Yehova Amapereka Mtendere ndi Choonadi Zochuluka
“Ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona.” —YEREMIYA 33:6.
1, 2. (a) Ponena za mtendere, kodi mbiri ya amitundu njotani? (b) Mu 607 B.C.E., kodi ndi phunziro lotani limene Yehova anaphunzitsa Israyeli ponena za mtendere?
MTENDERE! Ndi chinthu chokhumbirika chotani nanga, komabe wakhala wosapezekapezeka chotani nanga m’mbiri ya anthu! Makamaka zaka za zana la 20 sizinakhale zaka za mtendere. M’malo mwake, zaona nkhondo ziŵiri zowononga koposa m’mbiri ya anthu. Pambuyo pa nkhondo yoyamba yadziko, League of Nations inapangidwa kuti isungitse mtendere wa dziko lonse. Bungwe limenelo linalephera. Pambuyo pa nkhondo yachiŵiri yadziko, bungwe la United Nations linakhazikitsidwa ndi cholinga chimodzimodzicho. Tingofunikira kuŵerenga nyuzipepala za tsiku ndi tsiku kuti tione mmene nalonso likulepherera kotheratu.
2 Kodi tiyenera kudabwa kuti mabungwe a anthu satha kubweretsa mtendere? Ayi. Zaka zoposa 2,500 zapitazo, anthu osankhidwa a Mulungu, Aisrayeli, anaphunzirapo kanthu pankhani imeneyi. M’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., mtendere wa Israyeli unasokonezedwa ndi ulamuliro wa dziko lonse, Babulo. Israyeli anayang’ana kwa Igupto kaamba ka mtendere. Igupto analephera. (Yeremiya 37:5-8; Ezekieli 17:11-15) Mu 607 B.C.E., magulu ankhondo a Babulo anagwetsa malinga a Yerusalemu ndi kutentha kachisi wa Yehova. Motero Israyeli anaphunzira mwa njira yovuta za kupanda pake kwa kudalira mabungwe a anthu. M’malo mwa kusangalala ndi mtendere, mtunduwo unatengeredwa kuukapolo ku Babulo.—2 Mbiri 36:17-21.
3. Pokwaniritsa mawu a Yehova kupyolera mwa Yeremiya, kodi ndi zochitika za m’mbiri zotani zimene zinaphunzitsa Israyeli phunziro lina lofunika kwambiri ponena za mtendere?
3 Komabe, Yerusalemu asanagwe, Yehova anali ataulula kuti iye, osati Igupto, adzabweretsa mtendere weniweni pa Israyeli. Kupyolera mwa Yeremiya iye analonjeza kuti: “Ndidzawaululira iwo kuchuruka kwa mtendere ndi zoona. Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israyeli, ndipo ndidzamangitsa mudzi wawo, monga poyamba paja.” (Yeremiya 33:6, 7) Lonjezo la Yehova linayamba kukwaniritsidwa mu 539 B.C.E. pamene Babulo anagonjetsedwa ndipo mtendere unapatsidwa kwa akapolo achiisrayeli. (2 Mbiri 36:22, 23) Pofika chakumapeto kwa 537 B.C.E., kagulu ka Aisrayeli kanachita Phwando la Misasa panthaka ya Israyeli kwa nthaŵi yoyamba pambuyo pa zaka 70! Pambuyo pa phwandolo, iwo anayamba kumanga kachisi wa Yehova. Kodi iwo anamva bwanji ponena za zimenezi? Cholembedwa chimati: “Nafuula anthu onse ndi chi[m]fuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.”—Ezara 3:11.
4. Kodi ndi motani mmene Yehova anasonkhezerera Aisrayeli kuti achite ntchito ya kumanga kachisi, ndipo kodi ndi lonjezo lotani limene anapereka ponena za mtendere?
4 Komabe, pambuyo pa chiyambi chosangalatsa chimenecho, Aisrayeli analefulidwa ndi otsutsa ndipo analeka ntchito ya kumanga kachisi. Patapita zaka zingapo, Yehova anatuma aneneri Hagai ndi Zekariya kuti asonkhezere Aisrayeli kumaliza ntchito ya kumanganso. Zinali zokondweretsa chotani nanga kwa iwo kumva Hagai akunena za kachisi amene adzamangidwanso kuti: “Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m’malo muno ndidzapatsa mtendere”!—Hagai 2:9.
Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake
5. Kodi chapadera nchiyani ponena za chaputala chachisanu ndi chitatu cha Zekariya?
5 M’buku la Baibulo la Zekariya, timaŵerenga za masomphenya ambiri ndi maulosi amene analimbikitsa anthu a Mulungu kalelo mu zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. Maulosi amodzimodziŵa akupitirizabe kutitsimikizira za chichirikizo cha Yehova. Amatipatsa chifukwa chabwino chokhulupirira kuti Yehova adzapatsa anthu ake mtendere m’tsiku lathunso. Mwachitsanzo, m’chaputala cha chisanu ndi chitatu cha buku limene lili ndi dzina lake, mneneri Zekariya kwa nthaŵi khumi akunena mawu akuti: “Atero Yehova.” Nthaŵi iliyonse, mawuŵa atsegulira chilengezo chaumulungu chonena za mtendere wa anthu a Mulungu. Ena a malonjezo ameneŵa anakwaniritsidwa kalelo m’tsiku la Zekariya. Onse akwaniritsidwa kapena ali kukwaniritsidwa lerolino.
“Ndimchitira Nsanje Ziyoni”
6, 7. Kodi ndi m’njira yotani imene Yehova analili ndi ‘nsanje pa Ziyoni ndi ukali waukulu’?
6 Mawuwo choyamba akupezeka pa Zekariya 8:2, pamene timaŵerenga kuti: “Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu.” Lonjezo la Yehova la kuchita nsanje, kukhala ndi changu chachikulu pa anthu ake, linatanthauza kuti iye adzakhala maso pobwezeretsa mtendere wawo. Kubwezeretsedwa kwa Israyeli ku dziko lake ndi kumangidwanso kwa kachisi kunali umboni wa changucho.
7 Komabe, bwanji ponena za awo amene anatsutsa anthu a Yehova? Changu chake pa anthu ake chinali cholingana ndi “ukali [wake] waukulu” pa adani ameneŵa. Pamene Ayuda okhulupirika analambira pakachisi womangidwanso, iwo anatha kukumbukira za tsoka la Babulo wamphamvuyo, amene anali wowonongedwa tsopano. Iwo anali kuganizanso za kulephereratu kwa adani amene anayesa kulepheretsa kumanganso kachisi. (Ezara 4:1-6; 6:3) Ndipo anayamika Yehova kuti anakwaniritsa lonjezo lake. Changu chake chinawapatsa chipambano!
“Mudzi wa Choonadi”
8. M’masiku a Zekariya, kodi ndi motani mmene Yerusalemu anakhalira mudzi wa choonadi mosiyana ndi kale?
8 Nthaŵi yachiŵiri Zekariya akulemba kuti: “Atero Yehova.” Kodi mawu a Yehova tsopano ngotani? “Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, mudzi wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, phiri lopatulika.” (Zekariya 8:3) Chaka cha 607 B.C.E. chisanafike, Yerusalemu sanali mudzi wa choonadi ayi. Ansembe ndi aneneri ake sanali oona mtima, ndipo anthu ake sanali okhulupirika. (Yeremiya 6:13; 7:29-34; 13:23-27) Anthu a Mulungu tsopano anali kumanga kachisi, kusonyeza kudzipereka kwawo pa kulambira koyera. Mumzimu Yehova anali kukhala m’Yerusalemu kachiŵirinso. Choonadi cha kulambira koyera chinali kulankhulidwanso mwa iye, motero Yerusalemu anatchedwa “mudzi wa choonadi.” Malo ake apamwamba anatchedwa “phiri la Yehova.”
9. Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani kwa mkhalidwe kumene kunachitikira “Israyeli wa Mulungu” mu 1919?
9 Pamene kuli kwakuti zilengezo ziŵiri zimenezo zinali zatanthauzo kwa Israyeli wakale, zilinso ndi tanthauzo kwambiri kwa ife pamene zaka za zana la 20 zikufika kumapeto ake. Pafupifupi zaka 80 zapitazo, mkati mwa nkhondo yoyamba yadziko, zikwi zochepa za odzozedwa amene panthaŵiyo anaimira “Israyeli wa Mulungu” zinaloŵa mu ukapolo wauzimu, monga mmene Israyeli wakale analoŵera mu ukapolo ku Babulo. (Agalatiya 6:16) Mu ulosi, iwo ananenedwa kukhala mitembo yogona m’khwalala. Komabe, iwo anali ndi chikhumbo choona mtima cha kulambira Yehova “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Motero, mu 1919, Yehova anawamasula ku ukapolo, kuwautsa ku mkhalidwe wawo wa kufa kwauzimu. (Chivumbulutso 11:7-13) Motero Yehova anayankha ndi Inde womveka funso la Yesaya laulosi lakuti: “Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa?” (Yesaya 66:8) Mu 1919, anthu a Yehova anakhalanso ndi moyo monga mtundu wauzimu mu “dziko” lawo, kapena mkhalidwe wauzimu padziko lapansi.
10. Kuyambira mu 1919, kodi ndi madalitso otani amene Akristu odzozedwa akhala nawo “m’dziko” lawo?
10 Pomakhala mosungika m’dzikolo, Akristu odzozedwa anatumikira m’kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova. Iwo anasankhidwa kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” akumavomereza thayo la kusamalira zinthu zapadziko lapansi za Yesu, mwaŵi umene akali nawo pamene zaka za zana la 20 zikuyandikira mapeto ake. (Mateyu 24:45-47) Iwo anaphunziradi bwino kuti Yehova ndiye “Mulungu wa mtendere yekha.”—1 Atesalonika 5:23.
11. Kodi ndi motani mmene atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu asonyezera kuti ali adani a anthu a Mulungu?
11 Bwanji nanga za adani a Israyeli wa Mulungu? Changu cha Yehova pa anthu ake chikulingana ndi ukali wake pa adani awo. M’nkhondo yoyamba yadziko, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anayesayesa kwambiri—ndipo alephera—kufafaniza kagulu kakang’ono kameneka ka Akristu olankhula choonadi. M’nkhondo yachiŵiri yadziko, atumiki a Dziko Lachikristu anali ogwirizana pa chinthu chimodzi chokha: Kumbali zonse ziŵiri za nkhondoyo, iwo analimbikitsa maboma kupondereza Mboni za Yehova. Ngakhale lero, atsogoleri achipembedzo m’maiko ambiri akusonkhezera maboma kuchepetsa kapena kuletsa ntchito yachikristu yolalikira ya Mboni za Yehova.
12, 13. Kodi ukali wa Yehova wasonyezedwa motani pa Dziko Lachikristu?
12 Yehova waziona zimenezi. Pambuyo pa nkhondo yoyamba yadziko, Dziko Lachikristu, pamodzi ndi mbali yotsalayo ya Babulo Wamkulu, zinagwa. (Chivumbulutso 14:8) Choonadi cha kugwa kwa Dziko Lachikristu chinadziŵika kwa anthu onse kuyambira mu 1922 pamene miliri yophiphiritsira yotsatizana inatsanuliridwa, ikumavumbula poyera mkhalidwe wake wa kufa kwauzimu ndi kulichenjeza za kudza kwa chiwonongeko chake. (Chivumbulutso 8:7–9:21) Monga umboni wakuti kutsanuliridwa kwa miliri imeneyi kukupitirizabe, nkhani yakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ali Pafupi” inaperekedwa padziko lonse pa April 23, 1995, ndiyeno pambuyo pake mamiliyoni mazana a kope lapadera la Uthenga wa Ufumu.
13 Lerolino, Dziko Lachikristu lili mu mkhalidwe womvetsa chisoni. M’zaka za zana la 20 zonse, anthu ake aphana m’nkhondo zankhanza zodalitsidwa ndi ansembe ndi atumiki ake. M’maiko ena chisonkhezero chake nchochepa kwenikweni. Ilo laikidwira chiwonongeko pamodzi ndi mbali inayo ya Babulo Wamkulu.—Chivumbulutso 18:21.
Mtendere wa Anthu a Yehova
14. Kodi ndi chithunzi chaulosi chotani cha anthu ali pamtendere chimene chikuperekedwa?
14 Komabe, chaka chino cha 1996, anthu a Yehova akusangalala ndi mtendere wochuluka m’dziko lawo lobwezeretsedwa, monga momwe kwafotokozedwera m’chilengezo chachitatu cha Yehova kuti: “Atero Yehova wa makamu: M’misewu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m’dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake. Ndi m’misewu ya mudzi mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akuseŵera m’misewu yake.”—Zekariya 8:4, 5.
15. Mosasamala kanthu za nkhondo za amitundu, kodi ndi mtendere wotani umene atumiki a Yehova asangalala nawo?
15 Chithunzi chabwino kwambiri choperekedwa ndi mawuŵa chikusonyeza kanthu kena kapadera m’dziko lino losakazidwa ndi nkhondo—anthu okhala pamtendere. Kuyambira mu 1919, mawu aulosi a Yesaya akwaniritsidwa: “Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye. Koma . . . palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.” (Yesaya 57:19-21) Inde, anthu a Yehova, pamene kuli kwakuti saali mbali ya dziko, sangapeŵe kukhudzidwa ndi chipoloŵe cha amitundu. (Yohane 17:15, 16) M’maiko ena, iwo amapirira mavuto aakulu, ndipo angapo aphedwa. Komabe, Akristu enieni ali ndi mtendere m’njira zazikulu ziŵiri. Yoyamba, ali ndi “mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye [wawo] Yesu Kristu.” (Aroma 5:1) Yachiŵiri, ali ndi mtendere pakati pawo. Iwo amakulitsa “nzeru yochokera kumwamba,” imene “iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere.” (Yakobo 3:17; Agalatiya 5:22-24) Ndiponso, iwo amayembekezera kudzasangalala ndi mtendere m’lingaliro lake lonse pamene “ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
16, 17. (a) Kodi “amuna ndi akazi okalamba” limodzinso ndi “ana aamuna ndi aakazi” alimbitsidwa motani ndi gulu la Yehova? (b) Kodi mtendere wa anthu a Yehova umasonyezedwa ndi chiyani?
16 Pakali “amuna ndi akazi okalamba” pakati pa anthu a Yehova, odzozedwa amene amakumbukira zipambano zakale za gulu la Yehova. Chikhulupiriro chawo ndi chipiriro chawo zimayamikiridwa kwambiri. Odzozedwa ocheperapo msinkhu anatsogolera m’masiku ovuta a m’ma 1930, ndi m’Nkhondo Yadziko II ndi m’zaka zosangalatsa za kupita patsogolo zimene zinatsatira. Ndiponso, makamaka chiyambire 1935, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” laonekera. (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Pamene Akristu odzozedwa akalamba ndi kuchepa, nkhosa zina zapitiriza ntchito ya kulalikira ndi kuifutukula padziko lonse lapansi. M’zaka zaposachedwapa, nkhosa zina zaloŵa mwaunyinji m’dziko la anthu a Mulungu. Eya, chaka chatha chokha, 338,491 anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova! Atsopano ameneŵa ngochepa msinkhu kwambiri, mlingaliro lauzimu. Mphamvu zawo ndi changu chawo nzofunikadi pamene awonjezera chiŵerengero cha awo amene aimba zitamando zachiyamiko “kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chivumbulutso 7:10.
17 Lerolino, ‘m’misewu ya mudzi muli ana aamuna ndi aakazi,’ Mboni zokhala ndi nyonga yaachichepere. M’chaka chautumiki cha 1995, maiko ndi zisumbu za m’nyanja 232 anatumiza malipoti awo. Koma panalibe udani wa m’maiko osiyanasiyana, panalibe udani wautundu, palibe nsanje yopanda pake, pakati pa odzozedwa ndi nkhosa zina. Onse amakulira pamodzi mwauzimu, ogwirizana m’chikondi. Ubale wa dziko lonse wa Mboni za Yehova ngwapaderadi padziko.—Akolose 3:14; 1 Petro 2:17.
Kodi Nchovuta Kwambiri kwa Yehova?
18, 19. M’zaka zonse kuyambira mu 1919, kodi Yehova wakwaniritsa motani zimene kwa munthu zingakhale zitaoneka zovuta kwambiri?
18 Kalelo mu 1918 pamene otsalira a odzozedwa anali chabe anthu olefulidwa zikwi zochepa okhala muukapolo wauzimu, palibe akanaoneratu zimene zidzachitika. Ngakhale zili choncho, Yehova anadziŵa—monga momwe chilengezo chake chaulosi chachinayi chikusonyezera kuti: “Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa [“chovuta kwambiri,” NW] pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa [“chovuta kwambiri,”] pamaso panga? ati Yehova wa makamu.”—Zekariya 8:6.
19 Mu 1919, mzimu wa Yehova unapatsanso mphamvu anthu ake kuwakonzekeretsa ntchito imene inali mtsogolo. Komabe, panafunika chikhulupiriro kumamatira ku kagulu ka alambiri a Yehova. Iwo anali ochepa kwenikweni, ndipo zinthu zambiri sizinali zomveketsedwa bwino. Komabe, pang’onopang’ono Yehova anawalimbitsa monga gulu ndi kuwakonzekeretsa kuchita ntchito yachikristu ya kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Yesaya 60:17, 19; Mateyu 24:14; 28:19, 20) M’kupita kwa nthaŵi, anawathandiza kuzindikira nkhani zazikulu zonga ngati kusatenga mbali m’zandale ndi ulamuliro wa chilengedwe chonse. Kodi zinali zovuta kwambiri kwa Yehova kukwaniritsa chifuniro chake mwa kagulu kameneko ka Mboni? Mosakayikira yankho nlakuti ayi! Zimenezi zasonyezedwa pamasamba 12 mpaka 15 a magazini ano, amene akusonyeza tchati cha zochita za Mboni za Yehova m’chaka chautumiki cha 1995.
“Ndidzakhala Mulungu Wawo”
20. Kodi kusonkhanitsa anthu a Mulungu kunaloseredwa kuti kudzakhala kwakukulu motani?
20 Chilengezo chachisanu chikusonyezanso mkhalidwe wachimwemwe wa Mboni za Yehova lerolino pamene chimati: “Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m’dziko lakummaŵa, ndi m’dziko lakumadzulo; ndipo ndidzabwera nawo, nadzakhala mkati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenso ndidzakhala Mulungu wawo, m’choonadi ndi m’chilungamo.”—Zekariya 8:7, 8.
21. Kodi mtendere wochuluka wa anthu a Yehova wasungidwa ndi kufutukulidwa motani?
21 Mu 1996 tinganene mosakayikira kuti uthenga wabwino walalikidwa kuzungulira dziko lonse, kuchokera ku “dziko la kummaŵa,” mpaka ku “dziko la kumadzulo.” Ophunzira apangidwa mwa anthu a m’mitundu yonse, ndipo aona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Tili ndi mtendere chifukwa tikuphunzitsidwa ndi Yehova. Chifukwa cha zimenezi, mabuku akufalitsidwa m’zinenero zoposa pa 300. Chaka chatha chokha, panawonjezeka zinenero 21. Magazini a Nsanja ya Olonda tsopano akufalitsidwa pamodzi ndi Chingelezi m’zinenero 111, ndi Galamukani! m’zinenero 54. Misonkhano ya m’dziko lililonse ndi ya mitundu yonse imapereka umboni wapoyera wa mtendere wa anthu a Mulungu. Misonkhano ya mlungu ndi mlungu imatigwirizanitsa ndi kutipatsa chilimbikitso chimene timafunikira kuti tikhale olimba. (Ahebri 10:23-25) Inde, Yehova akuphunzitsa anthu ake “m’choonadi ndi m’chilungamo.” Iye akupatsa anthu ake mtendere. Ndife odala chotani nanga kukhalako ndi mtendere wochuluka umenewo!
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi ndi motani mmene Yehova wakhalira ‘wansanje ndi waukali waukulu’ pa anthu ake m’nthaŵi zamakono?
◻ Kodi anthu a Yehova amasangalala motani ndi mtendere, ngakhale m’maiko osakazidwa ndi nkhondo?
◻ Kodi ndi motani mmene ‘misewu ya mudzi yakhalira ndi ana aamuna ndi aakazi’?
◻ Kodi ndi makonzedwe otani amene apangidwa kotero kuti anthu a Yehova aphunzitsidwe ndi iye?
[Tchati pamasamba 12-15]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1995 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Mu zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., Ayuda okhulupirika amene anamanganso kachisi anaphunzira kuti Yehova ndiye magwero okha odalirika a mtendere