Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuitanira Anthu ku Chakudya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Iye ananena kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo ndipo anaitana anthu ambiri. . . . Anatumiza kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Tiyeni, chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ Koma onse mofanana anayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda, choncho ndiyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kufika!’ Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kufika!’ Komanso wina anati, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sindingathe kubwera.’”—Luka 14:16-20.

      Zifukwazi zinali zosamveka. Munthu amakaona munda kapena ng’ombe asanagule. Choncho n’zosamveka kuti azikaona zinthuzi atazigula kale. Munthu wachitatuyu sankakonzekera zokwatira. Anali atakwatira kale ndiye chimenechi sichinali chifukwa chokanira. Wokonza phwandoyo atamva zifukwazo anakwiya kwambiri ndipo anauza kapolo wakeyo kuti:

  • Kuitanira Anthu ku Chakudya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Zimene Yesu anafotokozazi zinasonyeza kuti Yehova Mulungu anamupatsa udindo woitana anthu kuti adzalowe mu Ufumu wakumwamba. Anthu oyamba kuitanidwa anali Ayuda omwe anali atsogoleri achipembedzo. Koma atsogoleri ambiri anakana mwayi umenewu pa nthawi yonse imene Yesu ankalalikira. Ndiyeno mwayi umenewu unaperekedwanso kwa anthu ena. Zimene Yesu ananena m’fanizo lija zinasonyeza kuti m’tsogolo padzaperekedwanso mwayi woti anthu ena alowe mu Ufumu ndipo anthu ake ndi Ayuda wamba komanso anthu omwe anatembenukira ku Chiyuda. Kenako mwayi wachitatu komanso womaliza udzaperekedwa kwa anthu amene Ayuda ankawaona kuti ndi osafunika pamaso pa Mulungu.—Machitidwe 10:28-48.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena