CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 4-5
Zimene Tikuphunzira pa Zomwe Yesu Anaphunzitsa pa Ulaliki Wapaphiri
Kodi mumazindikira zosowa zanu zauzimu?
Mawu akuti “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” kwenikweni amatanthauza “anthu amene amapempha mzimu.” (Mat. 5:3) Tingasonyeze kuti tikufuna kuti Mulungu azititsogolera ndi mzimu wake ngati . . .
timawerenga Baibulo tsiku ndi tsiku
timakonzekera komanso kupezeka pamisonkhano
timawerenga mabuku athu, komanso ngati n’zotheka, zinthu zosiyanasiyana zopezeka pawebusaiti yathu
timaonera pulogalamu ya JW Broadcasting ya mwezi uliwonse
Kodi ndingatani kuti nthawi zonse ndizikonda kuphunzira Mawu a Mulungu?