Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991 | March 1
    • Mogwirizana ndi Mateyu 26:26 mu New World Translation, Yesu, pamene anayambitsa phwando la Mgonero wa Ambuye, imanena motere ponena za mkate umene akuupatsira kwa ophunzira ake: “Uwu utanthauza thupi langa.” Matembenuzidwe ena ambiri amamasulira vesili motere: “Uwu ndi thupi langa,” ndipo amagwiritsiridwa ntchito kuchirikiza chiphunzitso chakuti mkati mwa phwando la Mgonero wa Ambuye, mkatewo umakhala mnofu weniweni wa Kristu. Liwu lotembenuzidwa “utanthauza” (es·tinʹ, mtundu wa ei·miʹ) mu New World Translation limachokera ku liwu Lachigiriki lotanthauza “kukhala,” koma lingatanthauzenso “kutanthauza.” Chotero, Greek-English Lexicon of the New Testament ya Thayer imanena kuti mneni ameneyu “kaŵirikaŵiri amafanana ndi kusonyeza, kuzindikiritsa, kupereka lingaliro.” Ndithudi, liwu lakuti “utanthauza” ndilo matembenuzidwe anzeru panopa. Pamene Yesu anayambitsa Mgonero Wotsirizira, mnofu wake udalikobe ku mafupa ake, nangano ndimotani mmene mkatewo ukanakhalira mnofu wake weniweni?a

  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991 | March 1
    • a Pa Chibvumbulutso 1:20, wotembenuza Wachijeremani Curt Stage anamasulira mneni mmodzimodziyo motere: “Zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zimatanthauza [ei·sinʹ] mipingo isanu ndi iŵiriyo.” Fritz Tillmann ndi Ludwig Thimme mofananamo amalimasulira kukhala “kutanthauza” [es·tinʹ] pa Mateyu 12:7.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena