Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Masomphenya a Zekariya Akukukhudzani Bwanji?
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | October
    • 16. (a) Kodi kenako Zekariya anaona chiyani? (Onani chithunzi 3.) (b) Kodi akazi awiri okhala ndi mapiko anapita nacho kuti chiwiya chija?

      16 Kenako, Zekariya anaona akazi awiri okhala ndi mapiko amphamvu ooneka ngati a dokowe. (Werengani Zekariya 5:9-11.) Akazi amenewa ndi osiyana kwambiri ndi mkazi amene anatsekeredwa m’chiwiya uja. Iwo ananyamula chiwiya chija mmene munali “Kuipa” n’kuuluka nacho. Kodi anapita nacho kuti? Anapita nacho “kudziko la Sinara” kapena kuti ku Babulo. Koma n’chifukwa chiyani anapita nacho kumeneko?

      17, 18. (a) N’chifukwa chiyani dziko la Sinara linali ‘malo oyenera’ kukhala “Kuipa”? (b) Kodi kuipa tiyenera kukuona bwanji?

      17 Mu nthawi ya Zekariya, Aisiraeli sakanavutika kumvetsa chifukwa chake kuipa anapita nako kudziko la Sinara. Zekariya ndi Ayuda anzake ankadziwa kuti Babulo unali mzinda woipa kwambiri pa nthawiyo. Popeza anakulira mumzindawu womwe anthu ake anali a makhalidwe oipa komanso olambira mafano, tsiku lililonse ankayenera kuyesetsa kuti asatengere makhalidwe oipawo. Masomphenya amenewa ayenera kuti anawakhazika mtima pansi chifukwa anawatsimikizira kuti Yehova sadzalekerera anthu ofuna kuipitsa kulambira koyera.

      18 Komabe masomphenyawa anakumbutsanso Ayuda kuti ayenera kuyesetsa kuti kulambira kwawo kuzikhala koyera nthawi zonse. Anthu a Yehova sayenera kulola kuti zinthu zoipa zilowe m’gulu lawo n’kukhazikika. Yehova watilola kuti tikhale m’gulu lake loyera limene limatisamalira mwachikondi choncho tili ndi udindo woonetsetsa kuti gululi lipitirizebe kukhala loyera. Kodi ifeyo timayesetsa kuchita zimenezi? M’paradaiso wathu wauzimu simuyenera kupezeka kuipa kwa mtundu uliwonse.

  • Kodi Masomphenya a Zekariya Akukukhudzani Bwanji?
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2017 | October
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena