-
Anawakonzekeretsa Kuti Azilalikira Ngakhale Pamene AkuzunzidwaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Yesu anapatsa atumwi ake, omwe anawagawa awiriawiri, malangizo abwino kwambiri ogwirira ntchito yolalikira. Koma atawapatsa malangizowo anawachenjezanso kuti pogwira ntchito yolalikirayo akakumana ndi anthu otsutsa. Iye anawachenjeza kuti: “Taonani! Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu. . . . Chenjerani ndi anthu, pakuti adzakuperekani kumakhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge awo. Inde, adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.”—Mateyu 10:16-18.
-
-
Anawakonzekeretsa Kuti Azilalikira Ngakhale Pamene AkuzunzidwaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
Kunena zoona Yesu anachenjeza, kulimbikitsa komanso kupereka malangizo abwino kwambiri kwa atumwi ake 12. Malangizo amene Yesu anapereka nthawi imeneyi anali othandizanso kwa anthu amene anali kudzagwira ntchito yolalikirayi Yesu atafa komanso ataukitsidwa. Tikutero chifukwa Yesu anauza ophunzira ake kuti “anthu onse adzadana nanu” osati anthu okhawo amene atumwiwa ankawalalikira. Ndipotu Baibulo silifotokoza zoti pa nthawi imene atumwiwa ankalalikira ku Galileya anthu anawatengera kwa mabwanamkubwa ndi mafumu kapena kuti anaperekedwa ndi achibale awo kuti aphedwe.
Choncho, n’zoonekeratu kuti pamene Yesu ankapereka malangizo amenewa kwa atumwi ake ankanena zimene zidzachitike m’tsogolo. Kumbukiraninso kuti anauza ophunzira ake kuti sadzamaliza kuzungulira mizinda yonse akugwira ntchito yolalikirayi “Mwana wa munthu asanafike.” Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti ophunzira ake sadzamaliza kulalikira za Ufumu wa Mulungu, Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu asanabwere monga woweruza.
-