Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ndi Ndani Amene Amalalikira Uthenga Wabwino?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 21. Munthu akuyankhulana ndi a Mboni za Yehova awiri omwe akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala.

      PHUNZIRO 21

      Ndi Ndani Amene Amalalikira Uthenga Wabwino?

      Posachedwapa, Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa mavuto onse amene tikukumana nawo. Uthenga umenewu ndi wosangalatsa kwambiri ndipo aliyense ayenera kuumva. Yesu ankafuna kuti otsatira ake azilalikira uthenga umenewu kwa wina aliyense. (Mateyu 28:​19, 20) Kodi a Mboni za Yehova amachita zotani pomvera lamulo la Yesu?

      1. Kodi lemba la Mateyu 24:14 likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?

      Yesu ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mateyu 24:14) A Mboni za Yehova amasangalala kugwira ntchito yofunika kwambiri imeneyi. Timalalikira uthenga wabwino padziko lonse m’zinenero zoposa 1,000. Ntchitoyi ndi yaikulu kwambiri. Ndipo imafunika kuigwira mwakhama komanso mwadongosolo. Komabe sitingakwanitse kuigwira patokha popanda kuthandizidwa ndi Yehova.

      2. Kodi timachita zotani kuti tilalikire anthu?

      Timalalikira kwina kulikonse kumene tingapeze anthu. Mofanana ndi Akhristu a m’nthawi ya atumwi, timalalikira “kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42) Njira imeneyi, imatithandiza kuti tizilalikira anthu mamiliyoni ambiri chaka chilichonse. Popeza nthawi zina anthu ena sapezeka pakhomo, timalalikiranso m’malo opezeka anthu ambiri. Timayesetsa kugwiritsa ntchito mwayi ulionse kuti tiuze ena zokhudza Yehova ndiponso zimene amafuna.

      3. Ndi ndani amene ali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino?

      Mkhristu woona aliyense ali ndi udindo wolalikira uthenga wabwino. Timaona kuti udindo umenewu ndi wofunika kwambiri. Timalalikira mulimonse mmene tingathere chifukwa timadziwa kuti miyoyo ya anthu ili pangozi. (Werengani 1 Timoteyo 4:16.) Sitilandira malipiro alionse tikamagwira ntchitoyi, chifukwa Baibulo limati: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:​7, 8) Ngakhale kuti anthu ena amakana uthenga wathu sitisiya kulalikira chifukwa kugwira ntchitoyi ndi mbali ya kulambira kwathu ndipo imasangalatsa Yehova.

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zimene a Mboni za Yehova amachita kuti alalikire padziko lonse komanso mmene Yehova amawathandizira.

      A. A Mboni za Yehova awiri akulalikira kwa munthu wina m’dera lamapiri ku Costa Rica. B. A Mboni za Yehova akulalikira kwa asodzi padoko lina ku United States. C. A Mboni za Yehova awiri akulalikira m’mudzi wina ku Benin. D. Mayi wina wa Mboni akulalikira kwa munthu wina m’boti logulitsiramo malonda ku Thailand. E. A Mboni za Yehova awiri akulalikira kwa mzimayi wina ataima pafupi ndi miyala yaikulu yoboola pakati ku Yap. F. A Mboni za Yehova awiri akulalikira kwa mzimayi wina pamsewu wina kunja kuli sinowo ku Sweden.

      Kulalikira padziko lonse: (A) Costa Rica, (B) United States, (C) Benin, (D) Thailand, (E) Yap, (F) Sweden

      4. Timachita khama kuti tilalikire anthu a mitundu yonse

      A Mboni za Yehova amachita khama kuti akalalikire anthu kulikonse komwe ali. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:

      VIDIYO: Kulalikira Mpaka “Kumalekezero a Dziko Lapansi” (7:33)

      • N’chiyani chimene chikukuchititsani chidwi mukaganizira khama limene a Mboni za Yehova amachita kuti alalikire anthu?

      Werengani Mateyu 22:39 ndi Aroma 10:13-15, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi ntchito yathu yolalikira imasonyeza bwanji kuti timakonda anthu?

      • Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amalalikira uthenga wabwino?​—Onani Aroma 10:15.

      5. Ndife antchito anzake a Mulungu

      Zimene zimachitika tikamagwira ntchito yolalikira ndi umboni wakuti Yehova amatsogolera ntchito yathu. Chitsanzo ndi zimene zinachitikira m’bale wina wa ku New Zealand, dzina lake Paul. Tsiku lina akulalikira kunyumba ndi nyumba chakumadzulo, anakumana ndi mayi wina. M’mawa wa tsikuli, mayiyu anali atapemphera kwa Mulungu pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova ndipo anamupempha kuti amutumizire munthu woti adzamulalikire. Ndiyeno M’bale Paul anati: “Patangopita maola atatu ndinafika pakhomo la mayiyu.”

      Werengani 1 Akorinto 3:9, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi chitsanzo cha ku New Zealand chikusonyeza bwanji kuti Yehova ndi amene amatsogolera ntchito yolalikira?

      Werengani Machitidwe 1:8, kenako mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani timafunikira thandizo la Yehova kuti tigwire bwino ntchito yathu yolalikira?

      Kodi mukudziwa?

      Mlungu uliwonse, pamsonkhano wamkati mwa mlungu, timaphunzira mmene tingagwirire ntchito yolalikira. Ngati munapangapo misonkhanoyi, kodi mukuona kuti maphunziro amenewa ndi othandizadi?

      A Mboni za Yehova awiri akuchita chitsanzo cha mmene angalalikirire pamsonkhano wampingo.

      6. Timamvera lamulo la Mulungu lakuti tizilalikira

      Mu nthawi ya atumwi, anthu otsutsa ankauza otsatira a Yesu kuti asiye kulalikira. Komabe, Akhristuwa anateteza ufulu wawo wolalikira mwa “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.” (Afilipi 1:7) Ndi zimenenso a Mboni za Yehova amachita masiku ano.a

      Onerani VIDIYO.

      VIDIYO: Timateteza Mwalamulo Uthenga Wabwino (2:28)

      Werengani Machitidwe 5:27-42, kenako mukambirane funso ili:

      • N’chifukwa chiyani sitingasiye kugwira ntchito yolalikira?​—Onani vesi 29, 38 ndi 39.

      MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amalalikira kunyumba ndi nyumba?”

      • Kodi mungamuyankhe bwanji?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Yesu analamula otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yonse. Yehova amathandiza anthu ake akamagwira ntchito imeneyi.

      Kubwereza

      • Ndi ndani amene amalalikira uthenga wabwino padziko lonse?

      • Kodi ntchito yathu yolalikira imasonyeza bwanji kuti timakonda anthu?

      • Kodi mukuona kuti ntchito yolalikira ingatithandize kukhala osangalala? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Onani zimene a Mboni za Yehova amachita polalikira m’mizinda ikuluikulu.

      Ntchito Yapadera Yolalikira M’malo Opezeka Anthu Ambiri ku Paris 5:11

      Kodi a Mboni za Yehova achitapo zotani pothandiza anthu othawa kwawo?

      Kuthetsa Ludzu Lauzimu la Anthu Othawa Kwawo 5:59

      Onani mmene kugwira ntchito yolalikira nthawi zonse kunathandizira munthu wina kukhala wosangalala.

      Ndimasangalala Kuti Ndinasankha Kutumikira Yehova 6:29

      Dziwani zokhudza milandu yofunika kwambiri imene tawinapo yomwe yathandizira kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ipite patsogolo.

      “Olalikira Ufumu Anayamba Kupititsa Milandu Yawo Kukhoti” (Ufumu wa Mulungu Ukulamulira!, mutu 13)

      a A Mboni za Yehovafe sitifunikira kupempha chilolezo cha munthu kuti tigwire ntchito yolalikira chifukwa Mulungu ndi amene anatilamula kuti tizigwira ntchitoyi.

  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Phunziro 23. Mzimayi akubatizidwa kuti akhale wa Mboni za Yehova ndipo wachita kuviikidwa thupi lonse m’madzi.

      PHUNZIRO 23

      Ubatizo Ungakuthandizeni Kukhala Ndi Tsogolo Labwino

      Yesu anaphunzitsa kuti Akhristu ayenera kubatizidwa. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Koma kodi ubatizo n’chiyani? Nanga munthu ayenera kuchita chiyani kuti abatizidwe?

      1. Kodi ubatizo n’chiyani?

      Mawu akuti “batiza” amachokera ku mawu a Chigiriki amene amatanthauza kuviika m’madzi. Pamene Yesu ankabatizidwa, thupi lake lonse linamizidwa mumtsinje wa Yorodano ndipo kenako ‘anavuuka m’madzimo.’ (Maliko 1:9, 10) Mofanana ndi Yesu, masiku ano Akhristu akamabatizidwa, thupi lawo lonse limaviikidwa kapena kumizidwa m’madzi.

      2. Kodi ubatizo ndi chizindikiro cha chiyani?

      Munthu akabatizidwa, amasonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova Mulungu. Koma kodi munthu amadzipereka bwanji? Asanabatizidwe, amapemphera kwa Yehova payekha n’kumuuza kuti akufuna kumutumikira kwa moyo wake wonse. Amalonjeza Yehova kuti azilambira Iye yekha, komanso kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake ndi kuchita zimene Yehova amafuna. Iye amasankha ‘kudzikana yekha ndi . . . kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa ndi kuchita mosalekeza.’ (Mateyu 16:24) Kudzipereka komanso kubatizidwa kumamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso Akhristu anzake.

      3. Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti abatizidwe?

      Musanabatizidwe, muyenera kuphunzira zokhudza Yehova komanso kuyamba kumukhulupirira kwambiri. (Werengani Aheberi 11:6.) Mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso kumukhulupirira, m’pamenenso mudzayambe kumukonda kwambiri. Kenako mudzayamba kufuna kulalikira zokhudza Yehova komanso kuchita zimene Iye amafuna pa moyo wanu. (2 Timoteyo 4:2; 1 Yohane 5:3) Munthu akangoyamba ‘kuyenda mogwirizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti azimukondweretsa pa chilichonse,’ amasankha kupereka moyo wake kwa Mulungu kenako amabatizidwa.​—Akolose 1:9, 10.a

      FUFUZANI MOZAMA

      Onani zomwe tingaphunzire pa ubatizo wa Yesu komanso zomwe munthu angachite pokonzekera ubatizo.

      4. Zimene tikuphunzira pa ubatizo wa Yesu

      Werengani Mateyu 3:​13-17 kuti mudziwe zomwe zinachitika pa ubatizo wa Yesu. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • Kodi Yesu anabatizidwa ali wakhanda?

      • Kodi pamene ankamubatiza, anachita kungomuwaza madzi?

      Yesu atangobatizidwa, anayamba kugwira ntchito yapadera yomwe Mulungu anamutuma padzikoli. Werengani Luka 3:21-23 ndi Yohane 6:38, kenako mukambirane funso ili:

      • Yesu atabatizidwa, kodi ndi ntchito iti yomwe ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri pa moyo wake?

      5. N’zotheka kukwaniritsa cholinga chanu choti mubatizidwe

      Poyamba mukhoza kuchita mantha mukaganizira za kudzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa. Komabe, mukapitiriza kuphunzira zambiri zokhudza Yehova, n’kufika pomudziwa bwino, mantha akhoza kutheratu ndipo mungakwanitse cholinga chofunika kwambiri chimenechi. Kuti muone anthu ena amene anakwanitsa kuchita zimenezi, onerani VIDIYO.

      VIDIYO: Mungatani Kuti Yehova Akhale Mnzanu? (1:11)

      Werengani Yohane 17:3 ndi Yakobo 1:5, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi munthu angatani kuti akonzekere kubatizidwa?

      A. Mzimayi akudzipereka kwa Yehova kudzera m’pemphero. B. Mzimayi yemwe uja akubatizidwa kuti akhale wa Mboni za Yehova ndipo wachita kuviikidwa thupi lonse m’madzi.
      1. Timadzipereka kwa Yehova pomuuza m’pemphero kuti tikufuna kumutumikira kwa moyo wathu wonse

      2. Pa tsiku la ubatizo timasonyeza anthu kuti tinadzipereka kwa Mulungu

      6. Tikabatizidwa timakhala m’banja la Yehova

      Tikabatizidwa, timakhala m’banja logwirizana lapadziko lonse. Ngakhale kuti timasiyana kochokera ndi zikhalidwe timakhulupirira zinthu zofanana ndiponso timayendera mfundo zamakhalidwe abwino zofanana pa moyo wathu. Werengani Salimo 25:14 ndi 1 Petulo 2:​17, kenako mukambirane funso ili:

      • Mogwirizana ndi mavesiwa, kodi ubatizo umathandiza bwanji munthu?

      Zithunzi: Mlongo wobatizidwa akuganizira madalitso amene akusangalala nawo chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino Akhristu anzake mumpingo. Akufotokozera mlongo wina nkhawa zake. 2. Akuthandiza mlongo wachikulire kuyenda. 3. Waitanira chakudya anzake amisinkhu yosiyanasiyana. 4. Akulalikira bambo wina limodzi ndi mlongo wina. 5. Ali kumsonkhano ndi anzake ndipo akudzijambula.

      ZIMENE ENA AMANENA: “Ndidzabatizidwabe m’tsogolomu chifukwa ndikuopa kuchotsedwa ndikalakwitsa.”

      • Ngati inunso mukuganiza choncho, kodi mukuona kuti mukufunika kuyesetsabe kuti mubatizidwe?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Yesu anaphunzitsa kuti Akhristu ayenera kubatizidwa. Munthu amene akufuna kubatizidwa, ayenera kukhulupilira kwambiri Yehova, kuyendera mfundo za Yehova pa moyo wake ndiponso kudzipereka kwa Yehova.

      Kubwereza

      • Kodi ubatizo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anthu amayenera kubatizidwa?

      • Kodi kudzipereka ndi kubatizidwa n’zogwirizana bwanji?

      • Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu ayenera kuchita asanafike podzipereka komanso kubatizidwa?

      Zolinga

      ONANI ZINANSO

      Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene ubatizo umatanthauza.

      “Kodi Ubatizo N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)

      Onani zimene munthu ayenera kuchita kuti afike pobatizidwa.

      “Munthu Amabatizidwa Chifukwa Chokonda Yehova Komanso Kumuyamikira” (Nsanja ya Olonda, March 2020)

      Werengani nkhaniyi kuti muone mmene munthu wina anasankhira kubatizidwa chifukwa chomvetsa bwino mfundo za m’Baibulo.

      “Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2013)

      Onani chifukwa chake ubatizo ndi wothandiza komanso zomwe mungachite kuti mufike pobatizidwa.

      “Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?” (Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, mutu 37)

      a Munthu ayenera kubatizidwanso ngakhale kuti anabatizidwa kale ku chipembedzo china. Tikutero chifukwa chipembedzocho sichinamuthandize kudziwa choonadi cha m’Baibulo.​—Onani Machitidwe 19:1-5 ndi Phunziro 13.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena