Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 3/15 tsamba 8-9
  • Mwini Chuma ndi Lazaro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwini Chuma ndi Lazaro
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Munthu Wachuma ndi Lazaro
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mmene Zinthu Zinasinthira kwa Munthu Wachuma Komanso kwa Lazaro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Munthu Wolemera mu Hade
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Mwini Chuma ndi Lazaro Akumana ndi Kusintha
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 3/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Mwini Chuma ndi Lazaro

YESU wakhala akulankhula kwa ophunzira ake ponena za kugwiritsira ntchito koyenera kwa chuma chakuthupi, akumalongosola kuti sitingakhale akapolo kwa izi ndipo pa nthaŵi imodzimodziyo kukhala akapolo kwa Mulungu. Afarisi nawonso akumvetsera, ndipo ayamba kunyodola Yesu chifukwa iwo ndi okonda ndalama. Chotero iye akunena kwa iwo kuti: “Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chizika mwa anthu chiri chonyansa pamaso pa Mulungu.”

Nthaŵi yafika kaamba ka magome kutembenuzidwa pa anthu omwe ali olemera m’zinthu za kudziko, mphamvu za ndale zadziko, ndi ulamuliro ndi chisonkhezero za chipembedzo. Iwo ayenera kutsitsidwa pansi, ndipo awo omwe azindikira zosowa zawo zauzimu ayenera kukwezedwa. Yesu akuloza ku kusintha koteroko pamene akupitiriza kunena kwa Afarisi kuti:

“Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane [Mbatizi]; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kuloŵamo. Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang’ono ka chilamulo kagwe nkwapatali.”

Alembi ndi Afarisi ali onyada ponena za kudzinenera kwawo kwa kumamatira ku Chilamulo cha Mose. Kumbukirani kuti pamene Yesu mozizwitsa anapatsa kuwona kwa munthu wina m’Yerusalemu, iwo anadzikuza kuti: “Ife ndife akuphunzira a Mose. Tidziŵa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose.” Koma tsopano Chilamulo cha Mose chakwaniritsa chifuno chake cholinganizidwira cha kutsogoza odzichepetsa kwa Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu. Chotero ndi kuyamba kwa utumiki wa Yohane, mitundu yonse ya anthu, makamaka odzichepetsa ndi osawuka, akudzikakamiza iwo eni kukhala nzika za Ufumu wa Mulungu.

Popeza kuti Chilamulo cha Mose chikukwaniritsidwa tsopano, thayo la kusunga icho likayenera kuchotsedwa. Chilamulo chinalola chisudzulo pa maziko osiyanasiyana, koma Yesu tsopano akunena kuti: “Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.” Ndimotani nanga mmene zilengezo zoterozo ziyenera kukhala zikukwiyitsira Afarisi, makamaka popeza kuti iwo amalola chisudzulo pa maziko ambiri!

Akupitiriza ndi ndemanga zake kwa Afarisi, Yesu akusimba fanizo lomwe likuwonetsa amuna aŵiri amene kaimidwe kawo, kapena malo, zasinthidwa mwadzidzidzi. Kodi mungagamulepo amene amunawa akuimira ndi chimene kusintha kwa mikhalidwe yawo kukutanthauza?

“Ndipo panali munthu mwini chuma,” Yesu akulongosola tero, “amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pa khomo pake wodzala ndi zironda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zironda zake.”

Yesu pano akugwiritsira ntchito mwini chuma kuimira atsogoleri a chipembedzo Achiyuda, kuphatikizapo osati kokha Afarisi ndi alembi komanso Asaduki limodzinso ndi akulu ansembe. Iwo ali olemera m’mathayo ndi mwaŵi wauzimu, ndipo amadzichititsa iwo eni monga mmene mwini chumayo anachitira. Zovala zawo za bafuta zimaimira mkhalidwe wawo woyanjidwa, ndipo nsalu yawo yoyera imaimira kudzilungamitsa kwawo.

Gulu la mwini chuma wonyada limeneli limawona osauka, anthu wamba ndi kunyozeka kotheratu, akumawatcha iwo ‛am ha·’aʹrets kapena anthu a dziko lapansi. Lazaro wopemphapempha chotero akuimira anthu amenewa kwa amene atsogoleri a chipembedzo anawamana kudyetsa koyenerera kwauzimu ndi mwaŵi. Chotero, mofanana ndi Lazaro wodzala ndi zironda, anthu wambawo amanyazitsidwa kukhala odwala mwauzimu ndipo oyenerera kokha kuyanjana ndi agalu. Komabe, awo a gulu la Lazaro akumva njala ndi ludzu kaamba ka chakudya chauzimu ndipo chotero ali pa chipata kufunafuna kulandira nyenyeswa zirizonse za chakudya chauzimu zomwe zingagwe kochokera pa gome la mwini chumayo.

Yesu tsopano akupitiriza kulongosola kusintha mu mkhalidwe wa mwini chuma ndi Lazaro. Ndi ati omwe ali masinthidwe amenewa, ndipo nchiyani chimene iwo akuimira? Mafunso amenewa adzalingaliridwa m’kope lotsatira la magazini yathu. Luka 16:14-21; Yohane 9:28, 29; Mateyu 19:3-9; Agalatiya 3:24; Akolose 2:14.

◆ Ndi kuyambika kwa utumiki wa Yohane, ndi kusintha kotani kumene Yesu akusonyeza kuti kukuchitika?

◆ Nchiyani chomwe chikachotsedwa pa imfa ya Yesu, ndipo ndimotani mmene ichi chikayambukirira nkhani ya chisudzulo?

◆ M’fanizo la Yesu, ndani omwe akuimiridwa ndi mwini chuma ndi Lazaro?

◆ Ndi chidziŵitso chotani chimene tikuyembekezera m’kope lotsatira la magazini ino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena