-
Simudziwa Zimene ZidzalolaNsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
Fanizo la Chofufumitsa
9, 10. (a) Kodi Yesu anatsindika mfundo yotani m’fanizo la chofufumitsa? (b) Kodi chofufumitsa nthawi zambiri chimaimira chiyani m’Baibulo, ndipo tikambirana funso lotani lokhudza mmene Yesu anagwiritsira ntchito chofufumitsa?
9 Si nthawi zonse pamene kukula kumaoneka ndi maso. Yesu anatsindika mfundo imeneyi m’fanizo lake lina. Iye anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati zofufumitsa, zimene mkazi anazitenga ndi kuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zopimira, ndipo wonsewo unafufuma.” (Mat. 13:33) Kodi chofufumitsa chimenechi chikuimira chiyani, ndipo chikugwirizana bwanji ndi kukula kwa Ufumu?
10 M’Baibulo, chofufumitsa nthawi zambiri chimaimira uchimo. Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chofufumitsa mwa njira imeneyi pamene ananena za munthu wochimwa amene anali kuipitsa mpingo wa ku Korinto. (1 Akor. 5:6-8) Ndiyeno kodi apa Yesu anagwiritsa ntchito chofufumitsa kuimira kukula kwa chinthu choipa?
11. Kodi kale Aisiraeli ankagwiritsa ntchito chofufumitsa motani?
11 Tisanayankhe funso limeneli, tifunikira kukumbukira mfundo zofunika zitatu. Yoyamba, ngakhale kuti Yehova sanalole chofufumitsa paphwando la Pasika, nthawi zina anali kulandira nsembe zokhala ndi chofufumitsa. Chofufumitsa chinkagwiritsidwa ntchito pansembe zoyamika za chiyanjano. Munthu ankapereka nsembe zimenezi mwaufulu poyamikira Yehova chifukwa cha madalitso ake ambiri. Akadya chakudyachi anali kusangalala kwambiri.—Lev. 7:11-15.
12. Kodi tikuphunzira chiyani ndi mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mafanizo?
12 Mfundo yachiwiri ndi yakuti, ngakhale kuti nthawi ina chinthu china m’Malemba chingaimire chinthu choipa, panthawi ina chinthu chomwecho chingagwiritsidwe ntchito kuimira chinthu chabwino. Mwachitsanzo pa 1 Petulo 5:8, Satana akuyerekezeredwa ndi mkango, posonyeza kuopsa ndi kulusa kwake. Koma pa Chivumbulutso 5:5, Yesunso akuyerekezeredwa ndi mkango, pomutchula kuti “Mkango wa fuko la Yuda.” Pamenepa, agwiritsa ntchito mkango kuimira kulimba mtima pochita chilungamo.
13. Kodi fanizo la Yesu la chofufumitsa likusonyeza chiyani za kukula kwauzimu?
13 Mfundo yachitatu ndi yakuti, m’fanizo lake, Yesu sananene kuti chofufumitsa chinaipitsa ufawo, n’kukhala wosatheka kuugwiritsa ntchito. M’malomwake, iye anangonena zimene zimachitika popanga mkate. Mkaziyo anachita kuikamo chofufumitsa, ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Chofufumitsa chinasakanizidwa, kapena kuti chinabisidwa mu ufa. Chotero, njira imene chofufumitsacho chinali kugwirira ntchito inali yobisika kwa mkaziyo. Zimenezi zikutikumbutsa za munthu uja amene amafesa mbewu ndi kugona usiku. Yesu ananena kuti: “Mbewuzo zimamera ndi kukula. Koma kwenikweni mmene zimenezi zimachitikira, [munthuyo] sadziwa ayi.” (Maliko 4:27) Imeneyitu ndi njira yosavuta yofanizira mmene kukula kwauzimu kumachitikira mosaoneka. Poyamba sitingaone kukulako, koma m’kupita kwa nthawi zotsatira zake zimayamba kuonekera.
14. Kodi ndi mbali iti ya ntchito yolalikira imene ikusonyezedwa ndi mfundo yakuti chofufumitsa chikufufumitsa ufa wonse?
14 Kuwonjezera pa mfundo yakuti kukula sikuoneka ndi maso, kukulako kumafalikira paliponse. Fanizo la chofufumitsa likutsindikanso mbali imeneyi. Chofufumitsacho chikufufumitsa ufa wonsewo, “wokwana mbale zopimira zazikulu zitatu.” (Luka 13:21) Mofanana ndi chofufumitsa, ntchito yolalikira Ufumu imene yachititsa kukula kwauzimu kumeneku yafalikira paliponse, motero kuti Ufumuwo ukulalikidwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Mat. 24:14) Ndi mwayi wapadera kwambiri kuthandiza nawo kuti ntchito ya Ufumu ifalikire mochititsa chidwi chonchi.
-
-
Simudziwa Zimene ZidzalolaNsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
20, 21. (a) Kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mafanizo a Yesu okhudza kukula? (b) Kodi inu mukufunitsitsa kuchita chiyani?
20 Ndiyeno, kodi taphunzira chiyani pambuyo pokambirana mwachidule mafanizo a Yesu okhudza kukula? Choyamba, mofanana ndi kukula kwa kambewu ka mpiru, zinthu za Ufumu zakula modabwitsa kwambiri padziko lapansi. Palibe chimene chingaletse ntchito ya Yehova kufalikira. (Yes. 54:17) Ndiponso, chitetezo chauzimu chaperekedwa kwa anthu amene ‘apeza malo okhala mu mthunzi [wa mtengowo].’ Chachiwiri, Mulungu ndi amene amakulitsa. Mofanana ndi mmene chofufumitsa chobisika chimafufumitsira ufa wonse, kukula kumeneku kwakhala kovuta kukuzindikira kapena kukumvetsa, koma kukulako kukuchitika ndithu. Chachitatu, sikuti anthu onse amene analabadira asonyeza kuti ndi nsomba zofunika. Ena akhala ngati nsomba zosafunika za m’fanizo la Yesu.
-