Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Nthaŵi zina timamva abale akulankhula kapena kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze padziko lapansi. Kodi kunenaku nkolondola?
Kwenikweni, kumeneku sikuli njira ya Malemba yofotokozera zinthu. Ufumu wa Mulungu ngwakumwamba. Nchifukwa chake, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kuloŵa ufumu wake wakumwamba; kwa iye ukhale ulemerero ku nthaŵi za nthaŵi. Amen.”—2 Timoteo 4:18; Mateyu 13:44; 1 Akorinto 15:50.
Ufumuwo unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, ndipo sudzasamutsidwira konse pa Paradaiso wa padziko lapansi wobwezeretsedwa kapena kwina kulikonse. Yesu Kristu ndiye Mfumu ya Ufumuwo. Monga Mfumu, Yesu ali ndi ulamuliro pa angelo. Chotero, malo ake oyenera a ulamuliro ndiwo kudzanja lamanja la Mulungu kumwamba. Akristu odzozedwa amagwirizana naye monga mafumu ndi ansembe kumwamba.—Aefeso 1:19-21; Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6.
Ndiyeno, kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitiyenera kutchulanso kwa Mulungu mawu opempha opezeka m’mawu a Pemphero la Ambuye limene limati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano”? (Mateyu 6:10) Mosiyana ndi zimenezo, pemphero limenelo nloyenera ndipo nlodzalabe ndi tanthauzo.
Ufumu wa Mulungu udzachitapo kanthu m’njira yotsimikizirika padziko lapansili, ndipo izi nzimene timakumbukira pamene tipemphera ndi kugwiritsira ntchito mafotokozedwe ofanana ndi mawu a m’Pemphero la Ambuye. Mwachitsanzo, Danieli 2:44 amaneneratu kuti Ufumuwo ‘udzadza’ kudzawononga mitundu yonse ndipo udzatenga ulamuliro wadziko lapansili. Chivumbulutso 21:2 chimanena za Yerusalemu Watsopano wotsika kuchokera kumwamba. Yerusalemu Watsopano ngwopangidwa ndi Akristu odzozedwa 144,000 amene adzakhala mkwatibwi wa Kristu. Iwo alinso oloŵa malo anzake a Yesu mu Ufumuwo. Chotero Chivumbulutso 21:2 chimafotokoza za chisamaliro chawo kulinga ku dziko lapansi, limodzi ndi madalitso aakulu operekedwa kwa anthu.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Mpaka pamene izi ndi maulosi ena ochititsa chidwi adzakwaniritsidwa, kudzapitirizabe kukhala koyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu mogwirizana ndi mawu a Yesu, “Ufumu wanu udze.” Koma tiyenera kukumbukira kuti Ufumuwo sudzabwera pa pulaneti la Dziko Lapansi m’lingaliro lenileni. Boma la Ufumu limakhala kumwamba, osati padziko lapansi.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Dziko Lapansi: Chozikidwa pa chithunzi cha NASA