Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988 | January 1
    • 15. (a) Ndi malangizo otani amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake pamene iye anawatumiza kunja kukalalikira? (b) Ndimotani mmene ochitira ndemanga Baibulo ena alongosolera ichi?

      15 Pamene Yesu anatumiza ophunzira ake kukalalikira, iye anawatumizanso mwachindunji kwa anthu. Ichi chikuwonedwa m’malangizo ake olembedwa pa Mateyu 10:1-15, 40-42. Mu versi 11 iye ananena kuti: “Ndipo m’mzinda uli wonse, kapena m’mudzi, mukalowamo, mufunitsitse amene ali woyenera momwemo, ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.” The Jerusalem Bible imaika versi iri motere: “Funsani kaamba ka winawake amene ali wokhulupirika,” ngati kuti ophunzirawo anafunikira kufunsa anthu ena otchuka kapena odziŵika m’mudziwo kupeza ndani amene anali ndi kukambidwa kwabwino ndipo chotero anali oyenera uthengawo. (Onaninso Weymouth ndi King James Version.) Ndipo aka ndi kalongosoledwe kamene ochitira ndemanga a Baibulo ena amapereka ku versi 11.

  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988 | January 1
    • 17. Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti ophunzira a Yesu sanali kokha kuitanira pa anthu oyenerera kuzikidwa pa kuyamikiridwa kapena kuikidwa?

      17 Ichi chikuwoneka m’mawu a Yesu pa Mateyu 10:14: “Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.” Yesu anali kulankhula ponena za ophunzira ake akupanga maulendo osaitanidwa pa anthu kulalikira kwa iwo. Zowona, iwo akayeneranso kulandira malo ogona ndi mmodzi wa eninyumba yemwe akavomereza ku uthengawo. (Mateyu 10:11) Koma chinthu chachikulu chinali ntchito yolalikira. Pa Luka 9:6 chanenedwa kuti: “Ndipo iwo anatuluka, napita m’midzi m’midzi, ndi kulalikira uthenga wabwino, ndi kuchiritsa ponse.” (Onaninso Luka 10:8, 9.) Oyenerera omwe analandira ophunzirawo m’nyumba zawo monga aneneri, mwinamwake kuwapatsa iwo “chikho cha madzi ozizira” kapena ngakhale malo ogona, sadakataya mphoto yawo. Iwo adakamva uthenga wa Ufumu.​—Mateyu 10:40-42.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena