Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
    Nsanja ya Olonda—2015 | July 15
    • 2. (a) Kodi Akhristu anafunika kutsatira chenjezo liti mu 66 C.E.? (b) Kodi anakwanitsa bwanji kuthawa?

      2 Ndiyeno zili choncho, mukukumbukira mawu a Yesu akuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatsatire bwanji chenjezo la Yesu limeneli? Nanga zingatheke bwanji kutuluka mu Yerusalemu asilikali atazungulira mzindawu?’ Koma kenako mukudabwa kuona kuti asilikali achiromawo akubwerera. Zimenezi zikukwaniritsa mawu a Yesu akuti “masikuwo adzafupikitsidwa.” (Mat. 24:22) Tsopano muli ndi mwayi wotsatira malangizo a Yesu aja. Mofulumira inuyo pamodzi ndi Akhristu anzanu okhulupirika mukuthawira kumapiri kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano.a Kenako mu 70 C.E. gulu lina la asilikali achiroma likufika n’kuwononga Yerusalemu. Koma inu mwapulumuka chifukwa chomvera malangizo a Yesu.

  • “Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
    Nsanja ya Olonda—2015 | July 15
    • NTHAWI YA MAYESERO NDIPONSO CHIWERUZO

      7, 8. (a) Kodi aliyense adzakhala ndi mpata wochita chiyani zipembedzo zonyenga zikadzawonongedwa? (b) Kodi atumiki a Yehova okhulupirika adzasiyana bwanji ndi anthu ena?

      7 Ndiyeno kodi chidzachitike n’chiyani pambuyo poti zipembedzo zonyenga zawonongedwa? Uwu udzakhala mpata woti aliyense asonyeze zimene zili mumtima mwake. Anthu ambiri adzafuna kuti atetezedwe ndi mabungwe a m’dzikoli omwe ali ngati ‘matanthwe a m’mapiri.’ (Chiv. 6:15-17) Koma anthu a Yehova adzathawira kumalo achitetezo ophiphiritsa amene Yehova adzawakonzere. Pamene chisautso chinaimitsidwa mu 66 C.E. sinali nthawi yoti Ayuda onse alowe Chikhristu. Koma inali nthawi yoti Akhristu achite zinthu mogwirizana ndi malangizo amene anapatsidwa. Ndi mmene zidzakhalirenso masiku a chisautso chachikulu akadzafupikitsidwa. Sikuti anthu ambiri adzayamba kutumikira Yehova. Koma udzakhala mpata woti Akhristu asonyeze kuti amakonda Yehova ndiponso woti athandize abale a Khristu.—Mat. 25:34-40.

      8 Sitikudziwa zonse zimene zidzachitike pa nthawiyo koma n’kutheka kuti padzafunika kusiya zinthu zina. Paja Akhristu oyambirira anafunika kusiya chuma chawo komanso kupirira mavuto osiyanasiyana kuti apulumuke. (Maliko 13:15-18) Kodi ifeyo tidzalolera kusiya zinthu zathu kuti tikhale okhulupirika kwa Mulungu? Kodi tidzamvera malangizo alionse amene tidzapatsidwe? Pa nthawiyo, atumiki a Yehova okhulupirika okha adzakhala ngati mneneri Danieli chifukwa adzapitiriza kulambira Yehova zinthu zitafika povuta.—Dan. 6:10, 11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena