Mutu 4
Chiwonongeko cha Dziko Lonse Choyamba—Kenako Mtendere wa Dziko Lonse
1-3. (a) Kodi nchiyani chimene chiri chiwonongeko cha dziko lonse chimene atsogoleri aumunthu akuchenjeza? (b) Kodi nchifukwa ninji chimenecho sindicho chimene Baibulo limatcha kukhala chiwonongeko cha dziko lonse chimene chidzatsegula njira kaamba ka mtendere wosatha ndi chisungiko?
MALINGA ndi kunena kwa ulosi Wabaibulo, mtundu wa anthu usanasangalale ndi mtendere wosatha, chiwonongeko cha dziko lonse chiyenera kuchitika choyamba. (2 Petro 3:5-7) Koma kodi nchifukwa ninji zimenezo ziri zofunika? Kodi chiwonongekocho chidzachokera kuti? Ndipo kodi chimatanthauzanji kwa anthu papulaneti lino?
2 Choyamba tiyenera kuzindikira kuti chiwonongeko cha dziko lonse chimene Baibulo limachineneratu sichiri chofanana ndi chipiyoyo cha pa dziko lonse lapansi chimene atsogoleri adziko ochuluka, asayansi, ndi ena akuchenjeza. Tsoka limene iwo amanena lingafike m’mpangidwe wa chiwonongeko chochititsidwa ndi anthu chobweretsedwa ndi zinthu zonga kuipitsa kapena mpikisano wa zida zankhondo zanyukliya, kapena zonse ziŵiri. Koma, ndithudi, chipiyoyo chotero sichikanasiya chiyembekezo chamtendere wosatha ndi chisungiko papulaneti lino.
3 Dziko lapansi likanawonongedwa kaamba ka zolengedwa zamoyo. Mwachitsanzo, utsi wa zida zankhondo zanyukliya kapena “chisanu chanyukliya” chofalitsidwacho sichikanasiya opulumukawo ali bwinopo—ngati mwinamwake kusali kukhala zowaipira kwambiri—koposa awo amene anali atafa. Kupulumuka kukakhala kwakukulukulu kodalira pa mwaŵi, ngakhale kuli kwakuti mosakaikira osauka akakhala pakati pa oyambirira kuvutika. Kodi nchiyembekezo chotani chimene inu mukakhala nacho cha kukhala pakati pa opulumuka chipiyoyo choterocho? Ndipo ngakhale ngati munapulumuka, kodi nchiyembekezo chotani chimene chikanakhalapo chakuti moyo sukabwereranso m’kusatsimikizirika kodzadza ndi nkhondo kofananako kumene tsopano kuli kochulukako?
Chimene Baibulo Limaneneratu Chimapatsa Chiyembekezo
4. Kodi ndani amene ayenera kuwonongedwa m’chiwonongeko cha dziko lonse chimene Baibulo limanena?
4 Chimene chimapanga chiwonongeko cha dziko chimene Baibulo limaneneratu kukhala chosiyana nchakuti chidzakhala chosankha, chidzakhala ndi chifuno. Silidzakhala tsoka limene limadza chabe monga chimake cha zolakwa za munthu. Mmalo mwa kudzetsa imfa mosasankha, chidzachotsa padziko lapansi awo okha amene kwenikweni ali oyenera kuwonongedwa. Chiwonongeko cha dziko cha mtundu uwu chiri chogwirizana ndi lamulo la makhalidwe abwino laumulungu pa Miyambo 2:21, 22, (NW) kuti: “Pakuti owongoka mtima ndiwo amene adzakhala m’dziko lapansi, opanda chifukwa nadzatsalamo. Ponena za oipa adzadulidwa m’dziko lapansi, achiwembu adzachotsedwamo.”
5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitikira dziko lapansi lenilenili mkati mwa chiwonongeko cha dziko lonse chimenecho? (b) M’njira imeneyi, kodi ndimotani mmene kudzakhalira “monga masiku a Nowa”?
5 Pamenepa, kodi nchiyani, chimene chidzawonongedwa? Ambiri amaganizira kuti Baibulo limaneneratu kuwotchedwa kotheratu kwa pulaneti Dziko Lapansi ndi chinthu chirichonse pa iro. Koma izi siziri choncho. Yesu Kristu iye mwini anati: “Achimwemwe ali odekha mtima, pakuti adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5, NW) Ndithudi ‘cholowa’ chimenecho sichidzakhala khala lopserera, lopandapo moyo! Baibulo limaperekanso chitsimikiziritso chenicheni cha Mulungu chakuti dziko lapansi lidzakhalabe losatha monga malo okhala anthu.—Salmo 104:5; Yesaya 45:18; Mateyu 6:9, 10.
6 Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo limatchula opulumuka amene adzatsala padziko lapansi chitapita “chisautso chachikulu” chimenecho. Yesu Kristu ananena kuti “monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.” Pamene chiwonongeko chapadziko lonse chinachitika m’nthawi ya Nowa panalinso opulumuka.—Mateyu 24:21, 37; 2 Petro 2:5, 9; Chivumbulutso 7:9, 10, 13, 14.
7. Kodi nchiyani chimene chidzatha panthawi imeneyo?
7 Kodi nchiyani chimene chiyenera kuwonongedwa? Ndicho dongosolo la zinthu ladziko lonse limene anthu alipanga padziko lapansi—limodzi ndi awo onse amene amalichirikiza mmalo mwa kuyang’ana kwa Mulungu ndi ulamuliro wake wolonjezedwa wa dziko lapansi. (Salmo 73:27, 28) Ndicho chifukwa chake mawu akuti “mapeto a dziko,” opezeka m’matembenuzidwe ena a Baibulo ngomasuliridwa molondola kwambiri m’Mabaibulo ena kukhala “mathedwe a nyengo” (NE), “matsiriziro a nyengo” (Ro), “mapeto a dongosolo la zinthu” (NW).—Mateyu 24:3.
8. (a) Kodi chiwonongekocho chidzadza kuchokera ku magwero otani? (b) Kodi chimenechi chiyenera kuchitika dongosolo la dziko lonse liripoli lisanafike pamkhalidwe wotani?
8 Magwero a chiwonongeko cha dziko lonse chirinkudza adzakhala—osati anthu—koma Yehova Mulungu. Mavuto amakono akuipitsa, njala, mantha a nyukliya, ndi zinthu zofanana zimene zachokera m’kusadziwa kwa anthu, kulakwa, ndi chisalungamo sindiwo amene adzachititsa chiwonongeko. Mmalo mwake, amenewa ali umboni wadyera ndi kulephera kotheratu kwa dongosolo la dziko limene liripoli. Iwo amapereka chifukwa choyenera choti Yehova Mulungu achotsere kotheratu dongosolo limenelo. Iye akulonjeza kuchita kachitidwe kameneko dongosolo la dziko liripoli lisanafike konse pamkhalidwe wa kugwa kapena lisanadziwononge lokha. (Chivumbulutso 11:17, 18) Koma kodi kachitidwe kamphamvu kameneko ndiko kwenikweni njira yokha?
Chifukwa Chake Dongosolo la Dziko Lonseli Liyenera Kutha Kuti Mtendere Weniweni Udze
9, 10. Kodi ndimotani mmene mbiri yaumunthu imasonyezera kuti kanthu kena kamphamvu kwambiri kakufunika koposa kusinthidwa chabe kwa dziko liripoli?
9 Ena angalingalire kuti Mulungu ayenera kupanga masinthidwe m’dongosolo liripoli, mmalo mwa kuliwononga. Koma Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akudziwa bwino lomwe kuti iro liri losati nkukonzeka.
10 Talingalirani nokha masinthidwe ochulukawo amene apangidwa ndi anthu mkati mwa zaka mazana ambiri zapitazo. Talingalirani mitundu yonse yosiyanasiyana ya maboma amene anthu apanga. Kunapangidwa maboma amzinda, maufumu, mademokrase, maboma achikomyunizimu ndi sosholizimu, ndi maulamuliro otsendereza ufulu. Kumbukirani mmene wolamulira amene alipo, kapena boma analowedwera mmalo mwa kaŵirikaŵiri ndi latsopano—mwa masankho, mwa kulanda boma, kapena chipanduko. Komabe sipanakhale chothetsera chosatha cha mavuto a anthu. Ngakhale anthu okhala ndi cholinga chabwino amene amayesa kukonza makhalidwe a anthu amapeza kuti zoyesayesa zawo zikudodometsedwa ndi dongosolo la zinthu mu limene iwo eniwo apanikizidwira. Monga momwe wolamulira wanzeru wa m’nthawi zakale anawonera, mwa zoyesayesa za anthu zokha “chimene chapangidwa kukhala chokhotakhota sichingawongoledwe.”—Mlaliki 1:14, 15, NW.
11-13. (a) Kodi nchiyani chimene chimalepheretsa anthu kupanga masinthidwe m’dongosolo liripoli kaamba ka ubwino wa anthu onse? (b) Chotero, kodi ndimotani mmene ukulu wa kusintha kofunikako ungalongosoledwere mwafanizo?
11 Mwachitsanzo, mizinda ya dziko, yakanthidwa ndi mavuto. Koma anthu sangathe kuiphwanya ndi kuyambiranso. Ziri zofanana ponena za dongosolo lonse la zachuma ndi la zamaindasitale la dziko. Kudzikonda ndi utundu zimafooketsa ndi kudodometsa kusintha kwenikweni kaamba ka ubwino wa anthu onse.
12 Motero dongosolo lonse lazinthu liri ngati nyumba yomangidwa pamaziko oipa, chifukwa cha kuipa kwa mapulani, ndi zomangira zokhala ndi nthenya. Kodi kudzachita ubwino wotani kulinganizanso mipando ndi matebulo kapena kukonzanso nyumbayo? Malinga ngati iri chiimire, mavutowo adzapitirizabe, ndipo nyumbayo idzapitirizabe kuipiraipira. Chinthu chokha chanzeru kuchita ndicho kugwetsa nyumbayo ndi kumanga ina, pamaziko abwino.
13 Yesu Kristu anagwiritsira ntchito fanizo lofanana pamene ananena kuti anthu “samathira vinyo watsopano m’matumba akale.” Matumba avinyo akalewo akaphulika ndi vinyo watsopanoyo. (Mateyu 9:17) Chifukwa cha chimenecho iye sanayese kukonzanso dongosolo la zinthu Lachiyuda limene anali kukhalamo. Mmalomwake, iye analalikira Ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo chokha kaamba ka mtendere ndi chisungiko. (Luka 8:1; 11:2; 12:31) Momwemonso, m’tsiku lathu, Yehova Mulungu sadzangokonzanso dongosolo liripoli lazinthu chifukwa chakuti kutero sikungabweretse phindu losatha.
14. Kodi kupangidwa kwa malamulo atsopano kungapangitse anthu kukonda chilungamo?
14 Mawu a Mulungu akugogomezera chowonadi chakuti nkosatheka kuloŵetsa chilungamo m’mitima ya anthu. Ngati iwo samakonda chimene chiri cholungama, palibe kuchuluka kulikonse kwa malamulo kumene kudzachiikamo. Pa Yesaya 26:10 timawerenga kuti: “Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m’dziko la machitidwe owongoka, iye adzangochimwa, sadzawona chifumu cha Yehova.”—Yerekezerani ndi Miyambo 29:1.
15, 16. Kodi ndimotani mmene kupanda chikondi chowona kaamba ka chilungamo kwa anthu ochuluka kwasonyezedwera m’kulabadira kwawo chifuniro cha Mulungu?
15 Chenicheni chosakanika ndicho chakuti anthu ambiri akusankha kukhalabe ndi dongosolo liripoli mosasamala kanthu za zolephera ndi zoipa zake. Samafuna kutembenukira ku chilungamo ndi kugonjera ku ulamuliro wochokera kwa Mulungu. Iwo angawone ukathyali wa madongosolo a ndale zadziko zaudziko, kupanda pake kwa nkhondo zake, ndi chinyengo cha zipembedzo zake, ndi umboni wowoneka bwino wakuti luso lake la zopangapanga lasayansi lapanga mavuto okulirapodi kwambiri koposa amene lawathetsa. Koma mosasamala kanthu za zonsezi, ambiri amakonda kukopedwera ku lingaliro lonyenga la chisungiko la atsogoleri achipembedzo ndi andale za dziko amene zikhumbo zawo ziri kusunga malo amene ali nawo. Iwo ali ngati Aisrayeli amene Mulungu ananena za iwo kuti: “Aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pa kulamulira kwawo; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?”—Yeremiya 5:31; Yesaya 30:12, 13.
16 Mwachiwonekere inu mumadziŵa anthu amene ali ndi zizoloŵezi zimene zimaika paupandu thanzi la iwo eni ndi chisungiko ndi zija za mabanja awo. Komabe iwo amakana zoyesayesa zonse zowathandiza kusintha. Koma pamene anthu akana uphungu wa Mulungu ndi chitsogozo, nkhaniyo imakhala yowopsa kwambiri. Awo amene amachita izi amasonyeza kuti samakondadi chowonadi ndi chilungamo. Ponena za anthu otero Yesu anati: “Pakuti mtima wa anthu awa wakhala wosalabadira, ndipo iwo amva ndi makutu awo mosalabadira, ndipo atseka maso awo; kuti asawone ndi maso awo ndi kumva ndi makutu awo ndi kupeza tanthauzo lake ndi mitima yawo ndi kutembenuka, ndipo [Mulungu] nkuwachiritsa.”—Mateyu 13:15, NW.
17. Ngati ziri zowona kuti Mulungu samakondwera ndi kubweretsa chiwonongeko pa anthu, kodi nchifukwa ninji adzachibweretsa?
17 Moyenerera, kudekha kwa Mulungu ndi chifundo ziri ndi polekezera pake. Ngati siziri choncho, kodi chikondi chake kaamba ka olungama chikanakhala pati? Iye sangakhale wosamvetsera zopempha zawo kaamba ka mpumulo ku kuvutika kumene kuipa kumadzetsa padziko lapansili. (Luka 18:7, 8; Miyambo 29:2, 16) Chotero, mikhalidwe ikufunikiritsa chiwonongeko cha dziko lonse lapansi. Iyo ikukakamiza Mulungu kuchita choncho na ngati iye ati achite mogwirizana ndi chimene chiri choyenera ndi cholungama ndi kusonyeza chifundo kwa awo amene amakondanso chimene chiri choyenera. Sindiko kuti Mulungu ali wokondwera kudzetsa chiwonongeko pamtundu wa anthu. “Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, sindiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo? . . . Chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.”—Ezekieli 18:23, 32.
18. Kodi ndimtengo wotani umene uyenera kulipiridwa kuwombola anthu ku kupanda chisungiko amene amakonda chilungamo?
18 Pamenepa, chiwonongeko cha awo okonda dongosolo liripoli la zinthu, ndiwo mtengo umene uyenera kulipidwa kumasula awo amene amakonda choyenera ku kupanda chisungiko ndi kuvutika. Chimenechi chiri chogwirizana ndi lamulo la Baibulo la khalidwe labwino, lakuti: “Wochimwa ndiye chiwombolo cha wolungama.”—Miyambo 21:18; yerekezerani ndi Yesaya 43:1, 3, 4.
Zotulukapo Zopindulitsa
19. Kodi ndimipiringidzo yotani ya mtendere wa dziko lonse imene idzachotsedwa mwa kuwonongedwa kwa dongosolo iri la zinthu?
19 Chiwonongeko cha dongosolo liripoli ndi ochirikiza ake chidzatheketsa dongosolo latsopano lolungama padziko lonse lapansi m’limene opulumuka adzakhala okhoza kugwira ntchito pamodzi mogwirizana, osati mu mpikisano wadyera. Malire ogawanitsa autundu ndi malire andale za dziko adzatha. Katundu wolemera wa ndalama zowonongeredwa pa zankhondo adzatha. Ndipo imene idzakhalanso itatha ndiyo mipiringidzo ya kusankhana kwa anthu imene imalepheretsa anthu kukhala banja logwirizana. Chinthu chofunika m’zonsezi chidzakhala chakuti onse okhala ndi moyo panthawiyo adzalankhula ‘chinenero chimodzi choyera’ cha chowonadi wina ndi mnzake, kulambira Mlengi wawo “mumzimu ndi chowonadi.” Izi zidzawatetezera kukhulupirira malaulo kwa chipembedzo kogawanitsa, miyambo, ndi ziphunzitso zopangidwa ndi anthu.—Zefaniya 3:8, 9; Yohane 4:23, 24, NW.
20. Monga momwe kwasonyezedwera ndi Salmo 72, kodi ndimkhalidwe wotani umene udzakhalako padziko lonse lapansi?
20 Pamene boma la Mulungu lokhala m’manja mwa Mwana wake Kristu Yesu lidzalamulira kotheratu padziko lonse lapansi, salmo lakale la Baibulo lidzakwaniritsidwa: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera kumtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.”—Salmo 72:7, 8.
21. Kodi ndimotani mmene dziko lapansi lenilenilo lidzapindulira ndi chiwonongeko cha dziko lonse chikudzacho?
21 Dziko lapansi lidzapindula ndi chiwonongeko cha dziko lonse chirinkudza. Silidzawonongedwanso ndi kuipitsidwa ndi oipitsa aumbombo ndi owononga ankhanza. Nyanja, mitsinje, nyanja zamchere kudzanso mpweya zidzapeza mpumulo kuzinyalala zonse zotayiridwamo ndipo posapita nthawi yaitali zidzadziyeretsa. Motero Mulungu adzasonyeza kuti iye sananyalanyaze chifuno chake choyambirira cha kukhala ndi pulaneti loyera, longa munda lodzadzidwa ndi anthu amene amasonyeza mikhalidwe yabwino kwambiri ya Mlengi wawo.—Genesis 1:26-28; Yesaya 45:18; 55:10, 11.
22. Kodi ndimotani mmene kubweretsedwa kwa chiwonongeko chimenecho kuliri kogwirizana ndi kukhala kwa Mulungu ‘Mulungu wamtendere’?
22 Chotero, kudzetsa kwa Mulungu chiwonongeko cha dziko lonse sikuli kosemphana ndi kukhala kwake ‘Mulungu wamtendere.’ Ndiponso sikuli kosemphana ndi kukhala kwa Yesu “Kalonga wa Mtendere.” Chiri chifukwa cha kukonda kwawo mtendere ndi chilungamo kuti iwo akuchita kachitidwe kameneka kubwezeretsa dziko lapansi ku mkhalidwe woyera ndi wolungama.—1 Akorinto 14:33; Yesaya 9:6, 7.
23, 24. Ngati titi tidzasangalale ndi mtsogolo mwa mtendere ndi chisungiko, kodi nchiyani chimene chiri chofunika kwambiri kwa aliyense wa ife kuchichita tsopano?
23 Pamenepa, monga munthu aliyense payekha, kodi tiyenera kuchitanji? Yesu anasonyeza kuti awo onyalanyaza malangizo a Mulungu anali kumanga ziyembekezo zawo zamtsogolo pa “mchenga” ndi kuti nyumba yoteroyo siikaima konse pa mikuntho yowononga imene irinkudza. Iye anasonyeza kufunika kwakukulu kwambiri kwa kumangira ziyembekezo zathu pa kumvera Mawu a Mulungu na ngati titi tikhale ndi mtsogolo mwamtendere ndi mosungika.—Mateyu 7:24-27.
24 Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu wayembekezera nthawi yaitali motero kuthetsa kuipa ndi kuvutika? Baibulo likuyankhanso funsoli ndipo likusonyeza chimene Mulungu wakhala akuchita mkati mwa zaka mazana onse zapitazo kukwaniritsa chifuno chake.
[Chithunzi patsamba 37]
Monga momwe anthu anapulumukira Chigumula, padzakhala opulumuka a “chisautso chachikulu”