Kodi Ndani Amene Akutsatira Kuunika kwa Dziko?
“Mukuŵala monga zounikira m’dziko.”—AFILIPI 2:15, NW.
1. Kodi Baibulo limanenanji za mauniko onyenga achipembedzo?
BAIBULO limasonyeza Yesu momvekera bwino kukhala “kuŵala kwakukulu,” “kuunika kwa dziko.” (Yesaya 9:2; Yohane 8:12) Komabe, oŵerengeka okha ndiwo anamtsatira pamene anali pa dziko lapansi. Ochuluka anasankha kutsatira ounikira onyenga, amene kwenikweni, anali onyamula mdima. Ponena za ameneŵa Mawu a Mulungu amati: “Otero ali atumwi onyenga, ochita ochenjera, odziwonetsa ngati atumwi a Kristu. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adziwonetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adziwonetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.”—2 Akorinto 11:13-15.
2. Kodi Yesu anati nchiyani chikakhala maziko akuweruzira anthu?
2 Chotero, sianthu onse amene amafuna kuunika, chinkana kukhale kwabwino motani. Yesu anati: “Chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.”—Yohane 3:19, 20.
Okonda Mdima
3, 4. Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo m’tsiku la Yesu anasonyezera kuti sanafune kutsatira kuunika?
3 Talingalirani mmene zimenezo zinaliri choncho pamene Yesu anali pa dziko lapansi. Mulungu anali atapatsa Yesu mphamvu ya kuchita zozizwitsa zochititsa nthumanzi monga njira yotsimikizirira kuti anali Mesiyayo. Mwachitsanzo, pa tsiku la Sabata, anabwezeretsa kuwona kwa munthu wakhungu chibadwire. Nchochitika chodabwitsa chachifundo chotani nanga! Munthuyo anayamikira chotani nanga! Iye anakhoza kuwona kwa nthaŵi yoyamba! Komabe, kodi atsogoleri achipembedzo anachita motani? Yohane 9:16 amati: “Ena pamenepo mwa Afarisi ananena [za Yesu], Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.” Mitima yawo inali yoluluzika chotani nanga! Panopa kuchiritsa kozizwitsa kunali kutachitika, koma mmalo mwa kukondwerera munthu amene anali wakhunguyo ndi kuyamikira wochiritsayo, iwo anamtsutsa Yesu! Mwakutero, iwo mosakaikira anachimwira mzimu woyera wowonekerawo wa Mulungu, tchimo losakhululukidwa.—Mateyu 12:31, 32.
4 Pambuyo pake, pamene onyengawo anafunsa amene anali wakhungu za Yesu, mwamunayo anati: “Pakuti chozizwa chiri m’menemo, kuti inu simudziŵa kumene [Yesu] achokera, ndipo ananditsegulira maso anga. Tidziŵa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo. Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosawona chibadwire. Ngati uyu [Yesu] sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.” Kodi atsogoleri achipembedzo anachita motani? “Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m’zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.” Ndikupanda chifundo kotani nanga! Anali ndi mitima yonga miyala. Chotero Yesu anawauza kuti ngakhale kuti anali kuwona ndi maso awo akuthupi, anali akhungu mwauzimu.—Yohane 9:30-41.
5, 6. Kodi nchiyani chimene atsogoleri achipembedzo a m’zaka za zana loyamba anachita kusonyeza kuti anakonda mdima?
5 Chenicheni chakuti onyenga achipembedzo ameneŵa anali kuchimwira mzimu wa Mulungu chikuwonekera poyera pachochitika china, pamene Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa. Chifukwa cha chozizwitsacho, unyinji wa anthu wamba unakhulupirira Yesu. Komabe, tamverani zimene atsogoleri achipembedzo anachita. “Ansembe akulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka iye kotero, onse adzakhulupirira iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.” (Yohane 11:47, 48) Iwo anali kudera nkhaŵa ndi malo awo ndi kutchuka kwawo. Mosasamala kanthu za kutaikiridwa kulikonse, iwo anafuna kukondweretsa Aroma osati Mulungu. Chotero, kodi iwo anachitanji? “Kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe iye [Yesu].”—Yohane 11:53.
6 Kodi zinali zokhazo? Ayi. Zotsatirapo zimene anachita zinasonyeza mmene iwo anakondera mdima: “Ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso; pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.” (Yohane 12:10, 11) Nkuipa kwankhalwe kotani nanga! Ngakhale kuti anachita zonsezi kutetezera malo awo, kodi chinachitika nchiyani? Mkati mwa mbadwo umenewo, iwo anapandukira Aroma, amene anawaukira mu 70 C.E. nawalanda malo awo, mtundu, ndi miyoyo yawo yomwe!—Yesaya 5:20; Luka 19:41-44.
Chifundo cha Yesu
7. Kodi nchifukwa ninji okonda chowonadi amadza muunyinji kwa Yesu?
7 Zirinso motero m’nthaŵi yathu, sionse amene amafuna kuunikira kwauzimu. Koma awo amene amakonda chowonadi amafuna kudza ku kuunika. Amafuna Mulungu kukhala Mfumu yawo, ndipo mwachangu amatembenukira kwa Yesu, yemwe Mulungu watuma kufotokoza chimene kuunika kuli, ndi kumtsata. Ndizo zimene anthu odzichepetsa anachita pamene Yesu anali padziko lapansi. Anadza muunyinji wawo kwa iye. Ngakhale Afarisi anavomereza zimenezo. Iwo anadandaula kuti: “Onani dziko litsata pambuyo pake pa iye.” (Yohane 12:19) Anthu onga nkhosa anakonda Yesu chifukwa anali wosiyana ndi atsogoleri achipembedzo adyera, otukumuka, ndi okonda ulamuliro amene Yesu anati: “Amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapeŵa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo. Koma amachita ntchito zawo zonse kuti awonekere kwa anthu.”—Mateyu 23:4, 5.
8. Mosiyana ndi onyenga achipembedzo, kodi ndimkhalidwe wotani umene Yesu anali nawo?
8 Mosiyana, tawonani mkhalidwe wachifundo wa Yesu uwu: “Powona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Ndipo kodi anachitaponji? Iye anati kwa awo amene analimidwa pamsana ndi dongosolo la Satana: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Yesu anachita zimene zinanenedweratu ponena za iye pa Yesaya 61:1, 2, pamene pamati: “Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am’nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m’ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.”
Kusonkhanitsa Onyamula Kuunika
9. Kodi ndizochitika zazikulu zotani zimene zinachitika mu 1914?
9 Atakwera kumwamba, Yesu anali kudzayembekezera kufikira pamene nthaŵi ikafika yakuti Mulungu ampatse mphamvu ya Ufumu. Ndiyeno akalekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” (Mateyu 25:31-33; Salmo 110:1, 2) Nthaŵiyo inafika pamene “masiku otsiriza” anayamba mu 1914. (2 Timoteo 3:1-5) Yesu, wopatsidwa mphamvu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, anayamba kusonkhanitsira kudzanja lake lamanja lachiyanjo awo amene anafuna kutsatira kuunika. Pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I, ntchito yakusonkhanitsa imeneyo inachitika paliŵiro lowonjezereka.
10. Kodi ndifunso lotani limene lingafunsidwe ponena za awo amene Yesu akuwagwiritsira ntchito m’ntchito yosonkhanitsa?
10 Mwachitsogozo cha Kristu Yesu, ntchito yosonkhanitsa yafupidwa ndi chipambano chachikulu. Sizinachitikepo m’mbiri yonse kukhala ndi anthu ochuluka chotero ochokera m’mitundu yonse kusonkhanitsidwa m’kulambira kowona kounikiridwa. Ndipo kodi ndani lerolino amene akutsatira kuunika kochokera kwa Mulungu ndi Kristu? Ndani kodi amene akuchita zimene Afilipi 2:15 (NW) amanena, “kuŵala monga zounikira m’dziko,” kuitanira ena ‘kudza ndi kutenga madzi a moyo kwaulere’?—Chivumbulutso 22:17.
11. Kodi malo a Chikristu Chadziko ngotani pa nkhani ya kuunika kwauzimu?
11 Kodi Chikristu Chadziko chikuchita zimenezo? Chikristu Chadziko, limodzi ndi zipembedzo zake zosiyanasiyana, sichikuŵala konse monga chounikira. Kwenikweni, atsogoleri achipembedzo ali ofanana ndi atsogoleri achipembedzo a m’tsiku la Yesu. Iwo sakuŵalitsira kuunika kowona kochokera kwa Mulungu ndi Kristu. Zaka 33 zapitazo, magazini ya Theology Today inati: “Mwachisoni kuyenera kuvomereredwa kuti kuunika kumeneku sikukuŵala mwamphamvu m’Tchalitchi. . . . Tchalitchi chikupitiriza kukhala chofanana ndi zitaganya za anthu ochizinga. Sichili kwenikweni kuunika kwa dziko koma mmalo mwake chili chiŵalitsiro cha miyuni yadziko younikira m’dzikomo.” Ndipo mkhalidwe wa Chikristu Chadziko ulidi woipirapo lerolino. Kumene kumatchedwa kuunika koŵalitsira kuchokera kudziko ndiko mdima chifukwa ndizo zokha zimene Satana ndi dziko lake angapereke. Ayi, palibe kuunika kwa chowonadi kochokera m’zipembedzo zokangana zaudziko za Chikristu Chadziko.
12. Kodi ndani amene amapanga gulu lowona la onyamula kuunika lerolino?
12 Tinganene mwachidaliro kuti chitaganya cha dziko latsopano cha Mboni za Yehova ndicho gulu lowona, lonyamula kuunika lerolino. Mogwirizana, ziŵalo zake zonse—amuna, akazi, ndi achichepere omwe—amalola kuunika kwawo kochokera kwa Yehova ndi Kristu kuŵalira anthu onse. Chaka chatha, m’mipingo pafupifupi 70,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, onyamula kuunika oposa kwambiri mamiliyoni anayi anali okangalika kuuza ena za Mulungu ndi zifuno zake. Ndipo chaka chirichonse tsopano, tikuwona kusonkhanitsidwa kopitirizabe kwakukulu kwa anthu amenenso amafuna kuunikira kwauzimu. Zikwi mazana ambiri akubatizidwa ataphunzira Baibulo ndi kupeza chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi. Ndithudi, Mulungu “afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.”—1 Timoteo 2:4.
13. Kodi tingayerekezere kuunika kochokera kwa Yehova ndi chiyani?
13 Tingayerekezere kuunikira kumene tsopano kukuchokera kwa Yehova ndi zimene zinachitika pamene anthu a Mulungu a m’nthaŵi zakale anachoka mu Igupto: “Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m’njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwaŵalitsira; kuti ayende usana ndi usiku.” (Eksodo 13:21, 22) Mtambo wowatsogolera usana ndi moto usiku zinali zitsogozo zodalirika zochokera kwa Mulungu. Zinali zodalirika kwambiri mofanana ndi dzuŵa limene Mulungu analenga kutipatsa kuunika m’nthaŵi ya usana. Choteronso, tingathe kudalira pa Yehova kupitiriza kuunikira njirayo mwauzimu kwa ofunafuna chowonadi m’masiku oipa ano otsiriza. Miyambo 4:18 imatitsimikizira kuti: “Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.”
Kuŵalitsira Kuunika kwa Ufumu
14. Kodi nchiyani chiyenera kukhala chifuno chachikulu cha onyamula kuunika?
14 Ngakhale kuti Yehova ndiye Magwero a kuunikira, ndipo Kristu ali Woŵalitsira kuunika Wamkulu, otsatira a Yesu nawonso ayenera kuwalitsira kuunikako. Iye anati ponena za iwo: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. . . . Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuwona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:14, 16) Ndipo kodi mutu wankhani waukulu wa kuunikaku kumene otsatira ake akaunikira pa anthu unali wotani? Kodi akaphunzitsa chiyani pa kaindeinde wa mbiri ya dziko pamenepo? Yesu sadanene kuti otsatira ake akalalikira demokrase, ulamuliro wotsendereza, mgwirizano wa Tchalitchi ndi Boma, kapena mipangidwe ina iriyonse yaudziko. Mmalo mwake, pa Mateyu 24:14 (NW) iye adaneneratu kuti pakati pa chitsutso cha padziko lonse, “mbiri yabwino imeneyi yaufumu [ika]lalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse, ndipo pomwepo mapeto [aka]fika.” Chotero, onyamula kuunika lerolino amauza ena za Ufumu wa Mulungu, umene udzathetsa dziko la Satana ndi kubweretsa dziko latsopano lachilungamo.—1 Petro 2:9.
15. Kodi ofuna kuunika adzatembenukira kuti?
15 Awo okonda kuunika sadzanyengedwa ndi manenanena okopa a dzikoli ndi zonulirapo zake. Manenanena onsewo ndi zonulirapozo zidzafafanizidwa posachedwapa, popeza kuti dziko lino likuyandikira mapeto ake. Mmalo mwake, okonda chilungamo adzafuna kutembenukira ku mbiri yabwino imene ikulengezedwa ndi awo amene awalitsa kuunika kwa Ufumu wa Mulungu kufikira ngondya zakutali za dziko lapansi. Iwowo ndiwo onenedweratu pa Chivumbulutso 7:9, 10, kuti: “Ndinapenya, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu [wa Mulungu] ndi pamaso pa Mwanawankhosa [Kristu] . . . ndipo afuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” Vesi 14 limati: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Inde, iwo akupulumuka mapeto a dziko lino kuloŵa m’dziko latsopano losatha mu Ufumu wa Mulungu.
Dziko Latsopano Lounikiridwa
16. Kodi nchiyani chidzachitikira dziko la Satana pa chisautso chachikulu?
16 Dziko latsopano lidzakutidwa ndi kuunika koŵala kwa chowonadi. Ndithudi, talingalirani mmene mkhalidwewo udzakhalira tsikulo Mulungu atachotsa dongosolo lazinthu lino. Satana, ziŵanda zake, ndi madongosolo ake andale zadziko, azamalonda, achipembedzo adzachotsedwa—onse! Onse ndi zonse zimene Satana amagwiritsira ntchito kuperekera manenanena ake okopa zidzachoka nazonso. Chotero, pambuyo pa chisautso chachikulu, sipadzalembedwanso nyuzipepala iriyonse, magazini, buku, kabuku, kapena kapepala kalikonse kochilikiza dziko loipali. Sipadzakhala zisonkhezero zoluluza zoulutsidwa pa wailesi yakanema yaudziko kapena nyumba za mphepo za wailesi. Dongosolo lonse lakupha la dziko la Satana lidzachotsedwa mwakukanthidwa kamodzi basi!—Mateyu 24:21; Chivumbulutso 7:14; 16:14-16; 19:11-21.
17, 18. Kodi mungafotokoze motani mkhalidwe wauzimu pambuyo pa mapeto a dziko la Satana?
17 Ha, udzakhala mpumulo waukulu wotani nanga! Kuyambira patsikulo kumkabe mtsogolo, mtundu wa anthu udzasonkhezeredwa ndi kuunika kwabwino kokha kotsitsimula mwauzimu kochokera kwa Yehova ndi Ufumu wake. Yesaya 54:13 akuneneratu kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Popeza ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi, lonjezo lake nlakuti, monga momwe Yesaya 26:9 amanenera, “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.”
18 Mwamsanga, mkhalidwe wonse wamaganizo ndi wauzimu udzasintha kukhala wabwino kwambiri. Zinthu zolimbikitsa zidzakhala umoyo wa masiku onse mmalo mwa zinthu zochititsa tondovi za makhalidwe oipa zimene tsopano zili zowanda kwambiri. Aliyense wokhala ndi moyo panthaŵiyo adzaphunzitsidwa chowonadi chonena za Mulungu ndi zifuno zake. M’lingaliro lokwanira kotheratu, ulosi wa Yesaya 11:9 udzakwaniritsidwa, umene umati: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”
Tsatirani Kuunikako Mwamsanga
19, 20. Kodi nchifukwa ninji awo ofuna kutsatira kuunika afunikira kukhala maso?
19 Tsopanoli, m’zaka zomalizira za dongosolo loipa lino, nkofunika mwamsanga kutsatira kuunika kwa dziko. Ndipo tifunikira kukhala maso, chifukwa pali nkhondo yaikulu imene ikumenyedwa yotilepheretsa kuyenda m’kuunika. Chitsutsochi chikuchokera kwa olamulira amdima—kuchokera kwa Satana, ziŵanda zake, ndi gulu lake lapadziko lapansi. Nchifukwa chake mtumwi Petro akuchenjeza kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”—1 Petro 5:8.
20 Satana adzaika chopinga chirichonse m’njira ya obwera ku kuunika, kuti ayese kuwachititsa kupitirizabe kuyenda mumdima. Chingakhale chitsenderezo cha achibale kapena mabwenzi akale otsutsa chowonadi. Zingakhale zikaikiro ponena za Baibulo chifukwa cha kuchititsidwa khungu maganizo ndi ziphunzitso za chipembedzo chonyenga kapena manenanena onyenga a osakhulupirira mwa zinthu zosawoneka ndi osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu ndi okaikira kukhalapo kwa Mulungu. Mwina zikhoterero zochimwa za munthu nzimene zingakuchititse kukhala kovuta kuti akwaniritse zofuna za Mulungu.
21. Kodi onse ofuna kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu ayenera kuchitanji?
21 Mosasamala kanthu za zopinga zimene zingakhalepo, kodi mufuna kusangalala ndi moyo m’dziko latsopano lopanda umphaŵi, upandu, chisalungamo, ndi nkhondo? Kodi mufuna kukhala ndi thanzi langwiro ndi moyo wamuyaya pa dziko lapansi laparadaiso? Pamenepo landirani Yesu ndi kumtsata monga kuunika kwa dziko ndi kumvetsera uthenga wa awo amene akugwira zolimba pa “mawu a moyo” ndi amene ‘akuŵala monga zounikira za dziko.’—Afilipi 2:15, 16, NW.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi atsogoleri achipembedzo amasonyeza motani kuti amakonda mdima?
◻ Kodi ndimkhalidwe wotani umene Yesu anali nawo kulinga kwa anthu?
◻ Kodi kusonkhanitsidwa kwa onyamula kuunika kwapitiriza motani?
◻ Kodi ndimasinthidwe aakulu otani amene adzachitika posachedwapa?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika mwamsanga kutsatira kuunika kwa dziko lerolino?
[Chithunzi pamasamba 14, 15]
Afarisi ouma mtima anataya kunja munthu amene Yesu anamtsegulira maso