-
Kuunikira Chidziŵitso pa Kukhalapo kwa KristuNsanja ya Olonda—1993 | May 1
-
-
8, 9. (a) Kodi kukhalapo kwachifumu kwa Yesu kumaloŵetsamo chiyani? (b) Kodi ulosi wa Yesu wonena za a Kristu onama umasonyezanji ponena za malo ndi mkhalidwe wa kukhalapo kwake?
8 Popeza kuti ufumu wa Yesu umakuta dziko lonse lapansi, kulambira kowona kukufutukukira ku zigawo zonse za dziko. Kukhalapo (pa·rou·siʹa) kwake kwachifumu kuli nthaŵi ya kuyang’anira kwa padziko lonse. (1 Petro 2:12) Koma kodi pali mzinda walikulu, kapena malo apakati, kumene anthu angamfikire Yesu ndi zofunsa zawo? Yesu anayankha funsoli mwakuneneratu kuti poyembekezera kukhalapo kwake, padzauka a Kristu onama. Anachenjeza kuti: “Akanena kwa inu, Onani, iye [Kristu] ali m’chipululu; musamukeko. Onani, ali m’zipinda; musavomereze. Pakuti monga mphezi idzera kum’maŵa, niwonekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso [kukhalapo, NW] [pa·rou·siʹa] kwake kwa Mwana wa munthu.”—Mateyu 24:24, 26, 27.
-
-
Kuunikira Chidziŵitso pa Kukhalapo kwa KristuNsanja ya Olonda—1993 | May 1
-
-
10. Kodi ndimotani mmene mphezi za chowonadi cha Baibulo zang’animira kuŵalira dziko lonse lapansi?
10 Mosiyana nzimenezo, sipakakhala kubisa kulikonse pakufika kwa Yesu monga Mfumu, pakuyambika kwa kukhalapo kwake kwachifumu. Monga momwe Yesu ananeneratu, pamlingo wadziko lonse, mphezi za chowonadi cha Baibulo zikupitirizabe kung’anima moŵalira madera aakulu kuchokera ku mbali zakum’maŵa mpaka ku mbali zakumadzulo. Ndithudi, monga onyamula kuunika amakono, Mboni za Yehova zikutsimikizira kukhala “kuunika kwa amitundu, kuti . . . chipulumutso [cha Yehova chifike] ku malekezero a dziko lapansi.”—Yesaya 49:6.
-