Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • 15, 16. Fotokozani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawalalikira.

      15 Mu 31 C.E., patatha zaka pafupifupi ziwiri akuchita mwakhama utumiki wake, Yesu anawonjezera utumikiwu poyamba “ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse” ya ku Galileya. Zimene anaona zinamukhudza kwambiri. Mtumwi Mateyu anafotokoza kuti: “Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mateyu 9:35, 36) Yesu ankamvera chisoni anthu wamba ndipo ankadziwa bwino kwambiri kuti sankasamalidwa mwauzimu. Yesu ankadziwanso kuti atsogoleri achipembedzo, amene anayenera kuweta anthuwa, sankawasamalira n’komwe koma ankangowazunza. Choncho Yesu anagwidwa ndi chifundo ndipo ankayesetsa mwakhama kuti alalikire anthuwo uthenga wopatsa chiyembekezo. Panalibe chinthu chabwino chimene anthuwo ankafunikira kuposa kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • 18 Tiziona anthu ngati mmene Yesu ankawaonera. Iye ankawaona kuti anali “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” Mwachitsanzo, yerekezerani kuti mwapeza kamwana kankhosa katasochera. Kamwana kankhosako kali ndi njala komanso ludzu chifukwa palibe m’busa woti akatsogolere kumene kuli msipu ndi madzi. Kodi simungakamvere chisoni? Kodi simungayesetse kuchita zonse zimene mungathe kuti mukapatse chakudya ndi madzi? Kamwana kankhosako kali ngati anthu ambiri amene sanamvebe uthenga wabwino. Abusa a zipembedzo zonyenga sakuthandiza anthu awo ndipo anthuwo ali ndi njala komanso ludzu lauzimu moti alibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo. Koma ifeyo tili ndi chilichonse chimene iwo angafune. Tili ndi chakudya chauzimu chopatsa thanzi ndiponso madzi otsitsimula a choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Yesaya 55:1, 2) Tikamaganizira njala yauzimu imene anthu amenewa ali nayo, timawamvera chisoni kwambiri. Mofanana ndi Yesu tikamamvera anthu chisoni tidzayesetsa kuwauza uthenga wa Ufumu wopatsa chiyembekezo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena