Tili ndi Chuma Chamtengo Wapatali Chofunika Kugawira Ena
1 Mawu a Mulungu ali ndi chuma chauzimu chochuluka ndipo timachikonda kwambiri. (Sal. 12:6; 119:11, 14) Panthawi ina, Yesu atapereka mafanizo osonyeza mbali zosiyanasiyana za Ufumu, anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi mukuzindikira tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo atavomera, iye anawauza kuti: “Popeza kuti zili choncho, mphunzitsi aliyense wa anthu, akaphunzitsidwa za ufumu wa kumwamba, amakhala ngati munthu, mwini nyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.”—Mat. 13:1-52.
2 Mfundo za m’Baibulo zimene tinazidziwa titangoyamba kuphunzira, zili ngati chuma chakale. Ndipo tikamapitiriza kuphunzira patokha zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu, timapezanso mfundo zina za m’Baibulo zimene kwa ife zimakhala chuma chatsopano. (1 Akor. 2:7) Kenako mothandizidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” timayamba kumvetsa bwino chuma chatsopanocho.—Mat. 24:45.
3 Ife timayamikira kwambiri chuma chauzimu chakale ndi chatsopano chimenechi. Chifukwa cha mtima woyamikira umenewu, timafuna kuphunzitsidwa kuti tikhale ndi luso monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu, ndipo timauzako ena mosaumira mfundo zamtengo wapatali zimene taphunzira.
4 Phunzirani kwa Yesu: Posonyeza kuti iye ankakonda chuma chimenechi, Yesu analimbikira kwambiri kugawira ena chumacho. Ngakhale kuti nthawi zina ankatopa, iye sanasiye kutulutsa chuma “m’nkhokwe” yake.—Yoh. 4:6-14.
5 Chikondi chimene Yesu anali nacho pa anthu osowa mwauzimu, chinamupangitsa kuwagawira chuma chopatsa moyo cha mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Sal. 72:13) Iye anamvera chifundo anthu amene anali ndi njala yauzimu ndipo ‘anawaphunzitsa zinthu zambiri.’—Maliko 6:34.
6 Tsanzirani Yesu: Ngati timayamikira kwambiri chuma chimene tili nacho, ifenso mofanana ndi Yesu, tidzayesetsa kusonyeza anthu chuma chauzimu chimene chili m’Baibulo. (Miy. 2:1-5) Ngakhale kuti nthawi zina tingatope, tidzauzabe ena mfundo za m’Malemba ndi mtima wathu wonse. (Maliko 6:34) Chifukwa choyamikira kwambiri chuma chimenechi, tidzachita chilichonse chimene tingathe muutumiki ndipo nthawi zonse tidzayesetsa kuchita zambiri.