-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
5. Mu fanizo la Yesu, kodi mdani akuimira ndani, nanga namsongole akuimira ndani?
5 Kodi mdani akuimira ndani, ndipo namsongole akuimira ndani? Yesu ananena kuti mdaniyo “ndi Mdyerekezi.” Ndipo anati namsongole ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:25, 38, 39) Namsongole amene Yesu ankanena, ndi mtundu wa udzu woipa kwambiri umene ukakhala waung’ono umafanana kwambiri ndi tirigu. Ilitu ndi fanizo labwino kwambiri pofotokoza za anthu amene amanamizira kuti ndi ana a Ufumu koma sabala zipatso zabwino. Akhristu onyenga amenewa, amanamizira kuti ndi otsatira Khristu koma zoona zake n’zakuti iwo ndi mbali ya “mbewu” ya Satana Mdyerekezi.—Gen. 3:15.
-
-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
7. Kodi tirigu wina anasintha n’kukhala namsongole? Fotokozani.
7 Yesu sananene kuti tirigu adzasintha n’kukhala namsongole koma anati namsongole anafesedwa m’munda wa tirigu. Choncho fanizoli silikunena za Akhristu oona amene agwa m’choonadi. Koma likunena za zimene Satana wachita n’cholinga chofuna kuipitsa mpingo wachikhristu mwa kulowetsa anthu oipa mumpingomo. Panthawi imene mtumwi Yohane anali wokalamba, mpatuko umenewo n’kuti utayamba kale kuonekera.—2 Pet. 2:1-3; 1 Yoh. 2:18.
-
-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
Nyengo Yokolola Imene Anthu Ankaiyembekezera
10, 11. (a) Kodi nthawi yokolola ndi iti? (b) Kodi tirigu wophiphiritsayu akusonkhanitsidwa bwanji munkhokwe ya Yehova?
10 Yesu ananena kuti: “Nthawi yokolola ndi mapeto a dongosolo lino la zinthu, ndipo okololawo ndi angelo.” (Mat. 13:39) M’masiku otsiriza ano a dongosolo lino la zinthu, ntchito yosiyanitsa anthu ikuchitika. Ana a Ufumu akusonkhanitsidwa ndipo akusiyanitsidwa ndi anthu omwe ali ngati namsongole. Pa nkhani imeneyi, mtumwi Petulo ananena kuti: “Ino ndiyo nthawi yoikika yakuti chiweruzo chiyambe, ndipo chiyambira pa nyumba ya Mulungu. Tsopano ngati chiyambira pa ife, ndiye mapeto a anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu adzakhala otani?”—1 Pet. 4:17.
11 Masiku otsiriza kapena kuti “mapeto a dongosolo lino la zinthu” atangoyamba, chiweruzo chinayamba pa anthu amene ankati ndi Akhristu oona, kuti zidziwike ngati alidi “ana a Ufumu” kapena “ana a woipayo.” Kumayambiriro kwa nyengo yokolola, Babulo wamkulu anagwa ndipo kenako ana a Ufumu anasonkhanitsidwa. (Mat. 13:30) Koma kodi tirigu wophiphiritsayu akusonkhanitsidwa bwanji munkhokwe ya Yehova? Ena mwa anthu amenewa, akusonkhanitsidwa mumpingo wachikhristu ndipo amayanjidwa ndiponso kutetezedwa ndi Mulungu. Ena akulandira mphoto yawo kumwamba.
12. Kodi kukolola kuchitika kwa nthawi yaitali bwanji?
12 Kodi chiweruzo chichitika kwa nthawi yaitali bwanji? Mawu akuti “nyengo” amene Yesu anagwiritsa ntchito ponena za kukolola, akusonyeza kuti ndi nthawi yaitali ndithu. (Chiv. 14:15, 16) Kuweruza munthu aliyense amene ali m’gulu la odzozedwa kukupitirirabe nthawi yonse yamapeto. Kudzatha pa nthawi imene odzozedwa onse adzasindikizidwa chizindikiro.—Chiv. 7:1-4.
-