Kodi Nchiyani Chimakusonkhezerani Kutumikira Mulungu?
“Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.”—MARKO 12:30.
1, 2. Kodi ndi zinthu zosangalatsa zotani zimene zikuchitidwa ndi ntchito yolalikira?
UBWINO weniweni wa galimoto sumadalira kweniweni pa maonekedwe ake. Penti wake angakongoletse maonekedwe ake akunja, ndipo mpangidwe wake waluso ungakope munthu wofuna kugula; koma chimene chili chofunika kwambiri ndicho zinthu zimene sizimaonekera kunja—injini imene imayendetsa galimoto, limodzi ndi ziŵiya zina zonse zimene zimalichititsa kuyenda bwino.
2 Ndi mmenenso wakhalira utumiki wa Mkristu kwa Mulungu. Mboni za Yehova zimakhala ndi ntchito zaumulungu zochuluka. Chaka chilichonse, maola oposa biliyoni imodzi amawonongeredwa pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndiponso, maphunziro a Baibulo mamiliyoni ambiri amachititsidwa, ndipo amene amabatizidwa amafika zikwi mazana ambiri. Ngati ndinu mlengezi wa uthenga wabwino, mwakhala ndi phande—ngakhale kuti lingaoneke kukhala laling’ono—m’ziŵerengero zosangalatsa zimenezi. Ndipo khalani wotsimikiza kuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”—Ahebri 6:10.
3. Kuwonjezera pa ntchito, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chofunika kwambiri kwa Akristu, ndipo nchifukwa ninji?
3 Komabe, ubwino weniweni wa utumiki wathu—kaya wa tonse pamodzi kapena wa mmodzi ndi mmodzi—sumadalira kwenikweni pa ziŵerengero. Kuli monga momwe Samueli anauzidwira kuti, “munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Inde, chimene ife tili mkati mwathu ndicho chili kanthu kwa Mulungu. Zoona, ntchito nzofunika. Ntchito za kudzipereka kwaumulungu zimakometsa chiphunzitso cha Yehova ndi kukopa amene angakhale ophunzira. (Mateyu 5:14-16; Tito 2:10; 2 Petro 3:11) Komabe, ntchito zathu sizimapereka chithunzi chonse. Yesu woukitsidwayo anali ndi chifukwa chodera nkhaŵa mpingo wa ku Efeso—mosasamala kanthu za ntchito zawo zabwino. “Ndidziŵa ntchito zako,” anatero kwa iwo. “Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.”—Chivumbulutso 2:1-4.
4. (a) Kodi ndimotani mmene ntchito yathu kwa Mulungu ingakhalire monga ntchito wamba? (b) Kodi nchifukwa ninji pali kufunika kwa kudzipenda?
4 Pali ngozi pamenepa. M’kupita kwa nthaŵi, utumiki wathu kwa Mulungu ungakhale monga ntchito wamba. Mkazi wina Wachikristu anafotokoza zimenezo motere: “Ndinali kumapita mu utumiki, kupita ku misonkhano, kuphunzira, kupemphera—koma zonsezo ndinangozichita monga chizoloŵezi chabe, popanda kukhudzidwa mtima kulikonse.” Zoona, atumiki a Mulungu ayenera kuyamikiridwa pamene ayesayesa zolimba mosasamala kanthu za kumva kwawo kukhala “ogwetsedwa” kapena “ogonekedwa pansi.” (2 Akorinto 4:9; 7:6, NW) Komabe, pamene kachitidwe kathu ka zinthu Kachikristu kakhala chizoloŵezi wamba, tiyenera kusuzumira mu injini ya galimoto lathu, titero kunena kwake. Ngakhale galimoto zabwino koposa zimafunikira kukonzedwa panthaŵi ndi nthaŵi; mofananamo, Akristu onse afunikira kudzipenda nthaŵi zonse. (2 Akorinto 13:5) Anthu ena akhoza kuona ntchito zathu, koma sangadziŵe chimene chimasonkhezera machitidwe athu. Chifukwa chake, aliyense wa ife ayenera kusinkhasinkha pa funso lakuti: ‘Kodi chimene chimandisonkhezera kutumikira Mulungu nchiyani?’
Zopinga Chisonkhezero Choyenera
5. Kodi ndi lamulo liti limene Yesu anati linali loyamba pa onse?
5 Pamene anafunsidwa kuti pamalamulo opatsidwa kwa Israyeli ndi liti limene linali loyamba pa onse, Yesu anagwira mawu lamulo limene linasonyeza chisonkhezero cha mkati, osati maonekedwe akunja: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:28-30) Motero Yesu anasonyeza chimene chiyenera kukhala chisonkhezero cha utumiki wathu kwa Mulungu—chikondi.
6, 7. (a) Kodi ndimotani mmene Satana mwamachenjera waukira banja, ndipo nchifukwa ninji? (2 Akorinto 2:11) (b) Kodi kaleredwe kangayambukire motani mkhalidwe wa maganizo wa munthu kulinga ku ulamuliro waumulungu?
6 Satana amafuna kufooketsa nyonga yathu ya kukulitsa mkhalidwe wofunika wa chikondi. Kuti iye achite zimenezi, imodzi ya njira zimene wagwiritsira ntchito ndiyo kuukira banja. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’banja ndi mmene malingaliro okhalitsa kwambiri a chikondi amakhwimira. Satana amadziŵa bwino lomwe lamulo la Baibulo lakuti chimene chaphunziridwa paubwana chingakhale chothandiza pauchikulire. (Miyambo 22:6) Iye amayesa mwamachenjera kusokoneza lingaliro lathu la chikondi pausinkhu waung’ono. Monga “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Satana amaona kuti zifuno zake zikuchitidwa pamene ambiri akulira m’nyumba zosakhala malo a chikondi koma mabwalo a nkhondo za chidani, mkwiyo, ndi minyozo.—2 Akorinto 4:4; Aefeso 4:31, 32; 6:4; Akolose 3:21.
7 Buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe limasonyeza kuti njira imene tate amachitira ntchito yake yaukholo ‘ingathe kukhala ndi chiyambukiro chapadera pa kaimidwe ka maganizo ka ana pambuyo pake kulinga ku ulamuliro, ponse paŵiri waumunthu ndi waumulungu.’a Mwamuna wina Wachikristu amene analeredwa ndi tate wankhanza anavomereza kuti: “Kwa ine, kumvera Yehova nkosavuta; kumkonda ndiko kovuta kwambiri.” Zoona, kumvera nkofunika, pakuti kwa Mulungu “kumvera ndiko kokoma koposa nsembe.” (1 Samueli 15:22) Koma kodi nchiyani chingatithandize kuchita zoposa kumvera chabe kuti tikulitse chikondi chathu kwa Yehova monga chisonkhezero cha kulambira kwathu?
“Chikondi cha Kristu Chitikakamiza”
8, 9. Kodi nsembe yadipo ya Yesu iyenera kusonkhezera motani chikondi chathu pa Yehova?
8 Chisonkhezero chachikulu kopambana chokulitsira chikondi cha mtima wonse kwa Yehova ndicho chiyamikiro cha nsembe yadipo ya Yesu Kristu. “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Pamene takazindikira ndi kukayamikira, kachitidwe kachikondi kameneka kamatikakamiza kusonyeza chikondi nafenso. “Tikonda ife, chifukwa anayamba [Yehova] kutikonda.”—1 Yohane 4:19.
9 Yesu anavomereza ndi mtima wonse ntchito yake yotumikira monga Mpulumutsi wa anthu. “Umo tizindikira chikondi, popeza iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife.” (1 Yohane 3:16; Yohane 15:13) Chikondi chodzipereka nsembe cha Yesu chiyenera kusonkhezera chiyamikiro mwa ife. Mwachitsanzo: Tinene kuti mwapulumutsidwa kumira pamadzi. Kodi mudzangochoka ndi kupita kunyumba, kukadzipukuta, ndi kuiŵala zonse? Ndithudi ayi! Mudzamva kukhala wamangawa kwa munthu wokupulumutsaniyo. Ndi iko komwe, mulidi wamangawa kwa munthuyo chifukwa cha moyo wanu. Kodi mangawa athu kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu saposa pamenepo? Popanda dipolo, aliyense wa ife akanamira mu uchimo ndi imfa, titero kunena kwake. M’malo mwake, chifukwa cha kachitidwe kachikondi chachikulu kameneka, tili ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi laparadaiso.—Aroma 5:12, 18; 1 Petro 2:24.
10. (a) Kodi ndimotani mmene tingapangire dipo kukhala lathulathu? (b) Kodi chikondi chimene Kristu ali nacho chimatikakamiza motani?
10 Sinkhasinkhani pa dipolo. Lioneni kukhala loperekedwera inuyo panokha, monga momwe Paulo anachitira: “Moyo umene ndili nawo tsopano m’thupi, ndili nawo m’chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agalatiya 2:20) Kusinkhasinkha koteroko kudzadzutsa chisonkhezero chokhudza mtima, pakuti Paulo analembera Akorinto kuti: “Chikondi cha Kristu chitikakamiza; popeza . . . adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) The Jerusalem Bible imanena kuti chikondi cha Kristu “chimatikhudza mtima.” Pamene tisinkhasinkha pa chikondi cha Kristu, timakakamizika, kusonkhezereka kwambiri, kukhudzika mtima kwenikweni. Chimakhudza mitima yathu ndi kutisonkhezera kuchitapo kanthu. Zili monga momwe matembenuzidwe a J. B. Phillips amaikira m’mawu ake kuti, “maziko enieni a machitidwe athu ndiwo chikondi cha Kristu.” Chisonkhezero cha mtundu wina uliwonse sichingabale zipatso zokhalitsa mwa ife, monga momwe chitsanzo cha Afarisi chinasonyezera.
“Yang’anirani Mupeŵe Chotupitsa Mkate cha Afarisi”
11. Fotokozani mmene Afarisi anaonera ntchito zachipembedzo.
11 Afarisi anachotsamo mzimu wake wonse m’kulambira Mulungu. M’malo mwa kugogomezera kukonda Mulungu, anagogomezera ntchito kukhala muyeso wopimira mkhalidwe wauzimu wa munthu. Kusamalira kwambiri malamulo ocholoŵana kunawachititsa kuoneka kukhala olungama mwa maonekedwe akunja, koma mkati anali ‘odzala . . . ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.’—Mateyu 23:27.
12. Yesu atachiritsa munthu, kodi ndimotani mmene Afarisi anasonyezera kuuma mtima kwawo?
12 Panthaŵi ina Yesu mwachifundo anachiritsa mwamuna wina amene dzanja lake linali lopuwala. Mwamunayo ayenera kuti anakondwera chotani nanga pamene anachiritsidwa kamodzi nkamodzi nthenda imene mosakayikira inali yovutitsa ndi yosautsa maganizo! Komabe, Afarisiwo sanakondwere naye. M’malo mwake, anapeza mlandu pa kachitidwe chabe—kuti Yesu anapereka thandizo pa Sabata. Posamalira kwambiri mamasuliridwe awo a Chilamulo oyang’ana pa zinthu wamba, Afarisiwo analephereratu kuona mzimu wa Chilamulo. Nchifukwa chake Yesu ‘anamva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo’! (Marko 3:1-5) Ndiponso, iye anachenjeza ophunzira ake kuti: “Yang’anirani mupeŵe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.” (Mateyu 16:6) Machitidwe ndi maganizo awo akuvumbulidwa m’Baibulo kuti atipindule.
13. Kodi tikutengapo phunziro lotani pa chitsanzo cha Afarisi?
13 Chitsanzo cha Afarisi chimatiphunzitsa kuti tiyenera kukhala ndi kaonedwe koyenera ka ntchito. Ndithudi, ntchito nzofunika, pakuti “chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.” (Yakobo 2:26) Komabe, anthu opanda ungwiro ali ndi chizoloŵezi cha kuweruza ena pa zimene amachita m’malo mwa zimene ali. Nthaŵi zina, tingadziweruze ife eni mwa njira imeneyo. Tingasamalire kwambiri za kachitidwe ka zinthu, monga ngati kuti ndiwo muyeso wopimira mkhalidwe wathu wauzimu. Tingaiŵale kufunika kwa kupenda zolinga zathu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 5:12.) Tingakhale osamalira malamulo mokhwimitsa mosalolera amene ‘akuntha udzudzu, koma ngamila ameza,’ osamalira cholembedwa cha lamulo ndi kuswa cholinga chake.—Mateyu 23:24.
14. Kodi ndimotani mmene Afarisi analiri monga chikho kapena mbale yakuda?
14 Chimene Afarisi sanadziŵe nchakuti ngati Munthu akondadi Yehova, machitidwe a kudzipereka kwaumulungu adzangotsatira mwachibadwa. Mkhalidwe wauzimu umachokera mkati ndi kutulukira kunja. Yesu anadzudzula Afarisi mwamphamvu kaamba ka kalingaliridwe kawo kolakwa pamfundo imeneyi, akumati: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkatimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka mkati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.”—Mateyu 23:25, 26.
15. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yesu amayang’ana zoposa maonekedwe chabe.
15 Maonekedwe akunja a chikho, mbale, kapena ngakhale nyumba samavumbula zonse. Ophunzira a Yesu anachita chidwi ndi kukongola kwa kachisi wa Yerusalemu, amene Yesu anamutcha “phanga la achifwamba” chifukwa cha zimene zinali kuchitika mkati mwake. (Marko 11:17; 13:1) Mmene kachisiyo analili ndi mmenenso alili odzitcha Akristu, monga momwe mbiri ya Dziko Lachikristu imasonyezera. Yesu ananena kuti adzaweruza ena amene anachita “zamphamvu zambiri” m’dzina lake kukhala “akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Mosiyana kwambiri ndi amenewo, iye anati za mkazi wamasiye amene anapereka ndalama yochepetsetsa mtengo pakachisi: “Mkazi wamasiye amene waumphaŵi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo . . . Anaponya mwa kusoŵa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.” (Marko 12:41-44) Kodi kunali kuŵeruza kokondera? Kutalitali. M’mikhalidwe yonse iŵiriyo, Yesu anasonyeza lingaliro la Yehova. (Yohane 8:16) Anaona zimene zinasonkhezera ntchitozo naweruza malinga ndi zimenezo.
“Kwa Iwo Onse Monga Nzeru Zawo”
16. Kodi nchifukwa ninji sitimafunikira nthaŵi zonse kumayerekezera ntchito zathu ndi za Mkristu mnzathu?
16 Ngati zolinga zathu zili zoyenera, palibe kufunika kwa kumayerekezerana nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, sikupindula kwenikweni kuyesayesa mwampikisano kuwonongera nthaŵi mu utumiki yofanana ndi mmene Mkristu wina amachitira kapena kufuna kulinganiza ndi zimene winayo amakwaniritsa mu ulaliki. Yesu anati kukonda Yehova ndi mtima wanu wonse, maganizo, moyo, ndi mphamvu—osati za munthu wina. Maluso a munthu aliyense, nyonga, ndi mikhalidwe zimasiyana. Ngati mkhalidwe wanu ulola, chikondi chidzakusonkhezerani kuwonongera nthaŵi yochuluka mu utumiki—mwinamwake monga mtumiki wa upainiya wa nthaŵi yonse. Komabe, ngati mukulimbana ndi matenda, nthaŵi imene mudzawonongera mu utumiki ingakhale yochepera pa imene mungakhumbe. Musalefuke. Kukhulupirika kwa Mulungu sikumapimidwa ndi maola. Pokhala ndi zolinga zoyenera, mudzakhalabe osangalala. Paulo analemba kuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”—Agalatiya 6:4.
17. M’mawu anuanu, simbani mwachidule fanizo la matalente.
17 Talingalirani za fanizo la Yesu la matalente, lolembedwa pa Mateyu 25:14-30. Munthu amene anali pafupi kuyenda ulendo wakutali anaitanitsa akapolo ake nawaikiza chuma chake. “Mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo.” Kodi mbuyeyo anapezanji pamene anabwera kudzaŵerengera chuma ndi akapolo ake? Kapolo amene anapatsidwa matalente asanu anapindulanso ena asanu. Mofananamo, kapolo amene anapatsidwa matalente aŵiri anapindulanso ena aŵiri. Kapolo amene anapatsidwa talente limodzi analikwirira pansi ndipo sanachite nayo kalikonse kuti awonjezere chuma cha mbuyake. Kodi mbuyeyo anauona motani mkhalidwewo?
18, 19. (a) Kodi nchifukwa ninji mbuyeyo sanayerekezere kapolo wopatsidwa matalente aŵiri kwa kapolo wopatsidwa matalente asanu? (b) Kodi fanizo la matalente limatiphunzitsa chiyani za kuyamikira ndi kuyerekezera? (c) Kodi nchifukwa ninji kapolo wachitatu anapatsidwa chiweruzo choipa?
18 Choyamba, tiyeni tipende za kapolo amene anapatsidwa matalente asanu ndiyeno amene anapatsidwa aŵiri. Kwa aliyense wa akapoloŵa, mbuyeyo anati: “Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika.” Kodi iye akananena zimenezi kwa kapolo wa matalente asanu akanapindula aŵiri okha? Osati kwenikweni! Ndiyenonso, kwa kapolo amene anapindula matalente aŵiri sananene kuti: ‘Nchifukwa ninji sunapindule asanu? Ona kuchuluka zimene kapolo mnzako wandipindulira!’ Ayi, mbuye wachifundoyo, amene anachitira chithunzi Yesu, sanayerekezere. Anagaŵira matalentewo “kwa iwo onse monga nzeru zawo,” ndipo sanayembekezera zoposa zimene aliyense anakhoza kubwezera. Akapolo aŵiriwo analandira chiyamikiro cholingana, pakuti onse anagwira ntchito ndi mtima wonse kwa mbuyawo. Tonsefe tingatengepo phunziro pamenepa.
19 Ndithudi, kapolo wachitatu sanayami kiridwe. Ndipo iye anaponyedwa kunja kumdima. Pokhala analandira talente limodzi chabe, sakanayembekezeredwa kubwezera zochuluka mofanana ndi kapolo wa matalente asanu. Komabe, iye sanayeseko nkomwe! Anapatsidwa chiweruzo choipa makamaka chifukwa cha mtima wake “woipa ndi waulesi,” umene unasonyeza kupanda kwake chikondi kwa mbuyake.
20. Kodi Yehova amaona motani zopereŵera zathu?
20 Yehova amafuna kuti aliyense wa ife amkonde iye ndi mphamvu yake yonse, komabe nkotonthoza mtima chotani nanga kuti “adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi”! (Salmo 103:14) Miyambo 21:2 imati “Yehova ayesa mitima”—osati ziŵerengero. Amazindikira kupereŵera kulikonse kumene tilibepo mphamvu, kaya kwa chuma, kuthupi, maganizo, kapena kwina kulikonse. (Yesaya 63:9) Panthaŵi imodzimodzi, iye amafuna kuti tiyesetse kugwiritsira ntchito zonse zimene tingakhale nazo. Yehova ali wangwiro, koma pochita ndi alambiri ake opanda ungwiro, samafuna ungwiro kwa iwo. Sali wosalolera m’zochita zake ndipo samayembekezera zosatheka.
21. Ngati utumiki wathu kwa Mulungu usonkhezeredwa ndi chikondi, kodi padzakhala zotulukapo zabwino zotani?
21 Kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu “kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.” (Marko 12:33) Ngati tisonkhezeredwa ndi chikondi, pamenepo tidzachita zonse zimene tingathe mu utumiki wa Mulungu. Petro analemba kuti ngati mikhalidwe yaumulungu, kuphatikizapo chikondi, ‘ikakhala ndi inu, ndipo ikachuluka, idzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.’—2 Petro 1:8.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kupenda
◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kusonkhezera utumiki wathu kwa Mulungu?
◻ Kodi chikondi cha Kristu chimatikakamiza motani kutumikira Yehova?
◻ Kodi ndi kusamala chiyani kwa Afarisi kumene tiyenera kupeŵa?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kosayenera kumayerekezera nthaŵi zonse utumiki wathu ndi wa Mkristu wina?
[Zithunzi patsamba 16]
Maluso, nyonga, ndi mikhalidwe zimasiyana kwa munthu aliyense