Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Tizitchula Zinthu Ziti Tikamapemphera kwa Mulungu?
    Galamukani!—2012 | February
    • Yesu ananena kuti: “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’”—Mateyu 6:9-13.

  • Kodi Tizitchula Zinthu Ziti Tikamapemphera kwa Mulungu?
    Galamukani!—2012 | February
    • “Ufumu wanu ubwere.” Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Iye posachedwapa adzayamba kulamulira dziko lonse lapansi. Lemba la Danieli 7:14 limanena kuti “anamupatsa ulamuliro, ulemerero, ndi ufumu.” Ufumu wa Mulungu ‘udzabwera’ kuti uphwanye maboma onse a anthu n’kuyamba kulamulira dziko lonse.—Danieli 2:44.

      “Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, anthu onse azidzachita chifuniro cha Mulungu. Ndipo chifukwa cha zimenezi, padziko lonse padzakhala mtendere ndipo anthu onse azidzalambira Mulungu m’njira yoyenera. Zinthu zimene zimachititsa anthu kuti asamagwirizane, monga ndale ndi chipembedzo chonyenga, sizidzakhalaponso. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limanena mophiphiritsa kuti “Chihema cha Mulungu” chidzakhala “pakati pa anthu.” Lembali limapitiriza kuti: “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena