Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 2/1 tsamba 32
  • “Maluŵa a Kuthengo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Maluŵa a Kuthengo”
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 2/1 tsamba 32

“Maluŵa a Kuthengo”

ULOVA. Kukwera kwa mitengo. Umphaŵi. Vuto lachuma. Mawu ameneŵa amawonekera mwakaŵirikaŵiri koposa m’malipoti anyuzi. Ndipo iwo amasonyeza mavuto amene anthu mamiliyoni ambiri amayang’anizana nawo pamene akuyesayesa kudyetsa ndi kuveka mabanja awo ndi kuŵapezera malo okhala.

Okhulupirira ndi osakhulupirira omwe akuyambukiridwa. Koma okhulupirira samasiidwa okha kuyang’anizana ndi mavuto amenewo. Yesu, polankhula kwa anthu wamba a m’zaka za zana loyamba, anati: ‘Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?’​—Mateyu 6:26.

Yesu anatinso: ‘Tapenyetsani maluŵa a kuthengo, makulidwe awo; sagwiritsa ntchito, kapena sapota; koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavala monga limodzi la ameneŵa. Koma ngati Mulungu aveka chotero maudzu a kuthengo, . . . si inu kopambana ndithu?’​—Mateyu 6:28-30.

Kodi izi zitanthauza kuti Mkristu safunikira kugwira ntchito kuti apeze zomchirikiza? Kutalitali! Mkristu amagwira ntchito zolimba kwambiri monga momwe kungafunikire kuti alipirire ngongole zake. Mtumwi Paulo anati: ‘Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.’ (2 Atesalonika 3:10) Komabe, Mkristu amazindikira chisamaliro chachikondi cha Mulungu ndipo ali ndi chikhulupiriro chakuti Atate wake wa kumwamba akumuyang’anira. Chotero, iye samatayikiridwa ndi kukhazikika kwake ndi nkhaŵa za moyo. Ngakhale m’nthaŵi zovuta, iye amayika zinthu zoyamba​—zinthu zauzimu​—poyamba. Iye amakhulupirira mawu a Yesu akuti: ‘Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezeredwa kwa inu.’​—Mateyu 6:33.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena