Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Perekani Kaamba ka Mtsogolo ndi Nzeru Yothandiza
YESU wangotsiriza kumene kusimba nkhani ya mwana wolowerera ku khamu lomwe likuphatikiza ophunzira ake, osonkhetsa msonkho osawona mtima ndi ochimwa ena ozindikiridwa, ndi alembi ndi Afarisi. Tsopano, akulankhula kwa ophunzira ake, iye akusimba fanizo lonena za munthu wolemera yemwe wangolandira mbiri yosamukomera ponena za woyang’anira wa nyumba yake, kapena kapitawo.
Mogwirizana ndi Yesu, munthu wolemerayo akuitana kapitawo wake ndi kumuwuza iye kuti adzamuchotsa ntchito. “Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitawo?” kapitawoyo akudabwa. “Kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Ndidziŵa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene adzanditulutsa mu ukapitawo, anthu akandilandire kunyumba kwawo.”
Kodi nchiyani chomwe chiri nzeru ya kapitawoyo? Chabwino, iye akuitana awo omwe ali m’ngongole kwa mbuye wake. “Unakongola chiyani kwa mbuye wanga?” iye akufunsa tero.
‘Mitsuko ya mafuta a azitona malita 2,200,’ woyambirira akuyankha tero.
‘Tenga kalata wako nukhale pansi msanga nulembere, 1,100,’ iye akumuwuza tero.
Iye afunsanso winawake: ‘Ndipo iwe uli nawo mangawa otani?’
‘Mitanga ya tirigu malita 22,000,’ iye akutero.
‘Tenga kalata wako nulembere 18,000.’
Kapitawoyo ali ndi kuyenera kwake kwa kuchepetsa ndalama zoperekedwa kwa mbuye wake, popeza kuti akali wolamulira wa zochitachita za ndalama za mbuye wake. Chotero mwa kuchepetsa unyinjiwo, iye akupanga mabwenzi ndi awo omwe angamubwezere ziyanjo pamene ataya ntchito.
Pamene mbuyeyo amva chomwe chachitika, iye asangalatsidwa. M’chenicheni, iye “anatama kapitawo wonyengayo, kuti anachita mwanzeru [yothandiza, NW].” Ndithudi, Yesu akuwonjezera kuti: “Ana a nthaŵi ya pansi pano ali anzeru mumbadwo wawo kuposa ana a kuwunika.”
Tsopano, akumakoka phunziro kaamba ka ophunzira ake, Yesu akulimbikitsa kuti: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.”
Yesu sakuyamikira kapitawoyo kaamba ka kusalungama kwake koma kaamba ka kuwona kwake patali, nzeru yothandiza. Kaŵirikaŵiri “ana a nthaŵi ya pansi pano” amagwiritsira ntchito ndalama zawo mochenjera kapena thayo kupanga mabwenzi ndi awo omwe angawabwezere iwo chiyanjo. Chotero atumiki a Mulungu, “ana a kuwunika,” afunikiranso kugwiritsira ntchito chuma chawo chakuthupi, “chuma [chawo] chosalungama,” m’njira yanzeru kudzipindulira iwo eni.
Koma monga momwe Yesu akunenera, iwo ayenera kupanga mabwenzi mwa kugwiritsira ntchito chuma chimenechi ndi awo omwe angawalandire iwo “m’mahema osatha.” Kwa ziwalo za kagulu ka nkhosa, malo amenewa ali kumwamba; kwa nkhosa zina, ali m’Paradaiso ya pa dziko lapansi. Popeza kuti kokha Yehova Mulungu ndi Mwana wake angalandire anthu m’malo amenewa, tiyenera kukhala anzeru m’kugwiritsira ntchito “chuma chosalungama” chirichonse chomwe tingakhale nacho kuchirikiza zikondwerero za Ufumu ndipo mwakutero kulimirira ubwenzi ndi iwo. Kenaka, pamene chuma chakuthupi chilephera kapena chikutha, monga mmene icho motsimikizirika chidzatero, mtsogolo mwathu mosatha mudzakhala motsimikizirika.
Yesu akupitirizabe kunena kuti anthu okhulupirika ngakhale m’kusamalira kaamba ka zinthu zakuthupi zimenezi, kapena zochepera, adzakhalanso okhulupirika m’kusamalira kaamba ka nkhani za chifuno chokulira. “Chifukwa chake,” iye akupitiriza tero, “ngati simunakhale okhulupirika m’chuma chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma chowona [uko ndiko kuti, zikondwerero, zauzimu, kapena za Ufumu]? Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zake za wina, [zikondwerero za Ufumu zimene Mulungu amaikiza kwa atumiki ake], adzakupatsani inu ndani za inu eni [mphoto ya moyo m’mahema osatha]?”
Ife sitingakhoze kokha kukhala atumiki owona a Mulungu ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo kukhala akapolo ku chuma chosalungama, chuma chakuthupi, monga momwe Yesu akutsirizira kuti: “Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye aŵiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma.” Luka 15:1, 2; 16:1-13.
◆ Ndimotani mmene kapitawo wa m’fanizo la Yesu akupangira mabwenzi ndi awo omwe angamthandize iye pambuyo pake?
◆ Kodi nchiyani chome chiri “chuma chosalungama,” ndipo ndimotani mmene tingapangire mabwenzi mogwiritsira ntchito icho?
◆ Ndani omwe angatilandire ife “m’mahema osatha,” ndipo nchiyani chomwe chiri malo amenewa?