Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/1 tsamba 5-10
  • “Kanthu Kalikonse Kali ndi Nthaŵi Yake”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kanthu Kalikonse Kali ndi Nthaŵi Yake”
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mphindi Yakugwa Misozi ndi Mphindi Yakuseka”
  • Ngakhale Tikulira, Ndifedi Achimwemwe!
  • “Mphindi Yakufungatirana ndi Mphindi Yakuleka Kufungatirana”
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kukwatira Ndiponso Kukhala ndi Ana M’nthawi Yamapeto Ino
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/1 tsamba 5-10

“Kanthu Kalikonse Kali ndi Nthaŵi Yake”

“Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.”​—MLALIKI 3:1.

1. Kodi anthu opanda ungwiro amalephera kuchitanji, ndipo zimenezi zapangitsa ena kutani nthaŵi zina?

NTHAŴI zambiri anthu amati, “Ndikanafulumira.” Mwinanso zinthu zitachitika kale iwo amati, “Ndikanangodikira.” Malingaliro ameneŵa akusonyeza kuti anthu opanda ungwiro amalephera kudziŵa nthaŵi yabwino yochitira zinthu zina. Kupereŵera kumeneku kwawonongetsa maunansi a anthu. Kwapangitsa ena kutaya chikhulupiriro mwa anthu ena ndiponso kwawagwiritsa mwala. Komanso choopsa kwambiri n’chakuti kwafooketsa chikhulupiriro cha anthu ena mwa Yehova ndi gulu lake.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani kuli kwanzeru kutsatira nthaŵi zoikidwiratu za Yehova? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi malingaliro abwino ati ponena za kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo?

2 Pokhala kuti Yehova ali ndi nzeru ndi kuzindikira kumene anthu alibe, iye atafuna amatha kudziŵiratu zotsatira za chochitika chilichonse. Amatha kudziŵa “chimaliziro kuyambira pachiyambi.” (Yesaya 46:10) Chotero, amatha kusankha mosalakwa nthaŵi yabwino kwambiri yochita chilichonse chimene akufuna kuchita. Chotero, m’malo moyendera kaonedwe kathu kolakwika ka nthaŵi, n’kwanzeru kutsatira nthaŵi zoikidwiratu za Yehova!

3 Mwachitsanzo, Akristu okhwima amadikira mokhulupirika nthaŵi imene Yehova waikiratu kuti maulosi ena a m’Baibulo adzakwaniritsidwe. Amakangalika muutumiki wake, panthaŵi yofananayo amakumbukira bwino lomwe nzeru ya pa Maliro 3:26 yakuti: “N’kokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.” (Yerekezani ndi Mika 7:7.) Panthaŵi imodzimodziyo, ali ndi chikhulupiriro chonse chakuti chiweruzo cholengezedwacho chimene Yehova adzapereka, ‘chikachedwa chidzafika ndithu, osazengereza.’​—Habakuku 2:3.

4. Kodi Amosi 3:7 ndi Mateyu 24:45 ayenera kutithandiza motani kudikira kwa Yehova moleza mtima?

4 Komanso, ngati sitikumvetsa malemba ena a m’Baibulo kapena mafotokozedwe opezeka m’zofalitsa za Watch Tower, kodi tiyenera kudandaula? N’kwanzeru kudikira nthaŵi imene Yehova waikiratu kuti nkhaniyo idzamveketsedwe bwino. “Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Lonjezotu lokhazika mtima pansi! Koma tikumbukire kuti Yehova amaulula chinsinsi chake panthaŵi imene iyeyo waiona kuti ndiyo yabwino. Kuti akwaniritse cholinga chimenecho Mulungu wapatsa mphamvu “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka kwa anthu ake ‘zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.’ (Mateyu 24:45) Ndiye chifukwa chake palibe chifukwa chokhalira nkhaŵa bi, mwina mpaka kusweka mtima, chifukwa chakuti nkhani zina sizinafotokozedwe mokwanira. M’malo mwake, tingakhale ndi chidaliro chakuti ngati tidikira kwa Yehova moleza mtima, iye adzapereka zofunikazo “panthaŵi yake” kudzera mwa kapolo wokhulupirika.

5. Kodi tidzapindulanji mwa kupenda Mlaliki 3:1-8?

5 Mfumu yanzeruyo Solomo inatchula zinthu 28, ndipo chilichonse mwa zinthu zimenezo chili ndi “nthaŵi yake.” (Mlaliki 3:1-8) Kumvetsa tanthauzo la zimene Solomo ananena ndi chimene zimasonyeza kudzatithandiza kudziŵa nthaŵi yabwino komanso nthaŵi yosayenera yochita zina ndi zina, malinga ndi mmene Mulungu amazionera. (Ahebri 5:14) Ndiyeno tikadziŵa, moyo wathu tidzaukonza moyenera.

“Mphindi Yakugwa Misozi ndi Mphindi Yakuseka”

6, 7. (a) N’chiyani chimapangitsa anthu odera ena nkhaŵa lerolino ‘kugwetsa misozi’? (b) Kodi dziko limayesa motani kupeŵa mkhalidwe woopsa umene lilimo?

6 Ngakhale kuti pali “mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka,” ndani angakonde kulira m’malo mwa kuseka? (Mlaliki 3:4) Koma n’zomvetsa chisoni kuti tikukhala m’dziko limene langodzaza zinthu zotipangitsa kulira. Nkhani zomvetsa chisoni zokhazokha n’zimene timamva panyuzi ndi kuziŵerenga m’manyuzipepala. Thupi limauma ndi mantha tikamamva zoti achinyamata ena aombera ana a sukulu anzawo kusukulu, za makolo ozunza ana awo, za zigaŵenga kuti zapha kapena kuvulaza zoopsa anthu osalakwa, ndiponso kuti masoka achilengedwe apha anthu ndi kusakaza zinthu. Ana anjala, owonda kwadzaoneni ndiponso anthu amene akuthaŵa kwawo chifukwa cha nkhondo ndi okhaokha amene timaona pawailesi yakanema. Mawu amene kumbuyoku anali osadziŵika kwenikweni monga akuti kuyeretsa fuko, AIDS, nkhondo ya zida zofalitsa tizilombo topereka matenda, ndi El Niño tsopano amatidetsa nkhaŵa​—alionse m’njira yakeyake.

7 N’zosachita kufunsa kuti lerolino dzikoli langodzaza masoka ndi zinthu zopweteketsa mtima. Komano, monga kuti zinthu sizinafike kale poipa, anthu opanga malonda a zosangalatsa amangosonyeza zinthu zopanda nzeru, zosasangalatsa zimenenso kaŵirikaŵiri zimakhala zachiwerewere ndi chiwawa, zokonzedwa kuti zitisocheze mwa kutipangitsa kunyalanyaza mavuto osaneneka amene ali ndi ena. Koma mzimu wosasamala za ena wongokonda nthabwala zopusa ndi phwete umene zosangalatsa zimenezi zimasonkhezera suyenera kuonedwa monga kuti ndicho chimwemwe chenicheni. Chimwemwe chimene chili chipatso cha mzimu wa Mulungu n’chinthu chimene dziko la Satana silingachipereke.​—Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 5:3, 4.

8. Kodi Akristu lerolino ayenera kutsogoza kugwetsa misozi kapena kuseka? Fotokozani.

8 Poona mmene dziko laipira, tikuonadi kuti lerolino si nthaŵi yotsogoza kuseka. Si nthaŵi yongokhalira maseŵera ndi zosangalatsa kapena yolola zosangalatsazo kukhala chinthu chofunika kwambiri kuposa kulondola zinthu zauzimu. (Yerekezani ndi Mlaliki 7:2-4.) “Iwo akuchita nalo dziko lapansi” akhale “monga ngati osachititsa,” anatero mtumwi Paulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW].” (1 Akorinto 7:31) Tsiku lililonse Akristu oona amakhala akuzindikira bwino lomwe kuti zinthu zafika poopsa m’nthaŵi zimene tikukhalamo ndi moyozi.​—Afilipi 4:8.

Ngakhale Tikulira, Ndifedi Achimwemwe!

9. Kodi ndi mkhalidwe womvetsa chisoni wotani umene unaliko m’masikuwo Chigumula chisanachitike, ndipo zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife lerolino?

9 Anthu amene analiko panthaŵi imene Chigumula chapadziko lonse chinachitika sanali kuona moyo monga momwedi unalili. Iwo ankangopitiriza zochita zawo zatsiku ndi tsiku osagwetsa misozi chifukwa cha “kuipa kwa anthu [kumene] kunali kwakukulu padziko lapansi,” ndipo ngakhale kuti “dziko lapansi . . . linadzala ndi chiwawa” iwo sizinali kuwakhudza. (Genesis 6:5, 11) Yesu anatchulapo za mkhalidwe womvetsa chisoni umenewo, ndipo ananeneratu kuti anthu adzakhalanso ndi malingaliro ofananawo m’tsiku lathu. Anachenjeza kuti: “Monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”​—Mateyu 24:38, 39.

10. Kodi Aisrayeli a m’masiku a Hagai anaonetsa motani kuti sanali kuzindikira nthaŵi zoikidwiratu za Yehova?

10 M’masiku a Hagai, zaka ngati 1,850 kuchokera pamene Chigumula chinachitika, Aisrayeli ambiri anaonetsanso kuti sanali kusamala za kufunika kwa zinthu zauzimu. Potanganitsidwa ndi kufuna kukhutiritsa zokhumba zawo, sanazindikire kuti nthaŵi yawo inali yofunika kuika zinthu za Yehova patsogolo. Timaŵerenga kuti: “Anthu aŵa anena, Nthaŵi siinafike, nthaŵi yakumanga nyumba ya Yehova. Pamenepo mawu a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Kodi imeneyi ndiyo nthaŵi yakuti inu nokha mukhala m’nyumba zanu zotchingidwa mkatimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka? Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu; Mtima wanu usamalire njira zanu.”​—Hagai 1:1-5.

11. Kodi ndi mafunso ati amene tingachite bwino kudzifunsa?

11 Monga Mboni za Yehova lerolino, okhala ndi ntchito ndi mwayi wofanana ndi wa Aisrayeli a m’nthaŵi ya Hagai, tingachitenso bwino kuti mtima wathu usamalire njira zathu, kuchita zimenezo mochokera pansi pa mtima. Kodi ‘timagwetsa misozi’ chifukwa cha mmene zinthu zilili m’dziko ndi chitonzo chimene zinthuzo zimadzetsa padzina la Mulungu? Kodi zimatipweteka mtima anthu akamati kulibe Mulungu kapena akamakaniratu kutsatira mapulinsipulo ake olungama? Kodi timachita monga momwe anachitira anthu olembedwa chizindikiro amene Ezekieli anaona m’masomphenya zaka 2,500 zapitazo? Ponena za anthu amenewo timaŵerenga kuti: “Yehova ananena [kwa mwamuna wokhala ndi zolembera], Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pamphumi zawo za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.”​—Ezekieli 9:4.

12. Kodi Ezekieli 9:5, 6 amatanthauzanji kwa anthu lerolino?

12 Kufunika kwa nkhani imeneyi kwa ife lerolino kumaoneka tikaŵerenga malangizo amene amuna asanu ndi mmodziwo okhala ndi zida zophera anapatsidwa kuti: “Pitani pakati pa mudzi kum’tsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo; iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika.” (Ezekieli 9:5, 6) Kuti tidzapulumuke chisautso chachikulu chimene chikuyandikira mofulumiracho zidzadalira pa kuzindikira kwathu kuti inoyi makamaka ndiyo nthaŵi yolira.

13, 14. (a) Kodi ndi anthu otani amene Yesu anati ndi achimwemwe? (b) Fotokozani chifukwa chake mukuganiza kuti mafotokozedwe ameneŵa amasonya kwa Mboni za Yehova.

13 Komatu ngakhale kuti atumiki a Yehova ‘akugwetsa misozi’ chifukwa cha mkhalidwe wodandaulitsa wa dziko lapansi zimenezi siziwaletsa kukhala achimwemwe. M’pang’ono pomwe! Iwotu ndiwo anthu achimwemwe koposa padziko lapansi. Yesu anapereka njira yodziŵira achimwemwe pamene anati: “Odala [“achimwemwe,” NW] ali osauka mumzimu; . . . achisoni; . . . akufatsa; . . . akumva njala ndi ludzu la chilungamo; . . . akuchitira chifundo; . . . oyera mtima; . . . akuchita mtendere; . . . akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo.” (Mateyu 5:3-10) Umboni wonse ulipo wosonyeza kuti mafotokozedwe ameneŵa akusonya kwa Mboni za Yehova, monga gulu, kuposa gulu lina lililonse lachipembedzo.

14 Makamaka kuyambira pamene kulambira koona kunabwezeretsedwa mu 1919, anthu a Yehova akhala ndi chifukwa chabwino kwambiri cha “kuseka.” Mwauzimu, anakhala ndi chisangalalo chonga chija cha awo amene anabwerera kuchokera ku Babulo m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E.: “Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; . . . Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.” (Salmo 126:1-3) Komabe, ngakhale kuti zikusekerera mwauzimu, Mboni za Yehova siziiŵala kuti nthaŵi zino n’zoipa. Dziko latsopano litadzakhazikika ndipo anthu padziko lapansi ‘atadzagwira moyo weniweniwo,’ m’pamene idzakhala nthaŵi yoti kulira kuloŵedwe m’malo ndi kusekerera kwamuyaya.​—1 Timoteo 6:19; Chivumbulutso 21:3, 4.

“Mphindi Yakufungatirana ndi Mphindi Yakuleka Kufungatirana”

15. N’chifukwa chiyani Akristu amasamala posankha mabwenzi?

15 Akristu amasamala posankha mabwenzi awo. Amakumbukira chenjezo la Paulo lakuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Ndipo mfumu yanzeruyo Solomo inati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”​—Miyambo 13:20.

16, 17. Kodi Mboni za Yehova zimaona motani kupalana ubwenzi, kucheza kwa mwamuna ndi mkazi osakwatirana, ndi ukwati, ndipo chifukwa chiyani?

16 Atumiki a Yehova amapalana ubwenzi ndi anthu amene amakonda Yehova ndi chilungamo monga iwo. Pamene kuli kwakuti amayamikira ndiponso amasangalala ndi ubwenzi wawo ndi anthu amenewo, iwo mwanzeru safuna kutengerako malingaliro olekerera momkitsa amene ali ofala kwambiri m’mayiko ena lerolino okhudza kucheza kwambiri pakati pa mwamuna ndi mkazi osakwatirana. M’malo mokuchita monga chosangalatsa wamba, iwo amakuona kukhala nkhani yaikulu yotsogolera kuukwati imene munthu ayenera kuichita pokhapokha atakhala wokonzekera mwakuthupi, m’maganizo, ndi mwauzimu​—komanso womasuka mwamalemba​—kuloŵa muukwati.​—1 Akorinto 7:36.

17 Ena amaganiza kuti kaonedwe koteroko ka kucheza ndi ukwati n’kachikale. Koma Mboni za Yehova sizilola malingaliro a ena kusonkhezera kasankhidwe kawo ka mabwenzi kapena zosankha zawo ponena za kucheza koteroko ndi ukwati. Zimadziŵa kuti “nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Nthaŵi zonse Yehova ndiye amadziŵa zonse, chotero Mboni zimatsatira mosamalitsa uphungu wake wonena za kukwatira kokha “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14) Zimapeŵa kuthamangira kuloŵa muukwati ndi maganizo akuti n’kotheka kusudzulana kapena kupatukana ngati ukwatiwo walephera, amene ali maganizo olakwika. Zimafatsa pofunafuna wokwatirana naye, podziŵa kuti akangopanga malumbiro a ukwati, lamulo la Yehovali limayamba kugwira ntchito: “Chotero kuti salinso aŵiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”​—Mateyu 19:6; Marko 10:9.

18. Kodi n’chiyani chimene chingakhale poyambira pa ukwati wachimwemwe?

18 Ukwati ndi mgwirizano wa moyo wonse umene umafuna kukonzekera bwino. Mwamuna ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi mkaziyu ndiyedi wondiyenera?’ Koma m’pofunikanso zedi kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndinedi womuyenera mkaziyu? Kodi ndine Mkristu wokhwima bwino amene ndingathe kusamalira zofunika zake zauzimu?’ Yehova amayembekeza ofuna kukwatiranawo onse aŵiri kukhala olimba mwauzimu, okhoza kumanga ukwati wolimba umene Mulungu amauvomereza. Mabanja achikristu zikwi zambiri angavomereze kuti chifukwa chakuti utumiki wa nthaŵi zonse umagogomezera kwambiri kupatsa m’malo mwa kulandira, uwo umakhala poyambira pabwino kwambiri pa ukwati wachimwemwe.

19. N’chifukwa chiyani Akristu ena ali paumbeta?

19 Akristu ena ‘safungatira’ mwa kusankha kukhala paumbeta chifukwa cha uthenga wabwino. (Mlaliki 3:5) Ena amakankhira nthaŵi yawo yoloŵa m’banja kutsogolo mpaka pamene adzafikire podzimva kuti ndi okhwima bwino mwauzimu moti n’kupeza mnzawo woyenerera. Komanso tisaiŵale Akristu amene ali paumbeta amene amakhumba ubwenzi wa muukwati ndi mapindu ake koma amene sakupeza okwatirana nawo. Tikudziŵa motsimikiza kuti Yehova amakondwera nawo akamakana kuswa mapulinsipulo aumulungu pamene akufunafuna mnzawo wa muukwati. Timachitanso bwino poyamikira kukhulupirika kwawo ndi kuwapatsa chilimbikitso chimene akufunikira.

20. N’chifukwa chiyani ngakhale anthu okwatirana ‘amaleka kufungatirana’ nthaŵi zina?

20 Kodi ngakhale okwatirana ayenera ‘kuleka kufungatirana’ nthaŵi zina? M’lingaliro lina zikuoneka choncho, popeza Paulo anati: “Ichi nditi, abale, yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe.” (1 Akorinto 7:29) Motero, kusangalatsa kwa ukwati ndi madalitso ake ziyenera kubwera pambuyo pa maudindo ateokalase nthaŵi zina. Kukhala wolinganizika pankhani imeneyi sikudzafooketsa ukwati koma kudzaulimbitsa chifukwa chakuti kumakumbutsa aŵiri okwatiranawo kuti nthaŵi zonse Yehova ndiye ayenera kukhala chinthu chofunika kwambiri cholimbitsa ukwati wawo.​—Mlaliki 4:12.

21. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza mabanja pankhani ya kukhala ndi ana?

21 Komanso, mabanja ena apeŵa kukhala ndi ana kuti akhale omasuka kwambiri pochita utumiki wawo kwa Mulungu. Iwo adzimana pochita zimenezi, ndipo Yehova adzawafupadi moyenerera. Komano, pamene kuli kwakuti Baibulo limalimbikitsa umbeta kaamba ka uthenga wabwino, ilo silitchulapo mwachindunji za kusakhala ndi ana pachifukwa chofananacho. (Mateyu 19:10-12; 1 Akorinto 7:38; yerekezani Mateyu 24:19 ndi Luka 23:28-30.) Chotero, mabanja ayenera kusankha choti achite malinga ndi mkhalidwe umene alimo ndi chikumbumtima chawo. Chosankha chilichonse chimene angasankhe, mabanja sayenera kuonedwa ngati olakwa.

22. Kodi n’kofunika kwa ife kudziŵa chiyani?

22 Inde, “kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” Palinso ngakhale “mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.” (Mlaliki 3:1, 8) Nkhani yotsatira idzafotokoza chifukwa chake kuli kofunika kwa ife kudziŵa kuti ino ndi nthaŵi iti mwa zinthu ziŵirizo.

Kodi Mungafotokoze?

◻ N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwa ife kudziŵa kuti “kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake”?

◻ N’chifukwa chiyani inoyi ndi “mphindi yakugwa misozi” makamaka?

◻ N’chifukwa chiyani Akristu alidi achimwemwe ngakhale kuti ‘akugwetsa misozi’?

◻ Kodi Akristu ena amaonetsa motani kuti nthaŵi ino amaiona kukhala “mphindi yakuleka kufungatirana”?

[Zithunzi pamasamba 6, 7]

Ngakhale kuti Akristu ‘akugwetsa misozi’ chifukwa cha mkhalidwe wa zinthu m’dziko . . .

. . . iwotu ndiwo anthu achimwemwe koposa padziko lapansi

[Chithunzi patsamba 8]

Utumiki wa nthaŵi zonse m’poyambira pabwino zedi pa ukwati wachimwemwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena