-
Ambuye Wowona Adza Kaamba ka ChiweruzoNsanja ya Olonda—1989 | July 1
-
-
Yehova samawona mopepuka awo osasonyeza ulemu kaamba ka kakonzedwe ka ukwati. Mosiyana ndi lamulo la Mulungu, amuna a ku Yuda adzitengera akazi achilendo. (Deuteronomo 7:3, 4) Iwo achita mwachinyengo ndi akazi a uchichepere wawo mwa kuwasudzula iwo. Yehova “adana nako kulekana,” Malaki akuchenjeza tero.—2:10-17.
-
-
Ambuye Wowona Adza Kaamba ka ChiweruzoNsanja ya Olonda—1989 | July 1
-
-
○ 2:13—Amuna ambiri a Chiyuda anali kusudzula akazi a uchichepere wawo, mwinamwake kuti akwatire akazi akunja achichepere. Guwa la Yehova linaphimbidwa ndi misozi—mwachiwonekere ija ya akazi okanidwa omwe anabwera ku malo oyera kutsanula chisoni chawo pamaso pa Mulungu.—Malaki 2:11, 14, 16.
-