Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 8/8 tsamba 12-13
  • Kodi Akristu Ayenera Kugwiritsira Ntchito Maina Aulemu Achipembedzo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akristu Ayenera Kugwiritsira Ntchito Maina Aulemu Achipembedzo?
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Levulendi,” “Bishopu,” ndi “Kadinala”
  • “Ambuye,” “Amonsinyolo,” ndi “Abambo”
  • Kulakwa kwa Chipembedzo
  • Choonadi Chonena za Mulungu Komanso Khristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • “Yesu Kristu Ndiye Ambuye”—Motani Ndipo Liti?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Ndi Bwino Kugwiritsa Ntchito Mayina Aulemu?
    Galamukani!—2008
  • Kodi N’zoona Kuti Petulo Anali Papa Woyamba?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 8/8 tsamba 12-13

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Ayenera Kugwiritsira Ntchito Maina Aulemu Achipembedzo?

ZAMBIRI zikunenedwa ponena za kupereŵera kwa atsogoleri achipembedzo m’Chikristu Chadziko lerolino, koma palibe kupereŵera kwa maina aulemu achipembedzo pakati pawo. Maina ena aulemu ngosavuta; ena ngodziwonetsera chabe. Nazi zitsanzo zochepa:

Mtsogoleri wachipembedzo: “Levulendi.”

Bishopu wa Angilikani: “Levulendi Woyenera Ambuye Bishopu.”

Bishopu wa Roma Katolika (ku Italiya): “Wopambana, Wotchuka Koposa ndi Monsinyolo Wolemekezeka Koposa.”

Kadinala: “Womvekatu.”

Papa: “Atate Woyera Koposa.”

Maina aulemuwo “levulendi” ndi “bishopu” akhala akugwiritsiridwa ntchito kwa nthaŵi yaitali kotero kuti samamveka moipa kwa ziŵalo zambiri zatchalitchi. Koma kodi maina aulemu otero ali ovomerezedwa ndi Baibulo?

“Levulendi,” “Bishopu,” ndi “Kadinala”

Mu King James Version, liwulo “revalandi” limawonekera kamodzi kokha, pa Salmo 111:9, limene limati: “Loyera ndi lolemekezeka [reverend] ndilo dzina lake.” Dzina la yani kodi? Vesi lotsatira limati: “Kuwopa AMBUYE ndiko chiyambi cha nzeru.” (Salmo 111:10) M’matembenuzidwe ena Achikatolika, mizera iŵiriyi ili ndi mawu akuti: “Nloyera ndi lowopsa dzina lake. Muzu wa nzeru ndiwo kuwopa Yahweh [Yehova].” (The New Jerusalem Bible) Chifukwa chake, malinga ndi Mawu a Mulungu, mantha aumulungu, kapena ulemu, nza Yehova yekha basi, Wamphamvuyonse. Pamenepo kodi nkolondola kuwapatsa kwa anthu?

“Ngati munthu akhumba udindo wa bishopu, aikhumba ntchito yabwino,” analemba motero Paulo kwa Timoteo. (1 Timoteo 3:1, KJ) Komabe, malinga ndi The New Jerusalem Bible, vesili limati: “Kufuna kukhala mkulu wotsogoza ndiko kukhumba ntchito yaulemu.” Akristu oyambirira okhala ndi mathayo auyang’aniro anali kutchedwa “akulu” ndi “oyang’anira.” Kodi mawu amenewo anagwiritsiridwa ntchito monga maina aulemu? Ayi. Amuna otero sanali kutchedwa konse kuti “Bishopu Petro” kapena “Mkulu Yakobo.” Ndicho chifukwa chake amuna okula msinkhu Achikristu pakati pa Mboni za Yehova amene amatumikira monga akulu samagwiritsira ntchito konse liwu lakuti “mkulu” monga dzina laulemu. Mawuwo “mkulu” ndi “woyang’anira” (bishopu) amagwira ntchito kwa amene ali ndi malo aukumu ndi athayo. Mawu amenewo amafotokozanso ziyeneretso za amuna oikidwa ndi ntchito imene amachita.

Bwanji ponena za dzina laulemu la “kadinala”? Kodi limapezeka m’Baibulo? Ayi. Silimapezeka m’matembenuzidwe alionse. Kunena zowona, Tchalitchi cha Roma Katolika chimavomereza kuti dzina laulemu limeneli siliri la m’Baibulo. New Catholic Encyclopedia imafotokoza kuti: “Liwulo latengedwa ku liwu Lachilatini la cardo lotanthauza ‘hinji,’ ndipo mogwirizana ndi mawu a Papa Eugene IV, anati ‘monga momwe chitseko cha nyumba chimayezekedwa pamahinji ake, choteronso Udindo Wautumwi umayezekedwa paukadinala, chitseko cha Tchalitchi chonse, chimaimapo ndi kupeza chichirikizo.’” Bukhu lamaumboni limeneli limatiuzanso kuti “akadinala ali ndi mwaŵi wakutchedwa mwachindunji monga ‘Omvekatu.’” Ndiponso malo awo audindo amawalola kuvala chibakuwa ndi nsuli zofiira. Kodi atumwi anali ndi ‘mwaŵi’ umenewo? Baibulo limayankha kuti ayi.

“Ambuye,” “Amonsinyolo,” ndi “Abambo”

Kodi ziŵalo za kagulu ka atsogoleri achipembedzo ziyenera kutchedwa ambuye? Abishopu Aangilikani amatchedwa “mbuye.” Kaŵirikaŵiri ansembe Achikatolika amatchedwa “amonsinyolo,” kutanthauza “Mbuye ŵanga.” M’maiko ena, aminisitala a Tchalitchi cha Dutch Reformed amatchedwa dominee, dzina laulemu lotengedwa ku liwu Lachilatini la dominus, lotanthauza “ambuye.” Koma Yesu analangiza ophunzira ake kuti: “Mudziŵa kuti m’dziko, olamulira amachita ufumu pa alambi awo, . . . koma sikudzakhala motero ndi inu.” (Mateyu 20:25, 26, The New English Bible) Ndiponso, mtumwi Petro analemba kuti: “Musachite ufumu pakagulu komwe muyang’anira, koma khalani chitsanzo ku gululo.” (1 Petro 5:3, NJB) Panthaŵi imene Yesu modzichepetsa anasambitsa mapazi a ophunzira ake, anati kwa iwo: “Mumanditcha Mphunzitsi ndi Ambuye, ndipo mumalondola; popeza ndine amene.” (Yohane 13:13, NJB) Kodi nkoyenera kwa anthu kugwiritsira ntchito dzina laulemu lachipembedzo limene liri la Mulungu ndi Mwana wake?

Kodi dzina laulemu lachipembedzo lakuti “abambo” nlolondola? Ilo limagwiritsiridwa ntchito mofala ndi Aroma Katolika ndi Aangilikani. “Padure,” lotanthauza “abambo,” limagwiritsiridwanso ntchito mofala. Koma Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti: “Musatche aliyense padziko lapansi bambo wanu, pakuti muli ndi Bambo mmodzi yekha, ndipo ali kumwamba.” (Mateyu 23:9, NJB) The New English Bible ili ndi mawu ofanana akuti: “Musatche munthu aliyense padziko lapansi ‘abambo.’” Kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo ndi otsatira awo amaswa lamulo limeneli loperekedwa ndi Ambuye Yesu Kristu?

Kaŵirikaŵiri papa wa Roma amatchedwa “Atate Woyera.” Koma antchito ake Achitaliyana kaŵirikaŵiri amamutcha kuti Santissimo Padre, limene limatanthauza “Atate Woyera Koposa.” “Atate Woyera” liri dzina laulemu limene limawonekera kamodzi kokha m’Baibulo. (Yohane 17:11) Liri dzina laulemu lapadera la Mulungu Wam’mwambamwamba yekha. Kodi nkoyenera kwa zolengedwa, zapadziko lapansi ndi zopanda ungwiro, kutchedwa ndi dzina laulemu limenelo?

Kulakwa kwa Chipembedzo

Chonde taŵerengani ndi kumvetsetsa mawu apambuyo ndi patsogolo a Mateyu 23:1-12. Yesu akuyamba kulankhula za Afarisi, amene ali kagulu kampatuko kotchuka ka Chiyuda. Iwo anali oumira chilamulo, ononomera pakusungidwa kwa mbali iriyonse ya Chilamulo cha Mose. Anakonda kuvala ndi kudzisungira mwa njira yakuti anali kukopa chisamaliro cha anthu. Chipembedzo chawo chinali cha kudzitukumula—m’kavalidwe kawo, malo awo apamwamba pachakudya, mipando yawo yakutsogolo m’masunagoge, ndi maina awo aulemu. Anafunsiradi ulemu wokulirapo woposa woperekedwa kwa makolo. Anafuna kutchedwa atate. Komabe, Yesu akusonyeza kuti otsatira ake onse ali olingana monga ana a Mulungu. Dzina laulemu lirilonse losonyeza zosiyana liri kulanda mwamwano kanthu kena kamene kali ka Mulungu. Chifukwa chake, Yesu akuletsa kugwiritsiridwa ntchito kwa liwulo “atate” monga dzina laulemu m’lingaliro lachipembedzo. Yesu akutsimikizira kuti otsatira ake ali ndi Atate mmodzi yekha m’chikhulupiriro, Yehova.

Kodi sikuli kwachiwonekere kuti atsogoleri achipembedzo ambiri akuima ‘pamalo oyera’ osungidwira Mulungu ndi Mwana wake, ndi kuti ulemu wochuluka umachotsedwa kwa iwo ndi kupatsidwa kwa anthu opanda ungwiro? Akristu owona lerolino amapeŵa kugwiritsira ntchito maina aulemu achipembedzo osyasyalika, ndipo amapeŵa chizoloŵezi cha kulemekeza atsogoleri achipembedzo. Pakati pa Mboni za Yehova njira yokha yotchulira aminisitala ndiyo “mbale.” (2 Petro 3:15) Zimenezo nzogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: “Inu nonse muli abale.”—Mateyu 23:8, NJB.

[Mawu a Chithunzi patsamba 12]

Abishopu Atatu ojambulidwa ndi Albrecht Dürer, pafupifupi 1507

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena