Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Amapereka Mtendere ndi Choonadi Zochuluka
    Nsanja ya Olonda—1996 | January 1
    • “Ndimchitira Nsanje Ziyoni”

      6, 7. Kodi ndi m’njira yotani imene Yehova analili ndi ‘nsanje pa Ziyoni ndi ukali waukulu’?

      6 Mawuwo choyamba akupezeka pa Zekariya 8:2, pamene timaŵerenga kuti: “Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu.” Lonjezo la Yehova la kuchita nsanje, kukhala ndi changu chachikulu pa anthu ake, linatanthauza kuti iye adzakhala maso pobwezeretsa mtendere wawo. Kubwezeretsedwa kwa Israyeli ku dziko lake ndi kumangidwanso kwa kachisi kunali umboni wa changucho.

      7 Komabe, bwanji ponena za awo amene anatsutsa anthu a Yehova? Changu chake pa anthu ake chinali cholingana ndi “ukali [wake] waukulu” pa adani ameneŵa. Pamene Ayuda okhulupirika analambira pakachisi womangidwanso, iwo anatha kukumbukira za tsoka la Babulo wamphamvuyo, amene anali wowonongedwa tsopano. Iwo anali kuganizanso za kulephereratu kwa adani amene anayesa kulepheretsa kumanganso kachisi. (Ezara 4:1-6; 6:3) Ndipo anayamika Yehova kuti anakwaniritsa lonjezo lake. Changu chake chinawapatsa chipambano!

  • Yehova Amapereka Mtendere ndi Choonadi Zochuluka
    Nsanja ya Olonda—1996 | January 1
    • 9. Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani kwa mkhalidwe kumene kunachitikira “Israyeli wa Mulungu” mu 1919?

      9 Pamene kuli kwakuti zilengezo ziŵiri zimenezo zinali zatanthauzo kwa Israyeli wakale, zilinso ndi tanthauzo kwambiri kwa ife pamene zaka za zana la 20 zikufika kumapeto ake. Pafupifupi zaka 80 zapitazo, mkati mwa nkhondo yoyamba yadziko, zikwi zochepa za odzozedwa amene panthaŵiyo anaimira “Israyeli wa Mulungu” zinaloŵa mu ukapolo wauzimu, monga mmene Israyeli wakale analoŵera mu ukapolo ku Babulo. (Agalatiya 6:16) Mu ulosi, iwo ananenedwa kukhala mitembo yogona m’khwalala. Komabe, iwo anali ndi chikhumbo choona mtima cha kulambira Yehova “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Motero, mu 1919, Yehova anawamasula ku ukapolo, kuwautsa ku mkhalidwe wawo wa kufa kwauzimu. (Chivumbulutso 11:7-13) Motero Yehova anayankha ndi Inde womveka funso la Yesaya laulosi lakuti: “Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa?” (Yesaya 66:8) Mu 1919, anthu a Yehova anakhalanso ndi moyo monga mtundu wauzimu mu “dziko” lawo, kapena mkhalidwe wauzimu padziko lapansi.

      10. Kuyambira mu 1919, kodi ndi madalitso otani amene Akristu odzozedwa akhala nawo “m’dziko” lawo?

      10 Pomakhala mosungika m’dzikolo, Akristu odzozedwa anatumikira m’kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova. Iwo anasankhidwa kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” akumavomereza thayo la kusamalira zinthu zapadziko lapansi za Yesu, mwaŵi umene akali nawo pamene zaka za zana la 20 zikuyandikira mapeto ake. (Mateyu 24:45-47) Iwo anaphunziradi bwino kuti Yehova ndiye “Mulungu wa mtendere yekha.”​—1 Atesalonika 5:23.

      11. Kodi ndi motani mmene atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu asonyezera kuti ali adani a anthu a Mulungu?

      11 Bwanji nanga za adani a Israyeli wa Mulungu? Changu cha Yehova pa anthu ake chikulingana ndi ukali wake pa adani awo. M’nkhondo yoyamba yadziko, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anayesayesa kwambiri​—ndipo alephera​—kufafaniza kagulu kakang’ono kameneka ka Akristu olankhula choonadi. M’nkhondo yachiŵiri yadziko, atumiki a Dziko Lachikristu anali ogwirizana pa chinthu chimodzi chokha: Kumbali zonse ziŵiri za nkhondoyo, iwo analimbikitsa maboma kupondereza Mboni za Yehova. Ngakhale lero, atsogoleri achipembedzo m’maiko ambiri akusonkhezera maboma kuchepetsa kapena kuletsa ntchito yachikristu yolalikira ya Mboni za Yehova.

      12, 13. Kodi ukali wa Yehova wasonyezedwa motani pa Dziko Lachikristu?

      12 Yehova waziona zimenezi. Pambuyo pa nkhondo yoyamba yadziko, Dziko Lachikristu, pamodzi ndi mbali yotsalayo ya Babulo Wamkulu, zinagwa. (Chivumbulutso 14:8) Choonadi cha kugwa kwa Dziko Lachikristu chinadziŵika kwa anthu onse kuyambira mu 1922 pamene miliri yophiphiritsira yotsatizana inatsanuliridwa, ikumavumbula poyera mkhalidwe wake wa kufa kwauzimu ndi kulichenjeza za kudza kwa chiwonongeko chake. (Chivumbulutso 8:7–9:21) Monga umboni wakuti kutsanuliridwa kwa miliri imeneyi kukupitirizabe, nkhani yakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ali Pafupi” inaperekedwa padziko lonse pa April 23, 1995, ndiyeno pambuyo pake mamiliyoni mazana a kope lapadera la Uthenga wa Ufumu.

      13 Lerolino, Dziko Lachikristu lili mu mkhalidwe womvetsa chisoni. M’zaka za zana la 20 zonse, anthu ake aphana m’nkhondo zankhanza zodalitsidwa ndi ansembe ndi atumiki ake. M’maiko ena chisonkhezero chake nchochepa kwenikweni. Ilo laikidwira chiwonongeko pamodzi ndi mbali inayo ya Babulo Wamkulu.​—Chivumbulutso 18:21.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena