-
Mbadwo Wa 1914—Kodi Nchifukwa Ninji Uli Wapadera?Nsanja ya Olonda—1992 | May 1
-
-
M’zaka za zana loyamba C.E., Yesu anati kukhalapo kwake kosawoneka monga Mfumu yatsopano ya dziko lapansi kukadziŵika ndi chizindikiro chowoneka. Iye anafunsidwa kuti: ‘Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?’ Kodi yankho lake linali lotani? ‘Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.’—Mateyu 24:3, 7, 8.
Chotero, nkhondo yomwe inaulika mu 1914 inatsagana ndi kupereŵera kwa zakudya kochititsa mantha, popeza kuti kulima kunasokonezedwa kwa zaka zoposa zinayi. Bwanji ponena za ‘zivomezi m’malo akutiakuti’? M’zaka khumi zotsatira 1914, zivomezi zosakaza zosachepera khumi zinapha anthu oposa 350,000. (Onani bokosi.) Ndithudi, mbadwo wa 1914 unawona “zowawa zoyamba.” Ndipo chiyambire pamenepo, zowawa zoyamba zakantha mokhazikika mumpangidwe wa masoka achilengedwe, njala, ndi nkhondo zambirimbiri.
Komabe, mbiri ya kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu mu 1914 ndimbiri yabwino chifukwa chakuti Ufumu umenewo udzapulumutsa dziko lapansili ku kuwonongedwa. Motani? Udzachotsa zipembedzo zonse zonama, zachinyengo, maboma oipa, ndi chisonkhezero choipa cha Satana. (Danieli 2:44; Aroma 16:20; Chivumbulutso 11:18; 18:4-8, 24) Ndiponso, lidzabweretsa dziko latsopano m’mene ‘mudzakhalitsa chilungamo.’—2 Petro 3:13.
Mwamsanga pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I, Ophunzira Baibulo okangalika, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira panthaŵiyo, anayamba kuzindikira mwaŵi wawo ponena za mbali ina ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu. Yesu Kristu ananeneratu kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa padziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.
Mwakuyamba pang’onopang’ono mu 1919, Mboni za Yehova zapitiriza osaleka kufalitsa “mbiri yabwino imeneyi.” Chifukwa chake, anthu mamiliyoni ambiri m’maiko oposa 200 akusonkhanitsidwa tsopano monga nzika za Ufumu wa Mulungu. Ndipo ndimadalitso otani nanga omwe akuyembekezera nzika zimenezi! Ufumuwo udzathetsa nkhondo, njala, upandu, ndi kutsendereza. Udzathetsanso matenda ndi imfa!—Salmo 46:9; 72:7, 12-14, 16; Miyambo 2:21, 22; Chivumbulutso 21:3, 4.
Mbadwo wa 1914 usanachoke, ntchito yolalikira Ufumu idzakhala itakwaniritsa chifuno chake. “Pa nthaŵi imeneyo,” ananeneratu Yesu, “kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zowona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amenewo, palibe munthu aliyense amene akadapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.”—Mateyu 24:21, 22, NW.
-
-
Mbadwo Wa 1914—Kodi Nchifukwa Ninji Uli Wapadera?Nsanja ya Olonda—1992 | May 1
-
-
[Tchati patsamba 7]
Zivomezi m’Zaka Khumi Zotsatira 1914
Deti: Malo: Ophedwa:
January 13, 1915 Avezzano, Italiya 32,600
January 21, 1917 Bali, Indonesia 15,000
February 13, 1918 Kwangtung Province, Tchaina 10,000
October 11, 1918 Puerto Rico (kumadzulo) 116
January 3, 1920 Veracruz, Mexico 648
September 7, 1920 Reggio di Calabria, Italiya 1,400
December 16, 1920 Ningsia Province, Tchaina 200,000
March 24, 1923 Szechwan Province, Tchaina 5,000
May 26, 1923 Iran (kumpoto koma chakum’mawa) 2,200
September 1, 1923 Tokyo-Yokohama, Japani 99,300
Zotengedwa pa ndandanda ya mutu wakuti “Significant Earthquakes of the World” m’bukhu lakuti Terra Non Firma, lolembedwa ndi James M. Gere ndi Haresh C. Shah.
-