Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pamene Mwana wa Munthu Avumbulidwa
PAMENE Yesu adakali kumpoto (kaya m’Samariya kapena m’Galileya), Afarisi akumufunsa iye ponena za kufika kwa Ufumu. Iwo akukhulupirira kuti uwo udzabwera ndi kuwonekera kwakukulu ndi phwando, koma Yesu akunena kuti: “Ufumu wa Mulungu sukudza ndi mawonekedwe; ndipo sadzanena, Tawonani uwu, kapena uwo! Pakuti, tawonani, Ufumu wa Mulungu uli [pakati panu, NW].”
Mawu a Yesu akuti “pakati panu” nthaŵi zina atembenuzidwa kukhala “mwa inu.” Chotero ena aganiza kuti Yesu anatanthauza kuti Ufumu wa Mulungu umalamulira m’mitima ya atumiki a Mulungu. Koma, mwachiwonekere, Ufumu wa Mulungu suli mkati mwa mitima ya Afarisi osakhulupirira amenewa kwa amene Yesu akulankhula. Komabe, uwo uli pakati pawo, popeza kuti Mfumu yoikidwa ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu, iri pakati pawo.
Chiri mwinamwake pambuyo pa kuchokapo kwa Afarisi pamene Yesu akulankhula mowonjezereka ndi ophunzira ake ponena za kudza kwa Ufumuwo. Iye mwapadera ali ndi kukhalapo kwake kwa mtsogolo m’malingaliro mu mphamvu ya Ufumu pamene akuchenjeza kuti: “Ndipo adzanena ndi inu, Tawonani ilo! tawonani iri! musachoka kapena kuwatsata [Amesiya onyenga amenewa]; pakuti monga mphezi ing’anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niwunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu.” Chotero, mongadi mmene mphezi imawonedwera m’malo okulira, Yesu akusonyeza kuti umboni wa kukhalapo kwake m’mphamvu ya Ufumu udzawonekera bwino lomwe kwa onse ofuna kukuwona iko.
Yesu kenaka akuika kuyerekeza ndi zochitika zakale kusonyeza mmene mikhalidwe ya anthu idzakhalira mkati mwa kukhalapo kwake kwa mtsogolo. Iye akulongosola kuti: “Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa munthu. . . . Monga momwemonso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka m’Sodomu udavumba moto ndi sulfure zochokera kumwamba, ndipo zinawawononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa munthu.”
Yesu sakunena kuti anthu m’tsiku la Nowa ndi la Loti anawonongedwa kokha chifukwa chakuti anatsatira machitachita a chibadwa a kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala, ndi kumanga. Ngakhale Nowa ndi Loti ndi mabanja awo anachita zinthu zimenezi. Koma enawo ankachita zochita za tsiku ndi tsiku zimenezi popanda kupereka chisamaliro chirichonse ku chifuno cha Mulungu, ndipo chinali kaamba ka chifukwa chimenechi kuti iwo anawonongedwa. Kaamba ka chifukwa chofananacho, anthu adzawonongedwa pamene Kristu adzavumbulidwa mkati mwa chisautso chachikulu pa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu.
Akumagogomezera kufunika kwa kuchitapo kanthu mofulumira ku umboni wa kukhalapo kwake kwa mtsogolo m’mphamvu ya Ufumu, Yesu akuwonjezera kuti: “Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ake m’nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m’munda modzimodzi asabwere ku zake za m’mbuyo. Kumbukirani mkazi wa Loti.”
Pamene umboni wa kukhalapo kwa Kristu uwonekera, anthu safunikira kulola kugwirizanitsidwa kwawo ku chuma chakuthupi kuwaletsa iwo kuchitapo kanthu mofulumira. Ali pa ulendo wake wotuluka m’Sodomu, mkazi wa Loti mwachiwonekere anayang’ana kumbuyo mokhumbira kaamba ka zinthu zosiyidwa kumbuyo, ndipo anasanduka mwala wa m’chere.
Akumapitiriza ndi kulongosola kwake kwa mkhalidwe umene ukakhalapo mkati mwa kukhalapo kwake kwa mtsogolo, Yesu akuwuza ophunzira ake kuti: “Usiku womwewo adzakhala aŵiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Padzakhala akazi aŵiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa.”
Kutengedwa kumafanana ndi kuloŵa kwa Nowa ndi banja lake m’chingalawa ndi kutengedwa kwa Loti ndi angelo ndi banja lake kutuluka m’Sodomu. Iko kumatanthauza chipulumutso. Ku mbali ina, kusiyidwa kumatanthauza kuvutika ndi chiwonongeko.
Pa nsongayi, ophunzirawo anafunsa kuti: “Kuti, Ambuye?”
“Pamene pali mtembo, pomweponso [ziwombankhanga, NW] zidzasonkhanidwa,” Yesu akuyankha tero. Awo “otengedwa” kaamba ka chipulumutso ali ngati ziwombankhanga zowona patali m’chakuti zimasonkhana pamodzi pa “mtembo.” Mtembowo umalozera kwa Kristu wowona pa kukhalapo kwake kosawoneka ndi maso m’mphamvu ya Ufumu ndi ku phwando lauzimu limene Yehova akupereka. Luka 17:20-37; Genesis 19:26.
◆ Ndimotani mmene Ufumu unali pakati pa Afarisi?
◆ Ndi m’njira yotani mmene kukhalapo kwa Kristu kuli kofanana ndi mphezi?
◆ Nchifukwa ninji anthu adzawonongedwa mkati mwa kukhalapo kwa Kristu?
◆ Kodi chimatanthauzanji kutengedwa, ndi kusiyidwa?