Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kulongosola Nkhani za Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Ndalama za Kristu
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
    • 6 “Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”—Mateyu 25:13-30.

      7. Kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi matalente?

      7 M’fanizo limeneli, kodi matalente amaimira chiyani? Chinthu chamtengo wapatali, osati m’lingaliro la ndalama, koma m’lingaliro lauzimu. Matalente amaimira lamulo la kukapanga ophunzira a Kristu lamulo limeneli limayendera limodzi ndi mwaŵi wapamwamba wa kukhala nthumwi za Kristu, Mfumuyo, kuimira Ufumuwo kumitundu yonse ya dziko.—Aefeso 6:19, 20; 2 Akorinto 5:20.

      8. (a) Kodi ndimumdima wotani umene kagulu ka kapolo “waulesi” kaponyedwamo mkati mwa ‘mapeto a dongosolo lino la zinthu’? (b) Kodi nchifukwa ninji dziko la mtundu wa anthu silikusangalala ndi kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso?

      8 Mosakaikira konse, ife lerolino tafika kumapeto kwa kukwaniritsidwa kwa fanizo lolosera limeneli! Pa mbadwo uno pafika nyengo ya mdima wa ndiwe yani kuposa mbiri yonse ya anthu! Ndithudi, kuli mdima waukulu kunja kwa mbali yowoneka ya gulu la Yehova kumene “kagulu ka kapolo waulesi” ndi “wopanda pake” kangaponyeredweko molamulidwa ndi Ambuye. “Mdima wakunja” umenewo umatanthauza mkhalidwe wa mdima wa anthu, makamaka m’lingaliro lachipembedzo. Anthu alibe kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso. Saali m’kuunika kwa kudziŵa Ufumu wa Mulungu. Likulamulidwa ndi “mulungu wanthaŵi ino ya pansi pano,” amene ‘wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawaŵalire.’—2 Akorinto 4:4.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena