Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • 3 Yesu anamva kufuula kwawo ngakhale kuti gulu la anthulo linkasokosa kwambiri. Ndiye kodi iye anatani? Pa nthawiyi, anali ndi zinthu zambiri zimene zinkamudetsa nkhawa mumtima mwake. Panali patangotsala mlungu umodzi wokha kuti aphedwe ndipo ankadziwa kuti posachedwa, azunzidwa komanso kuphedwa mwankhanza ku Yerusalemu. Komabe, iye sananyalanyaze anthu osaona omwe ankafuulawo. Choncho, iye anaima n’kulamula kuti anthu osaonawo awabweretse kwa iye. Iwo anamupempha kuti: “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona.” Yesu “atagwidwa ndi chifundo,” anagwira maso awo ndipo anayamba kuona.a Nthawi yomweyo, iwo anayamba kumutsatira.​—Luka 18:35-43; Mateyu 20:29-34.

  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • a Anthu ena amati mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “atagwidwa ndi chifundo,” ndi ena mwa mawu amphamvu kwambiri m’Chigiriki osonyeza kumvera ena chisoni. Buku lina limati mawu amenewa “samangosonyeza kumva chisoni kokha ukaona anthu amene akuvutika, koma amatanthauzanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuwathandiza komanso kuthetsa mavuto awo.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena