Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 3/15 tsamba 12-13
  • Kuphunzitsa ndi Mafanizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzitsa ndi Mafanizo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Kuphunzitsa mwa Mafanizo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mafanizo Ofotokoza za Ufumu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kupindula Kuchokera ku Mafanizo a Yesu
    Nsanja ya Olonda—1987
  • ‘Mulungu Ndi Amene Amakulitsa’!
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 3/15 tsamba 12-13

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kuphunzitsa ndi Mafanizo

YESU mwachiwonekere ali ku Kapernao pamene akudzudzula Afarisi. Pambuyo pa tsiku limenelo iye akuchoka kunyumbako ndi kuyenda kufupi ndi Nyanja ya Galileya, kumene makamu a anthu asonkhana. Kumeneko iye akwera ngalawa, ndi kuchoka, ndikuyamba kuphunzitsa anthu am’mphepete mwa nyanja ponena za Ufumu wa kumwamba. lye akuchita choncho mwa njira ya ndandanda ya zoweruzirapo, kapena mafanizo, chiri chonse chokhala ndi makhazikitsidwe ozolowereka kwa anthuwo.

Poyambirira, Yesu akukamba za wofesa yemwe anafesa mbewu. Mbewu zina zinagwa m’mphepete mwa msewu ndipo zinadyedwa ndi mbalame. Mbewu zina zinagwa pa nthaka ya thanthwe. Popeza mizuyo sinazike, mbewu zomera kumenezo zifota pansi pa kutentha kwa dzuwa. Komabe zina zinagwa pakati pa minga, yomwe inatsamwitsa mbewuzo pamene zinamera. Pomalizira, mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala kuwirikiza zana, zina kuwirikiza makumi asanu ndi limodzi, ndipo zina makumi atatu.

Mu fanizo lina, Yesu ananena kuti Ufumu wa Mulungu uli monga pamene munthu afesa mbewu. Pamene masiku apita, pamene munthu agona ndi kudzuka, mbewu zimera. Munthuyo sadziwa ndi motani. Zimamera mwa izo zokha ndi kubala zipatso. Pamene mbewuzo zikhwima, munthuyo amazikolola izo.

Yesu apereka fanizo lachitatu ponena za munthu yemwe anafesa mbewu yabwino; koma pamene iye anali mtulo, mdani wake akudza nafesa namsongole pakati pa tirigu. Antchito a munthuyo anafunsa ngati anayenera kumuzula namsongole. Koma iye akuyankha: ‘Ayi, kuti kapena m’mene mukasonkhanitsa namsongoleyo mungazulenso tirigu pamodzi naye. Tazilekani zonse ziwiri zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo mnyengo ya kututa ndidzauza akututawo, muyambe kusonkhanitsa namsongole mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m’nkhokwe yanga.’

Kupitiriza nkhani yake kwa khamulo pa gombe, Yesu anapereka mafaniziro owonjezera awiri. lye akulongosola kuti “Ufumu wa kumwamba” uli wofanana ndi mbewu ya mpiru yomwe munthu amafesa. Angakhale kuti iyo iri mbewu yaing’ono kwambiri ya mbewu zonse, iye akuti, iyo imakula kukhala yaikulu kwambiri pa ndiwo za masamba zonse. Iyo imakhala mtengo kumene mbalame zimafika, kumapeza mthunzi pakati pa nthambi zake.

Ena lerolino amatsutsa kuti pali mbewu zina zache zimene ziri zocheperapo kuposa mbewu ya mpiru. Koma Yesu pano sakupereka phunziro la mitengo. Pa mbewu zimene anthu a ku Galileya anali ozolowerana nazo, mbewu ya mpiru inalidi mbewu yaing’ono kwambiri. Chotero iwo anayamikira nkhani ya kukula kowonekera kumene Yesu anali kuchitira chitsanzo.

Pomalizira, Yesu akuyerekeza “Ufumu wa kumwamba” ndi chotupitsa chimene mkazi amatenga ndi kusanganiza ku miyezo itatu yaufa. Mkupita kwa nthawi iye akuti, chimalowerera mu mbali zonse za ufa. Pambuyo pa kupereka mafaniziro asanu amenewa, Yesu akulibalalitsa khamu ndi kubwerera ku nyumba imene iye akukhala. Mwamsanga atumwi ake 12 ndi ena abwera kwa iye kumeneko. Mateyu 13:1-9, 24-36; Marko4:1-9, 26-32; Luka 8:1-8.

◆ Ndiliti ndipo ndikuti kumene Yesu akulankhula ndi zifaniziro kwa makamu?

◆ Ndi zifaniziro zisanu ziti zimene Yesu anauuza khamulo?

◆ Kodi ndi chifukwa ninji Yesu ananena kuti mbewu ya mpiru iri mbewu yaing’ono kwambiri ya mbewu zonse?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena