitsimikizira kukhala wokonzekera ndi wofunitsitsa kupereka ngakhale mwana wokondedwa ameneyo kukhala nsembe yaumunthu momvera lamulo la Mulungu wake, Yehova. Chisonyezero chapadera cha chikhulupiriro ndi kumvera chimenechi chinasonkhezera Yehova kwambiri kotero kuti anati kwa “bwenzi” lake, Abrahamu:
8, 9. (a) Kodi Yehova anayankha motani chisonyezero chimenechi cha chikhulupiriro cha Abrahamu ndi kumvera? (b) Kodi Mulungu anadzipanga kukhala ndi thayo kwa yani?
8 “Pa ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wayekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi zakumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo; m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadzidalitsadi (NW): chifukwa wamvera mawu anga.”—Genesis 22:15-18.
9 Ameneŵa ndiwo malo oyamba m’Baibulo kumene Yehova akusimbidwa kukhala akulumbira. Chifukwa chakuti iye sakanalumbira munthu wina wamkulu kwambiri kuposa iye, anadzilumbira, akumadzigwirizanitsa nalo. Mwanjira imeneyi anachititsa kuti pasakhale munthu wina woŵerengerako kusiyapo iye yekha. Kuyenera kukhala kukwaniritsa chifuno chake kaamba ka thamo la iye yekha.
Kumlingo Wotani?
10. Kodi ndipafupifupi utali wotani kalelo pamene Mulungu anachita pangano lake ndi Abrahamu, ndipo chifukwa chake ndifunso lotani limene limabuka?
10 Abrahamu analoŵa m’dziko lolonjezedwa la Kanani pafupifupi zaka 4 000 zapitazo. Chotero tsopano, kodi ndikumlingo wotani ku umene pangano limenelo lochitidwa 1943 B.C.E. lakwaniritsidwira?
11. (a) Kodi kukhala membala ya UN kwa Lipabuliki la Israyeli kumasonyeza chiyani, ndipo ndizotulukapo zotani? (b) Kodi mbadwa zakuthupi za Abrahamu zimafikitsa ziyeneretso za kukhala “mbewu” yolonjezedwa?
11 Lerolino, ku Middle East kuli Lipabuliki la Israyeli. Chifukwa cha dyera, iyo iri memambala ya Mitundu Yogwirizana. UN imaimira kukanidwa kwa Ufumu wa Yehova kupyolera mwa “mbewu” yolonjezedwa ya Abrahamu ndipo motero idzawonongedwa ‘m’nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu wa Mphamvuyonse,’ Armagedo. Membala iriyonse ya UN, kuphatikizapo Lipabuliki la Israyeli, adzawonongedwa psiti. Mwachisoni, mbadwa zakuthupi, zachibadwidwe za Abrahamu sizikufikitsa zofunika kuti zikhale “mbewu” Yaumesiya kupyolera mwa imene Yehova Mulungu adzadalitsira anthu onse.—Chivumbulutso 16:14-16.
12, 13. (a) Mosiyana ndi Davide kholo lake, kodi ndichifukwa ninji “Kalonga wa Mtendere” sadzalamulira yekha? (b) Kodi Akristu odzozedwa anafunikira kuyembekezera kufikira Ufumuwo utakhazikitsidwa m’1914 kuti alandire dalitso lolonjezedwa, ndipo tidziŵa bwanji?
12 Mowoneka mokwanira kuti munthu aliyense awone, Mesiya wolonjezedwayo samalamulira ku Yerusalemu wa padziko lapansi, wa ku Middle East kaamba ka kukwaniritsidwa kwa pangano la Abrahamu. Mosiyana ndi Davide kholo lake lakale, Mesiya ndi “Kalonga wa Mtendere” sadzalamulira yekha. Iye analonjeza kugwirizana naye mu ulamuliro wake atumwi ake okhulupirika 12 ndi ophunzira ake ena obadwa ndi mzimu, ofikira chiŵerengero cha 144 000. (Chivumbulutso 7:1-8; 14:1-4) Pakali chikhalirebe otsalira a ophunzira otero padziko lapansi. Kodi nchiyani chimene ameneŵa achitiridwa kupititsa patsogolo kukwaniritsidwa kwa pangano la Abrahamu limene Mulungu analumbirira? Munthu amene anali membala woyembekezeredwa wa patsogolo mu Ufumu umenewo, mtumwi Paulo, analemba pa Agalatiya 3:8: “Ndipo malembo, pakuwoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira uthenga wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.”
13 Akristu osankhidwa kuchokera pakati pa amitundu sanafunikire kuyembekezera kufikira kukhazikitsidwa kwa Ufumu mu 1914 kuti alandire dalitso lolonjezedwa, chifukwa chakuti mtumwi Paulo anapitirizabe kunena kuti: “Kotero kuti iwo achikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.” (Agalatiya 3:9) Paulo anali Mkristu ndipo anali kudalitsidwa, choteronso Akristu ena onse obadwa ndi mzimu a m’tsiku lake.a Mofananamo lerolino, otsalira, opangidwa ndi Akristu obadwa ndi mzimu amene amamamatira ku chikhulupiriro mwa Mesiya monga “mbewu” yaikulu ya Abrahamu yodalitsira anthu onse, akusangalala ndi dalitso lolonjezedwa.
14. (a) Kodi ndimotani mmene Akristu odzozedwa adalitsidwira mwapadera mogwirizana ndi pangano la Abrahamu? (b) Kodi zimenezi zalemekeza Yehova m’njira yotani?
14 Mwa kudzipatulira okha kwa Yehova ndi kusonyeza kudzipatulira kumeneku mwa ubatizo wa m’madzi ndiyeno kubadwa ndi mzimu wa Mulungu kuloŵa mu mkhalidwe wauzimu, Akristu ameneŵa afikira kukhala ana auzimu a Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu. Iwo afikiranso kukhala oloŵa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu, Isake Wamkulu. (Aroma 8:17) Ndithudi iwo amadalitsidwa mwapadera mogwirizana ndi pangano la Abrahamu. Yehova wakhala akukwaniritsa zimene analumbira kuchita, mwa kutero kudzitsimikizira monga wolankhula chowonadi, Uyo wokhoza kukwaniritsa mosaphonyetsa zimene amalumbira mwa lumbiro kuchita kaamba ka dzina la iye yekha.
15. Kodi mtumwi Paulo akunena kuti membala aliyense wa otsalira a Akristu obadwa ndi mzimu ali chiyani?
15 Membala aliyense wa otsalira a Akristu obadwa ndi mzimu ali Myuda m’lingaliro lauzimu. Monga momwe mtumwi Paulo adanenera: “Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suuli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mu mtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mu mzimu, si m’malembo ayi.”—Aroma 2:28, 29.
16. Kodi Ayuda auzimu amapanga kagulu kotani konenedweratu pa Zekariya 8:23?
16 ‘M’mapeto a dongosolo la zinthu’ ano, Akristu obadwa ndi mzimu amenewo, amene ali Ayuda chamkati odulidwa m’mitima yawo, amapanga kagulu ka Ayuda kamene kanenedweratu pa Zekariya 8:23, pamene palembedwa kuti: “Atero Yehova wamakamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”
17. (a) Kodi ndani amene akuimiridwa ndi “amuna khumi” amene amafuna kulambira Yehova limodzi ndi otsalira a Ayuda auzimu amakono? (b) Mwa kugwirizana ndi Ayuda auzimu m’kulambira Yehova, kodi mamembala a “nkhosa zina” akusangalala ndi chiyani tsopano?
17 “Anthu” amene “amuna khumi” amenewo afuna kupita nawo kukalambira Yehova Mulungu ndiwo otsalira amakono amene ali Ayuda auzimu, kagulu kamene kamapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wa pa Mateyu 24:45-47. Popeza kuti chiŵerengero cha khumi chimaimira kukwanira kwa zinthu za padziko lapansi, “amuna khumi a manenedwe onse amitundu” akaimira nkhosa zophiphiritsira zonse zonenedweratu pa Mateyu 25:32-46. Ameneŵa ndiwo kagulu ka “nkhosa zina” zimene Yesu adanena kuti akazisonkhanitsira pamodzi ndi otsalira onga nkhosa kupanga limodzi nawo “gulu limodzi” mosamalidwa ndi “mbusa mmodzi,” mwiniyo. (Yohane 10:16) Mwanjira imeneyi iwo amalaŵiratu madalitso a pangano la Abrahamu kudzera mwa “mbewu” ya Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu. Pamenepa, ndithudi, zimene Mulungu analumbirira kuchitira anthu onse zayandikira!
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za dzinalo “Akristu,” mawu amtsinde a Reference Bible pa Machitidwe 11:26 amati: “M’Chihebri, Meshi·chi·yimʹ, ‘Atsatiri a Mesiya.’”
[Chithunzi patsamba 89]
Baibulo lidaneneratu kuti anthu ochokera kumitundu yonse akagwirizana ndi Israyeli wauzimu