Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 4/15 tsamba 29
  • Kodi Mumakumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumakumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mudzapindula Kuchokera ku Mapangano a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mapangano Ophatikizapo Chifuno Chosatha cha Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • ‘Mudzakhala Ufumu wa Ansembe’
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Madalitso Aakulu Kudzera m’Pangano Latsopano
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 4/15 tsamba 29

Kodi Mumakumbukira?

Kodi mwapeza makope a posachedwapa a Nsanja ya Olonda kukhala a phindu logwira ntchito kwa inu? Kenaka nchifukwa ninji osayesa chikumbukiro chanu ndi zotsatirazi?

◻ Nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene iye ananena kuti palibe aliyense angakhale wophunzira wake kusiyapo ngati ‘ada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde moyo wake womwe wa iyemwini’? (Luka 14:26)

Yesu sanatanthauze kukti mmodzi wa atsatiri ake ayenera kuda kwenikweni achibale ake kapena moyo wake weniweni. M’malomwake, iye anatanthauza kuti wophunzira afunikira kukonda ena kapena moyo wake weniweniwo mochepera ndi mmene amakondera Yesu.​—1/1, tsamba 8.

◻ Ndi ziti zomwe ziri nsonga zitatu zazikulu zomwe zathandizira ku chipambano cha ntchito ya Mboni ya umishonale, yapapitapo ndi ya lerolino?

Imodzi iri kugwirizana kwaumwini ndi anthu panyumba zawo. Ina iri uthenga wa Ufumu wachindunji ndi wopepuka wozikidwa pa Baibulo. Yachitatu iri chikondi chonga cha Kristu chosonyezedwa ndi amishonale m’kuchita ndi anthu.​—1/1, tsamba 14.

◻ Nchifukwa ninji Mulungu anawonjezera mosakhalitsa pangano la Chilamulu ku pangano la Abrahamu?

Pangano la Chilamulo linatsimikizira kuti Aisrayeli anali ochimwa ofunikira wansembe wa nthaŵi zonse ndi nsembe yangwiro. Linachirikiza mzere wa Mbewu ndi kuthandiza kuzindikiritsa amene Mbewuyo inali. Ilo linasonyezanso kuti tsiku lina Mulungu akakhala ndi mtundu wa mafumuansembe.​—2/1, tsamba 16.

◻ Kodi ndi ati omwe ali mapangano opita patsogolo asanu ndi aŵiri aumulungu otsogolera ku madalitso osatha kaamba ka tonsefe?

Pangano la mu Edeni, pangano la Abrahamu, pangano la Chilamulo, pangano la kukhala ndi wansembe wofanana ndi Melikizedeke, pangano la Ufumu wa Davide, pangano latsopano, ndi pangano la Ufumu.​—2/1, tsamba 19.

◻ Kodi zikwi za kusiyana mu mamanusikripiti a Baibulo zimafooketsa kudzinenera kwa Baibulo kukhala Mawu a Mulungu?

Ayi. Ophunzira Baibulo amatiwuza kuti chifupifupi kusiyana konse kumeneku kuli kwa kufunika kochepera ku lembalo. Iko kumatumikira kokha kulimbitsa kutsimikizira kwa kuwona kwa Malemba. (Salmo 119:105; 1 Petro 1:25)​—2/1, masamba 29, 30.

◻ Ndi kuchokera ku chiyani kumene liwu lakuti “osadziŵa” likutengedwa, ndipo nkimotani mmene likugwiritsidwira ntchito m’Baibulo?

“Osadziŵa” likutengedwa kuchokera ku liwu la Chigriki a’gno·stos, lomwe limatanthauza “chosadziŵika.” Paulo anagwiritsira ntchito mkhalidwe wa ilo m’kulankhula kwake kwa Aatene pamene analozera ku guwa lansembe lachikunja loperekedwa “Kwa Mulungu Wosadziŵika.” (Machitidwe 17:23)​—2/15, tsamba 5.

◻ Ndimotani mmene tiyenera kuchitira pamene chilozero china cha Malemba chingawonekere kukhala chotseguka ku malingaliro osiyana?

Tifunikira kusonyeza kuvomereza kodzichepetsa komwe kunasonyezedwa ndi Akristu oyambirira, kulandira zigamulo ndi zitsogozo zochokera ku mpingo wa Mulungu. (Machitidwe 15:6-29)​—2/15, tsamba 20.

◻ Nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene ananena kuti: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m’mahema osatha”? (Luka 16:9)

Tiyenera kukhala akhama m’kugwiritsira ntchito chuma chirichonse chomwe tiri nacho kuchirikiza zikondwerero za Ufumu ndipo mwakutero kulimirira ubwenzi ndi Yehova ndi Mwana wake. Iwo ali okhawo omwe angapereke malo kaamba ka ife m’mwemba kapena pa dziko lapansi la paradaiso pamene chuma chakuthupi chilephera kapena chitha.​—3/1, tsamba 9.

◻ Ndi zinthu zitatu ziti zomwe zikufunikira ku mbali yathu ngati titi tipindule kuchokera ku chidziŵitso chimene Yehova akuchipanga kukhalapo?

Tiyenera kuyamikira gulu la Yehova; tiyenera kuphunzira mokhazikika Mawu a Mulungu ndi zithandizo zomwe zaperekedwa, zomwe zimatitheketsa ife kumvetsetsa ilo; ndipo tiyenera kusinkhasinkha pa zimene taphunzira ndi mmene tingagwiritsire ntchito zimenezi m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.​—3/15, tsamba 14.

◻ Nchifukwa ninji anthu a Israyeli wakale anachita ndi kusoweka kwa chidziŵitso kokulira koteroko?

Iwo analephera kusinkhasinkha moyamikira pa zinthu zimene Yehova anachita kaamba ka iwo. (Salmo 106:7, 13)​—3/15, tsamba 17.

◻ Nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi “ankhondo apakavalo” olankhulidwa pa Chibvumbulutso 9:16?

Akavalo ophiphiritsira amenewa amaimira osati kokha otsalira a odzozedwa omazimiririka komanso “khamu lalikulu” lomakulakula ndi lamphamvu la “nkhosa zina.” (Chibvumbulutso 7:9; Yohane 10:16)​—4/1, tsamba 19.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena