PHUNZIRO 59
N’zotheka Kupirira Ena Akamakuzunzani
Anthu akhoza kuyamba kutizunza kapena kutitsutsa ndi cholinga choti tisiye kutumikira Yehova. Koma kodi zimenezi ziyenera kutidabwitsa?
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kuti anthu akhoza kuyamba kutizunza?
Baibulo limanena kuti: “Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Timoteyo 3:12) Yesu anazunzidwa chifukwa sanali mbali ya dziko la Satanali. Nafenso sitili mbali ya dzikoli, choncho sitimadabwa maboma komanso zipembedzo za m’dzikoli zikamatizunza.—Yohane 15:18, 19.
2. Kodi tingachite chiyani pokonzekera chizunzo?
Tiyenera kuyamba panopa kudalira kwambiri Yehova. Tsiku lililonse tizipeza nthawi yopemphera kwa iye komanso kuwerenga Mawu ake. Tiyeneranso kumachita nawo misonkhano yampingo nthawi zonse. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kuti musamafooke mukamakumana ndi mayesero ngakhale ochokera kwa anthu am’banja mwanu. Mtumwi Paulo yemwenso nthawi zambiri ankazunzidwa analemba kuti: “Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.”—Aheberi 13:6.
Tikamagwira ntchito yolalikira nthawi zonse zimatithandiza kukhala olimba mtima. Kulalikira kumatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova komanso kuti tisamaope anthu. (Miyambo 29:25) Mukamalalikira molimba mtima panopa, simudzavutika kupitiriza kulalikira ngakhale boma litaletsa ntchito yathu.—1 Atesalonika 2:2.
3. Kodi kupirira tikamazunzidwa kuli ndi ubwino wotani?
N’zoona kuti sitimasangalala tikamazunzidwa. Komabe, tikamapirira pozunzidwa chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri. Timakhala pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova chifukwa pa nthawi imene tikuona kuti sitingakwanitse kupirira, m’pamene iye amatithandiza. (Werengani Yakobo 1:2-4.) Yehova akamaona kuti tikuzunzidwa, zimamupweteka kwambiri. Koma iye amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kupirira. Baibulo limati: “Mulungu amasangalala mukamapirira mavuto chifukwa choti mukuchita zabwino.” (1 Petulo 2:20) Tikapitiriza kukhala okhulupirika anthu ena akamatizunza, Yehova adzatidalitsa potipatsa moyo wosatha m’dziko lomwe simudzakhala anthu otitsutsa.—Mateyu 24:13.
FUFUZANI MOZAMA
Onani chifukwa chake n’zotheka kupirira ena akamatizunza komanso mmene Yehova adzatidalitsire tikapitiriza kukhala okhulupirika.
4. N’zotheka kupirira mukamatsutsidwa ndi achibale anu
Yesu ankadziwa bwino kuti achibale athu ena sangagwirizane ndi zimene tasankha zoti tizilambira Yehova. Werengani Mateyu 10:34-36, kenako mukambirane funso ili:
Mogwirizana ndi lembali, kodi achibale athu angachite chiyani tikasankha kutumikira Yehova?
Kuti muone chitsanzo cha zimenezi, onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi mungatani ngati wachibale kapena mnzanu akufuna kuti musiye kutumikira Yehova?
Werengani Salimo 27:10 ndi Maliko 10:29, 30. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi lonjezoli lingakuthandizeni bwanji achibale kapena anzanu akamakutsutsani?
5. Musasiye kutumikira Yehova mukamazunzidwa
Timafunika kulimba mtima kuti tipitirize kutumikira Yehova anthu ena akamatizunza. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi zitsanzo zamuvidiyoyi zakulimbikitsani bwanji?
Werengani Machitidwe 5:27-29 ndi Aheberi 10:24, 25. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kulambira Yehova ngakhale boma litatiletsa kusonkhana kapena kugwira ntchito yathu yolalikira?
6. Yehova adzakuthandizani kuti mukwanitse kupirira
A Mboni za Yehova amisinkhu yosiyanasiyana padziko lonse amapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale akuzunzidwa. Kuti muone zimene zimawathandiza kupirira, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane funso ili:
Muvidiyoyi, n’chiyani chinathandiza abale ndi alongowa kuti akwanitse kupirira?
Werengani Aroma 8:35, 37-39 ndi Afilipi 4:13. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi lembali likusonyeza bwanji kuti n’zotheka kupirira mukamakumana ndi mayesero ena alionse?
Werengani Mateyu 5:10-12, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani mukhoza kumasangalalabe pamene mukuzunzidwa?
A Mboni za Yehova ambirimbiri sanasiye kutumikira Yehova ngakhale pamene ankazunzidwa. Nanunso mungakwanitse
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Sindingakwanitse kupirira ena akamandizunza.”
Kodi ndi malemba ati amene angathandize munthu wotereyu kuti akhale wolimba mtima?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova amayamikira khama lomwe timasonyeza pomutumikira ngakhale ena akutizunza. Iye adzatipatsa mphamvu zomwe zingatithandize kupirira.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuyembekezera kuzunzidwa?
Kodi muyenera kuchita chiyani panopa pokonzekera chizunzo?
N’chiyani chingakuthandizeni kuti musamakayikire kuti mukhoza kumatumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale mukukumana ndi mayesero?
ONANI ZINANSO
Onani mmene Yehova anathandizira m’bale wina kupirira atakana kulowerera ndale.
Onani chimene chinathandiza anthu am’banja lina kuti azitumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri ngakhale kuti ankazunzidwa.
Anatumikira Yehova Panthawi Imene Zinthu Zinali Zitasintha (7:11)
Onani zimene mungachite kuti muzichita zinthu molimba mtima mukamazunzidwa.
“Tizikonzekera Kuti Tidzathe Kupirira Pozunzidwa” (Nsanja ya Olonda, July 2019)
Kodi tizitani ngati achibale athu akutitsutsa? Nanga tingatani kuti tizichitabe zinthu mwamtendere komanso kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova?
“Choonadi Sichibweretsa ‘Mtendere Koma Lupanga’” (Nsanja ya Olonda, October 2017)