Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapeza makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa kukhala okupindulitsani? Bwanji osadziyesa kuti muone ngati mukukumbukira mwa kuyankha mafunso otsatiraŵa:
◻ Kodi ndi mafunso aŵiri ati amene athandiza Akristu amene akulingalira zopeza ntchito kusankha okha chochita?
Funso loyamba lalikulu n’lakuti: Kodi ntchitoyo n’njoletsedwa m’Baibulo? Funso lachiŵiri n’lakuti: Kodi kugwira ntchito imeneyi kungam’pangitse munthu kukhala wotengamo mbali mumchitidwe woletsedwa?—4/15, tsamba 28.
◻ Ndi m’njira yotani mmene cholengedwa cha umunthu chagonjetsedwera kuutsiru? (Aroma 8:20)
“Tinagonjetsedwa kuutsiru” chifukwa cha zimene makolo athu oyambawo Adamu ndi Hava anachita. “Chinali chosafuna enife” kapena chifukwa cha zimene aliyense anasankha kuti zimenezi zichitike. Tinachita kubadwa nazo. Ngakhale kuti makolo athu oyambawo tsopano anali kudzapatsira ana awo kupanda ungwiro, uchimo ndi imfa, Yehova mwa chifundo anawalola kubereka ana. Chotero imfa inafikira anthu onse, choncho m’lingaliro limenelo Mulungu ‘anagonjetsa cholengedwa kuutsiru.’—5/1, tsamba 5.
◻ Kodi n’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kunena kuti “chonyansa” ‘chidzaima m’malo oyera’ m’tsogolo? (Mateyu 24: 15)
Kalelo, ‘chonyansa choima m’malo oyera’ chinakhudzana ndi kuukira kwa Aroma motsogozedwa ndi Kazembe Gallus mu 66 C.E. Kuukira kwamakono kolingana ndi kwakaleko—kuyambika kwa chisautso chachikulu—kudakali m’tsogolo. (Mateyu 24: 21) Chotero “chonyansa cha kupululutsa” chidzaima pamalo oyera m’tsogolo.—5/1, masamba 16, 17.
◻ Kodi bambo ndi mayi apantchito angapeze motani nthaŵi yocheza ndi ana awo?
Mayi yemwe watopa ataŵeruka kuntchito angapemphe ana ake kum’thandiza kuphika chakudya. Bambo yemwe ali ndi zochita zambiri kumapeto a mlungu angagwire ntchitoyo limodzi ndi ana ake.—5/15, tsamba 6.
◻ Kodi amene ‘akuyenda m’njira ya Yehova’ ayenera kuchita chiyani? (Yeremiya 7: 23)
Kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kukhulupirika—kutsimikiza mtima kuti tidzatumikira yekhayo basi. Zimafuna kukhulupirira—chikhulupiriro chenicheni chakuti malonjezo a Yehova ali odalirika ndipo adzakwaniritsidwadi. Kuyenda m’njira ya Yehova kumafuna kumvera—kutsatira malamulo ake ndi kusapatukapo komanso kusunga miyezo yake yapamwamba. (Salmo 11:7)—5/15, tsamba 14.
◻ Kodi ndi maudindo ofunika anayi ati amene “mphatso za amuna” zingaŵachite? (Aefeso 4:8)
Angathe kutiwongolera mwachifundo, kutimangirira mwachikondi, kulimbikitsa umodzi wa mpingo, ndi kutiteteza molimba mtima. (Aefeso 4:12-14)—6/1, tsamba 14.
◻ Kodi tingaphunzirenji pa kuyanjana kwa Paulo ndi anthu okwana zana limodzi otchulidwa m’Machitidwe ndi m’makalata ake ena?
Nthaŵi zonse tiyenera kugwira ntchito limodzi ndi gulu la Mulungu, ndi mpingo wakwathu, komanso ndi okhulupirira anzathu. Timafunikira thandizo lawo, chichirikizo chawo, ndi chitonthozo chawo pamtendere ndi pamavuto.—6/1, tsamba 31.
◻ Ndi mfundo zitatu ziti zimene tingagwiritse ntchito pothandiza ena kulingalira za Mlengi?
Luso limene timaliona m’zinthu zakuthambo ndi za padziko, chiyambi cha moyo padziko lapansi, komanso kudabwitsa kosatsutsika kwa ubongo wa munthu, ndi luso lake losiyanasiyana.—6/15, tsamba 18.
◻ N’chifukwa chiyani kudziŵa tanthauzo la dzina lenileni la Mlengi kuli kofunika?
Dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako” ndipo limatsimikizira kuti iye amachita chimene wafuna. Mwa kudziŵa ndi kugwiritsa ntchito dzina lakelo, tingazindikire bwino lomwe kuti iye amakwaniritsa malonjezo ndi cholinga chake.—6/15, tsamba 21.
◻ Kodi ana angatenge mbali motani pa phunziro la Baibulo la banja?
Ngati n’kotheka, mwana aliyense akhale ndi Baibulo ndi buku lophunziridwa lakelake. Wachichepere angapemphedwe kukambapo pa zithunzi zomwe zili m’nkhani imene mukuphunzirayo, ndipo mwana wina angauzidwiretu kuti aŵerenge lemba. Wokulirapo angapatsidwiretu mwayi wodzafotokoza mbali zimene mungagwiritse ntchito zomwe mwaphunzirazo.—7/1, tsamba 15.
◻ Kodi ndi zolinga zina ziti zimene banja lingaphatikize m’kukonzekera kwawo misonkhano ya mpingo?
(1) Aliyense m’banjamo akonzekere kukayankhapo pamsonkhano; (2) aliyense akonzekere kukayankha m’mawu akeake; (3) kuphatikiza malemba m’mayankho; ndipo (4) kupenda nkhaniyo ndi kuona mmene ingathandizire aliyense payekha.—7/1, tsamba 20.
◻ Kodi kiyi ya ukwati wabwino n’chiyani?
Kuti mutsegule ndi kuloŵa m’zisangalalo zamtengo wapatali za ukwati wabwino, chofunika kwambiri ndicho kulankhulana kwabwino. Zimenezi zimaphatikizamo kupatsana maganizo. Ndipo kulankhulana kwabwino kumaphatikiza kuuzana zinthu zimene zili zomagirira, zotsitsimula, zokoma mtima, zotamandika, ndi zotonthoza. (Aefeso 4:29-32; Afilipi 4:8)—7/15, tsamba 21.
◻ Kodi ‘njira ya Yehova’ n’chiyani? (Salmo 25:8, 9, 12)
Njira imeneyo ndiyo njira ya chikondi. Yazikidwa pa kuchita cholungama mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Baibulo limatcha chikondi chalamulo chimenechi “njira yokoma yoposatu.” (1 Akorinto 12:31)—8/1, tsamba 12.